Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!
Transcript of Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!
![Page 1: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/1.jpg)
Chichewa version No. 1. July, 2011
Phunzirani izi:
Ndikufuna
Kudziwa! Ndi Nkhono ziti zomwe zimafalitsa
matenda, nanga mungazitetedze bwanji ku matendawa inu pamodzi ndi banja lanu?
•Kufunika kwa Nkhono pa chilengedwe•
Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!
• Nkhono monga chakudya
Monga mwakafukufuku wa Dr. Bajope Baluku
Kabuku Kolembedwa ndi Museums of Malawi mogwirizana ndi The Field Museum, Chicago, USA
![Page 2: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/2.jpg)
Kodi Nkhono nchiyani?
Nkhono ndi kanyama kamoyo
Ndi kanyama kamene kakhala kakupezeka padziko lapansi kwa zaka zochuluka
1
2
1
![Page 3: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/3.jpg)
Zimapezeka m’minda ndi mnkhalango
MALAWI
Nkhono zotchedwa Biophalaria
Nkhono zotchedwa Bulinus
Nkhono zopezeka Pamtunda
NkhonozotchedwaAchatina Chatina
Zazikulu Zazing’ono
Ndi mitundu iti ya Nkhono imene imapezeka kuno ku Malawi ? 2
Nkhono zopezeka m’madzi
![Page 4: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/4.jpg)
Kodi Nkhono nchiyani?Nkhono zimamakhala pamtunda ndi mmadzi momwe
M’minda
Nkhalango
Mtsinje
Pamtunda M’madzi
Nkhono ndichakudya cha nyama zosiyanasiyana, choncho ndizofunika pachilengedwe
3
3
4
![Page 5: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/5.jpg)
Nkhono zina zimafalitsa matenda pakati pathu
Mtundu wa Nkhono
izi umapezek
a ndi
tizirombo tim
ene
timayambisa
matenda a Lik
odzo!
Nkhono zimene zimafalitsa matenda amenewa ndi Nkhono zomwe zimapezeka m’madzi
Nkhono za mtundu wa Biophalaria
Nkhono za mtundu wa Bulinus
4
![Page 6: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/6.jpg)
Chipangizo chimene Akatswiri a sayansi amagwiritsa ntchito, pofuna kuwona tizirombo ting’onoting’ono timene sitingathe kutiona ndi maso
Kachirombo ka Likozdo kamene kakuzidwa kwambiri pogwiritsa ntchito Microscope
Kodi kachirombo ka Likodzo nchiyani?
Ndikachirombo kakang’ono kwambiri kamene kamayambitsa matenda a Likodzo kakalowa mthupi la munthu
Kachiromboka kamakhala mkati mwa Nkhono za m’madzi kwa masiku ochepa
Ndikakang’ono
kwambiri
moti mukhoza kuk
awona
pokhapokha
mutagwiritsa
ntchito chip
angizo
chotchedwa Microsc
ope
Ndikakang’ono kwambiri kuposa nsonga ya zingano!
5
Microscope:
Kachirombo koyambitsa Likodzo
![Page 7: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/7.jpg)
6
Apa tikuwona kachirombo koy-ambitsa Likodzo kakamuna ndi kakakazi. Kachirombo kakakazi kamakhala ndi mazira ambiri. Mazira amenewa amayambitsa Likodzo mthupi mwathu
Kachirombo kamene kamayambitsa Likodzo ndi kakang’ono kwambiri
Tiyeni tiwone za kachirombo koyambitsa Likodzo
Kakamuna
Kakakazi
Mazira
Tsopano tiyeni tiwone njira zimene zingatithandize kupewa kachirombo ka Likodzo kulowa mthupi mwathu—
Kachirombo koyambitsa Likodzo
![Page 8: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/8.jpg)
Nthawi zambiri matendawa amapezeka m’njira yodutsa mikodzo ndi m’matumbo
Kodi Likodzo ndi matenda anji?
Kusekula m’mimba
Kusagayika kwa chakudya m’thupi
7
ZIZINDIKIRO ZA MATENDAWA
Matendawa amawononga ziwalo zoberekera za amuna ngakhale akazi ndipo akhoza kupangitsa munthu kukhala
wosabereka
ZIZINDIKIRO ZA MATENDAWA
Kuchita chimbuzi chosakanikirana ndi
magazi
Kumva ululu pokodzaKukodza mikodzo yosakanikirana
ndi magazi
Ziwalo zogaya chakudya m’thupi
Kutupa kwa mimba ndi chimodzi mwazizindikiro za matendawa
![Page 9: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/9.jpg)
Matumbo ndi njira yodutsa mikodzo mwa munthu uyu muli mazira zikwizikwi a tizirombo
Tsopano tiyeni tiwone zigawo za moyo wa tizirombo toyambitsa Likodzo ndi gawo lomwe Nkhono zimatengapo pofalitsa matendawa
Galo loyamba ndi munthu amene ali ndi mazira m’thupi mwake a tiziromboti
8
1
Mazira
![Page 10: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/10.jpg)
NKHONO IMENE ILI NDI TIWANA TATIZIROMBO TOYAMBITSA LIKODZO
Mazira a tizirombo toyambitsa Likodzo amalowa m’madzi pamene munthu wachitiramo chimbuzi kapena kukodzeramo
Tiana tatizirombo toyambitsa Likodzo timakhala mkati mwa Nkhono
2 34
Mazirawa amasosola kukhala tiwana tatizirombo toyambitsa Likodzo
NKHONO
Mas
abat
a at
atu
mpa
ka a
nayi
56
9 Zigawo za moyo wa kachirombo koyambitsa Likodzo
Mazira alowa m’madzi
Munthu akulowa m’madzi
“Munthu yemwe
akudwala Likodzo”
Tiwana ta tizirombo toyambitsa Likodzo timalowa mthupi mwa munthu kupyolera pa khungu
![Page 11: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/11.jpg)
Choncho mukhoza kulowedwa tizirombo toyambitsa Likodzo pokhapokha ngati mwalowa m’madzi m’mene muli tiziromboti
Malo amene kachirombo koyambitsa Likodzo kalowera
1
2
710
3
![Page 12: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/12.jpg)
Tiyeni tiunikenso zigawo za moyo wa kachirombo koyambitsa Likodzo
Zigawo za moyo wakachirombo koyambitsa Likodzo
Umayamba pamene munthu wodwala matenda a Likodzo wachitira chimbuzi m’madzi kapena kukodzera m’madzi
Munthu yemwe akudwala Likodzo akuchitira chimbuzi mmadzi kapenanso kukodzera mmadzi a m’mitsinje ndi m’nyanja
Mazira akulowa m’madzi
1 2
3
4
5
6
Mazira amasosola kukhala tiwana tomwe timalowa mu Nkhono zimene zimapezeka m’madzi
Pakatha masabata atatu kapena anayi tiwanati timatuluka mu Nkhono ndikulowa m’madzi— m’mitsinje ndi m’nyanja
Zigawo za moyo wakachirombo ka Likodzo kamayambanso ndi munthu amene walowedwa tiziromboti
11
Tiwana takachirombo koyambitsa Likodzo timalowa m’thupi la munthu amene walowa m’mtsinje kapena m’nyanja kupyolera pa khungu
Moyo wa kachiromboka umatheka chifukwa cha zinthu izi: kusowa ukhondo, kupezeka kwa tiziromboti, Nkhono, ndi munthu amene ali ndi tiziromboti mthupi mwake
![Page 13: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/13.jpg)
Kodi tingapewe bwanji matenda a Likodzo? 12
Njira zopewera matendawa:Musasambe kapena kusambira m’madzi amene angoyima kapena akuyenda pang’onopang’ono. Tizirombo toyambitsa Likodzo sitikonda kukhala m’madzi amene akuyenda mothamanga kwambiri
Tipewe kusamba kapena kusambira m’madzi am’misitsinje kapena m’nyanja amene ali munthunzi.
•
•
Choncho onetsesani kuti mukusamba madzi amene ali powala kapena padzuwa m’mtsinje kapena m’nyanja
•
![Page 14: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/14.jpg)
Mungadwale Likodzo pokhapokha ngati thupi lanu lakhuzana ndi madzi omwe muli tizirombo toyambitsa Likodzo, ndipo talowa m’thupi mwanu kupyolera pa khungu
13 Kumbukirani kuti mutha kumwa madzi omwe muli tizirombo toyambitsa Likodzo ndipo. Simungadwale matendawa!
Mukhozanso kuchapa zovala m’madzi momwe muli tizirombo toyambitsa Likodzo— Simungadwale matendawa povala zovala zimene zachapidwa m’madzimo.
Simungadwale Likodzo pomwa madzi amenewa
![Page 15: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/15.jpg)
14
Kukhuzana ndi madzi kwa gawo lina lililonse la thupi lanu kwa mphindi
khumi ndi zisanu
Mphindi khumi ndi zisanu!
Njira yokhayo imene mungatengere tizirombo toyambitsa Likodzo ndi pokhapokha ngati thupi lanu lakhuzana ndi madzi amene muli tiziromboti kwa mphindi khumi ndi zisanu kapena kuposera apo.
KUMBUKIRANI!
![Page 16: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/16.jpg)
Mutha kudya nyama ya Nkhono chifukwa ndiyokoma!
Imu ndimomwe mungakonzere Nkhono kukhala ndiwo—
Kukonza nyama ya Nkhona kukhala ndiwo pa banja lanu ndikosavuta
15
![Page 17: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/17.jpg)
Kumbukirani kuti kudya nyama ya Nkhono yophika simungatenge tizirombo toyambitsa matenda a Likodzo
•
16Nyama ya Nkhono monga nyama ina iliyonse muli chakudya chomanga ndi kukulitsa thupi!!
Tulutsani Nkhono m’chigoba chake poyikoka
Phikani ndipo kazingani nyama ya Nkhono
bwinolomwe ndipo mukhonza kudyera mpunga ngakhale nsima Mukhonza kuwonjedzeranso ndiwo za masamba
•
![Page 18: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/18.jpg)
17
M’zigobamu mumapezeka mchere umene umapangitsa matupi anu kukhala athanzi.
Poyamba phikani zigoba za Nkhono
Kenako phwanyani kapena sinjani zigobazi mpaka zitasandulika ngati ufa umene mungasakanize ndi chakudya chanu
Zigoba za
Nkhono
ndizofunik
anso!
Mukhonzanso kudya zigoba za Nkhono.
![Page 19: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/19.jpg)
18Mukhonzanso kupanga chakudya cha Nkhuku pogwiritsa ntchito Zigoba za Nkhono
Patsirani Nkhuku zanu zigoba za Nkhono zimene mwaziphwanya
Phikani zigoba za Nkhono kwa mphindi makumi atatuZiwumitseni poziyanika padzuwaPhwanyani kapena sinjani zigobazi
mpaka zitakhala ziduswa zing’onozing’onoPatsirani Nkhuku zanu tiziduswati
•
••
•
![Page 20: Zoona Zake Zofotokoza za Nkhono!](https://reader036.fdocument.pub/reader036/viewer/2022082216/589efba61a28ab4a0f8b5e67/html5/thumbnails/20.jpg)
Science Booklet Series No. 1 (Chichewa Version) July, 2011
Tikufuna
Kudziwa!
Phunzirani za zinthu zachilengedwe za ku Malawi
Museums of Malawi
Mukafuna Kudziwa Zambiri Funsani a Museums of Malawi
(Top Mandala Museum kapena
Chichiri Museum, Blantyre)
Science Museum
Wolemba: Dan Brinkmeier ndi Christopher SalemaWojambula Zithuzi: Dan Brinkmeier
Kabuku Kolembedwa ndi Museums of Malawi Mogwirizana ndi The Field Museum, Chicago, USA
This booklet was made possible by a training grant from The Council on Africa, The Field Museum, and with additional generous assistance from Bruce and Mary Feay, Chicago