Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA...

77
Christian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro 1 - Mutha Kusintha Mawu oyamba: Zofooka zathu ndi kusakhwima m’nzeru kwathu, kumatibweretsera kuzunzika kwakukulu. Chifukwa cha zimenezi, timasowa zinthu zambiri zabwino. Timadziwa momwe tiyenera kukhalira ndi kuchitira koma timangolepherabe mu njira zomwezo. Timafuna titathana nako kulephera kwathuko ndi kuyamba kukula mwa Ambuye. Koma kapena mwina tinayamba tayesera, koma timangolepherabe. Ena a ife mwina tataya kale mtima pankhani yofuna kuthana ndi mavuto a khalidwe lathu lofookalo, maonekedwe athu, kapena ubale wathu ndi Mulungu. Mawu a Mulungu amakulimbikitsani ndi kukutsimikizirani kuti mungathe kusintha inu! Mungathe kukula ndi kukulirabe mofanana naye Mulungu ndi kukhala ndi moyo wapumphu wochuruka zedi. Phunziroli likhudza magawo ozama kwambiri ndi mkatikati mwa miyoyo yathu, komanso zofuna kupirira pomvetsera, koma zotsatira zake ndi zopindulitsa koposa. Muphunziroli, tigwiritsa ntchito malemba awa: Yohane 1:12 - "Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu ya kukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake. Mateyu 5:6 - "Odala ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo; chifukwa adzakhuta. Yohane 7:37-39 - "Ngati pali munthu akumva ludzu, adze kwa Ine, namwe. Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kuturuka m’kati mwake. Koma ichi anati za Mzimu amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandira." 2 Corinthians 3:17,18 - "Koma Ambuye ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu. Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m’chithunzi thunzi chomwechi kuchokera kuulemerero kumka kuulemerero, monga ngati kuchokera kwa Ambuye Mzimu.” 1. Ngati Ndalepherapo Kale, nchifukwa chiyani ndigathe kukula nthawi ino? Mungathe chifukwa: A. Mungathe kumvetsa bwino ndi kuzindikira kutanthauza kwa zinthu zambiri tsopano, kusiyana ndi kale. B. Mungathe kukhala ndi zolinga za mphamvu tsopano kusiyana ndi kale. C. Mungathe kulandira malangizo ndi zithandizo zabwino kuchokera kwa ena kusiyana ndi nthawi za kale zija. D. Mungathe kukhala pafupi kwambiri ndi Mulungu koposa kale lija. M’mawu a Mulungu muli nzeru ndi luntha lomwe lingachize ndi kuthana ndi vuto la mtundu uliwonse, kapenanso kufooka kwa mtundu uliwonse, m’moyo wanu wa mzimu. Ngakhale kuti panali nthawi zina zomwe mwakhala mu kusakaza ndi kuononga moyo wanu, kaya kuti kulephera kwanu kwakhala kwa mtundu woipitsitsa chotani, pali njira yochokera pamene inu mwaimapo nthawi ino, kupita kutsogolo kukafika pa ubwino wapumphu, chimwemwe ndi mtendere mwa Ambuye, ngati muli ndi chidwi chofuna kugonjera ndi kukhala pansi pa ufumu wake wa Yesu, monga Ambuye wanu, ndi kuyenda m’njira yomwe iye wapereka ija. 2. Mawu a Mulungu Amalonjeza kuti tingathe kukula, Iwo amanena za: A. Kuleka moyo wakale ndi kuyamba moyo watsopano. 1) Mwa kubadwa mwatsopano - Yohane 3:3-5.

Transcript of Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA...

Page 1: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

1

Kukula m’Moyo mwa Chikhristu

Phunziro 1 - Mutha Kusintha

Mawu oyamba: Zofooka zathu ndi kusakhwima m’nzeru kwathu, kumatibweretsera kuzunzika kwakukulu. Chifukwa

cha zimenezi, timasowa zinthu zambiri zabwino. Timadziwa momwe tiyenera kukhalira ndi kuchitira koma

timangolepherabe mu njira zomwezo. Timafuna titathana nako kulephera kwathuko ndi kuyamba kukula mwa Ambuye.

Koma kapena mwina tinayamba tayesera, koma timangolepherabe. Ena a ife mwina tataya kale mtima pankhani yofuna

kuthana ndi mavuto a khalidwe lathu lofookalo, maonekedwe athu, kapena ubale wathu ndi Mulungu.

Mawu a Mulungu amakulimbikitsani ndi kukutsimikizirani kuti mungathe kusintha inu! Mungathe kukula ndi

kukulirabe mofanana naye Mulungu ndi kukhala ndi moyo wapumphu wochuruka zedi. Phunziroli likhudza magawo

ozama kwambiri ndi mkatikati mwa miyoyo yathu, komanso zofuna kupirira pomvetsera, koma zotsatira zake ndi

zopindulitsa koposa. Muphunziroli, tigwiritsa ntchito malemba awa:

Yohane 1:12 - "Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu ya kukhala ana a

Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake.

Mateyu 5:6 - "Odala ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo; chifukwa adzakhuta.

Yohane 7:37-39 - "Ngati pali munthu akumva ludzu, adze kwa Ine, namwe. Iye wokhulupirira Ine,

monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kuturuka m’kati

mwake. Koma ichi anati za Mzimu amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandira."

2 Corinthians 3:17,18 - "Koma Ambuye ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.

Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole

ulemerero wa Ambuye, tisandulika m’chithunzi thunzi chomwechi kuchokera

kuulemerero kumka kuulemerero, monga ngati kuchokera kwa Ambuye Mzimu.”

1. Ngati Ndalepherapo Kale, nchifukwa chiyani ndigathe kukula nthawi ino? Mungathe chifukwa:

A. Mungathe kumvetsa bwino ndi kuzindikira kutanthauza kwa zinthu zambiri tsopano, kusiyana ndi kale.

B. Mungathe kukhala ndi zolinga za mphamvu tsopano kusiyana ndi kale.

C. Mungathe kulandira malangizo ndi zithandizo zabwino kuchokera kwa ena kusiyana ndi nthawi

za kale zija.

D. Mungathe kukhala pafupi kwambiri ndi Mulungu koposa kale lija.

M’mawu a Mulungu muli nzeru ndi luntha lomwe lingachize ndi kuthana ndi vuto la mtundu uliwonse,

kapenanso kufooka kwa mtundu uliwonse, m’moyo wanu wa mzimu. Ngakhale kuti panali nthawi zina zomwe

mwakhala mu kusakaza ndi kuononga moyo wanu, kaya kuti kulephera kwanu kwakhala kwa mtundu

woipitsitsa chotani, pali njira yochokera pamene inu mwaimapo nthawi ino, kupita kutsogolo kukafika pa

ubwino wapumphu, chimwemwe ndi mtendere mwa Ambuye, ngati muli ndi chidwi chofuna kugonjera ndi

kukhala pansi pa ufumu wake wa Yesu, monga Ambuye wanu, ndi kuyenda m’njira yomwe iye wapereka ija.

2. Mawu a Mulungu Amalonjeza kuti tingathe kukula, Iwo amanena za:

A. Kuleka moyo wakale ndi kuyamba moyo watsopano.

1) Mwa kubadwa mwatsopano - Yohane 3:3-5.

Page 2: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

2

2) Mwa kukhala wolengedwa watsopano - 2 Akorinto 5:17.

3) Mwa “kufa” ku munthu wa machimo, ndi kukhala “amoyo” kwa Mulungu- Aroma 6:1-14.

4) Mwa kuvula munthu wakale, ndi kuvala munthu wina watsopano - Akolose 3:5-14; Aefeso

4:22-32; 5:1-21.

5) Mbiya yoonongeka yomwe woumba uja atha kuumbanso - Yeremiya 18:1-10.

B. Kufananira fananirabe ndi Yesu.

1) Kuyang’anitsitsa Yesu ndi kusinthika pofuna kufanana naye - 2 Akorinto 3:17,18.

2) Chipatso cha Mzimu chibadwa mwa ife - Agalatiya 5:22,23.

3) Chifaniziro cha Mulungu chomwe chinatayika chibwezeretsedwa mu umunthu watsopano -

Akolose 3:10; Aefeso 4:22-24.

4) Kutenga gawo pa umulungu wake - 2 Petro 1:4-7.

5) Tikulamulidwa kuti tikule, choncho ichi chitanthauza kuti tingathe - 2 Petro 3:18.

C. Kuthandizana ndi Kulimbikitsana:

1) Alipo mautumiki operekedwa kuti atithandize kukula ndi kufanana ndi Yesu - Aefeso 4:11-

13.

2) Kuliponso kulimbikitsa kochokera kwa Akhristu anzathu - Ahebri 10:24,25; Aroma 15:1-3.

3) Kuthetsa chizolowezi cha thupi ndi zofooka zake - Aroma 7 and 8.

4) Malamulo a Mulungu olembedwa pa mitima yathu (kumvera kuchokera pansi pamitima) -

Yeremiya 31:31-34.

5) Kupumula ku zolemetsa ndi zothodwetsa zathu - Mateyu 11:28-30.

6) Kumasulidwa ku ukapolo wa machimo - Luka 4:18,19.

7) Kuthana ndi machimo mothandizidwa ndi Mzimu Woyera - Aroma 8:13.

8) Moyo wochuluka - Yohane 10:10.

9) Mulungu amene anayamba ntchito yabwinoyi mwa ife, adzaitsiriza yekha - Afilipi 1:6.

3. Ziphunzitso Zina Zothandiza Posintha mwa Uzimu ndi Kukula mwa Uzimu:

A. Kukula mu uzimu kumayamba pang’ono pang’ono, sichinthu cha lero ndi lero ayi – Marko 4:26-29; 2

Akorinto 3:17,18.

B. Mayesero amabweretsa chipiriro, kulimba ndinso kukhwima - Yakobo 1:2,3; Aroma 5:3,4; ndiponso

amatiyeretsa nachotsa zoipa nakhazikitsa zabwino - Yohane 15:1,2; Ahebri 12:5-11; Malaki 3:3.

C. Kasankhidwe kathu kamatibweretsera zizolowezi zina. Zizolowezi zimapanga khalidwe. Choncho

kukula, kumadaliranso kasankhidwe koyenera kwa zinthu zowoneka ngati zazing’ono pa moyo

Page 3: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

3

wathu watsiku ndi tsiku kusintha kumayamba pomwepo.

D. Sinthani maganizo anu ndipo mudzasinthanso machitidwe anu - Miyambo 4:23; Afilipi 4:8.

Komanso kusinthika mu machitidwe kudzasinthanso momwe mtima wanu umamvera.

E. Pamene mukula ndi pamenenso mungathe kukulirabe. Ngati simulabadira kukula kwanu mu uzimu,

kukhalanso kovuta kuti inu mukule - Mark 4:24,25. Mutha kubwereranso ku moyo wanu wa uzimu

woona ngakhale munatayika ndi kulowerera kodetsa nkhawa. Koma ngati munthu aumitsa mtima

wake nazolowera tchimo ngati chosewera nacho chabe ndi kutayirira, ndi pamenenso kumakhala

kovuta kwambiri kuti abwerere ndi kulapanso. Choncho mukuona kufunikira kwake kosankha nthawi

yomwe ino. poyamba kutsata njira zoyenerera zotithandiza kuchotsa kalikonse komwe

kangatichedwetse kuyamba kukula m’moyo wa Chikhristu - Luka 15:17-19; Ahebri 12:1.

F. Kukhulupirka m’zinthu zazing’ono, kumapherezera mu kukhulupirika m’zinthu zazikulu - Luka

16:10-12; 19:17.

G. Kumzimu, iripo yoyesera, kapena kupirira, kudziwa vuto lenileni ndi kuchizira monga momwe

zimakhalira ku thupi. Munthu aliyense ayenera adziyese yekha m’moyo wake wa iye yekha, ndipo

mwa pemphero angafune kukambirana za mavuto ake a uzimu ndi oyang’anira mpingo, aphunzitsi

kapena aliyense yemwe ndi Mkhristu wodalilika, wokhulupirika ndi wokhwima - 2 Akorinto 13:5;

Ahebri 4:12; Masalimo 139:23,24; Yakobo 5:16; Marko 10:17-21.

4. Zinthu Zina Zoyenera Kukhala Nazo kuti Mukule Bwino.

A. Kubadwa. Kodi “munabadwadi kachiwiri” moona, “mwa madzi ndi Mzimu Woyera?”

Kodi mumayanjanadi ndi Mulungu yemwe ali moyo? Yohane 3:3-5; Machitidwe 2:38;

1 Yohane 1:7,9.

B. Kukhala mozunguliridwa ndi zinthu ndi anthu abwino zothandiza pa kukula – Ahebri 10:24-25; 1

Akorinto 15:33.

C. Chakudya ndi chakumwa chabwino - Ahebri 5:11-14; 6:1-3; Chibvumbulutso 22:17; Yohane 6:35;

Afilipi 4:8; Masalmo 119:97,103.

D. Moyo wa ukhondo - Marko 7:20-23; 2 Akorinto 6:14-7:1; 2 Timoteo 2:20-22.

E. Kugwiragwira ndi kuyesayesa kuti mukhale olimba - Ahebri 5:14; Mateyu 7:24-27.

5. Zinthu Zolimbana ndi Kuchedwetsa Kukula mu Chikhristu.

A. "Zilakolako zathupi, za maso, kunyadira za thupi kapena moyo wa dziko” - 1 Yohane 2:15-17;

Agalatiya 5:17; Yakobo 4:4-10; Aroma 8:5-8.

B. Mitima youma, kusadzipereka kotheratu, kutanganidwa ndi zokoma zadziko - Luke 8:4-15.

6. Makhalidwe ndi Zochita za Munthu Wokhwima m’Chikhristu.

A. Kusamalira zamkati koposa zooneka kunja; pochita ndi mtima wonse osakhala kungochita

“mwachinyenga mphunzitsi” kuti andione - Luka 17:20; 1 Samueli 16:7; Luka 11:37-42.

B. Mtima wofuna kupulumutsa ena, wofuna kutumikira, woganizira ena, osadziganizira ndi kudzifunira

zabwino inu nokha - Afilipi 2:5-11; Aroma 15:1-3.

Page 4: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

4

C. Wotha kupereka zinthu zina ndi maufulu ena ndi cholinga chofuna kupeza zinthu zina zabwino

koposa. Wosafuna kuti ziri zonse zabwino zikubwera zikhale zake.

D. Wotha kubvomereza kulakwitsa kwake kuti zinthu zionongeke – osati wongotchula ena kuti ndiwo

amulakwitsa, kapena zinthu zina, kuti ndizo zamulakwitsa, kapena chilichonse.

E. Wotha kulolera kutumikira pa nthawi yovuta ndi yoopsa, ndi cholinga chofuna kuchita bwino pa

uzimu - Luke 19:11-26.

F. Wokhoza kutsata cholinga chenicheni cha ziphunzitso za Mulungu, osati kungosamala maonekedwe

chabe.

G. Wotha kulamula ndi kugonjetsa zomvedwa mu mtima m’malo molamulidwa iyeyo; wotha kusankha

kuchita zinthu zovuta kuchita, zoti iye sanali wokonzeka kuchita.

7. Zoyenera Kuyang’anitsitsidwa mu Phunziroli:

A. Kukonza zolakwa zanu zonse zakale, ndi kukonzanso ubale womwe unaonongeka m’mbuyomo.

B. Kuchotsa zokayikitsa zonse zomwe zimafooketsa chikhulupiriro chanu, ndi kukulepheretsani kugwira

ntchito ya Ambuye.

C. Kuthana nawo ukapolo wa zilakolako za thupi, zokondweretsa za dziko, malingaliro oyipa ndi zina

zotere.

D. Kupachika pa mtanda munthu wakale, kuti muchepetse moyo wolimbana ndi anzanu, ndipo potero

mutha ndithu kumvera Mulungu.

E. Kuphunzira kudzisunga nokha ndi kudzilamulira nokha, kuti muthe kuthetsa zilakolako zanu

zokupangitsani kukhala osabala kanthu mwa uzimu.

F. Kuphunzira kulamulira ndi kuwongolera zofuna zanu m’malo molamulidwa ndi zofunazo.

G. Kuphunzira kukhala wodzisungira ulemu ndi kudzikhulupirira nokha, kotero kuti tikhale wokonda ndi

kugwira ntchito bwino ndi anzathu.

H. Kukhala wopanga chisankho cholondola, wamaganizo achindunji kuti tikhale wodziwa zolinga ndi

zofunika kuzichita.

I. Kuzindikira zofunikira zenizeni kuti tisanyengeke ndi kutaya miyoyo yathu motsata zinthu zachabe..

J. Kuika zokhudzana ndi ufumu koyambirira kotero kuti zofunikira kwambiri zichitidwe ndi

kukwaniritsidwa.

K. Kusunga ubale wabwino ndi wobvomerezeka ndi anthu onse, kuthetsa moyo wolimbana ndi ena.

L. Kusankha mnzanu wokwatirana naye, woyenera ndi wabwino (nkhani iyi ndi nkhani yaikuru kwambiri

pa moyo wa munthu).

M. Kutsatira utsogoleri ndi ulamuliro wa Mulungu; momwe mungatsimikizire chifuniro ndi cholinga

chake nchotani.

N. Kumangiririka pa maziko a chiphunzitso cha choonadi, ndi kuzindikira choyenera kukhulupirira.

Potsiriza: Ngakhale tiri ndi malire kapena pothera pake pa mphamvu ya kaganizidwe kathu chifukwa cha chibadwa

chathu ndi malo omwe takulira, dziwani kuti tiri nazonso mphatso. Mpata waukulu ulipo woti titha kukula ndithu.

Page 5: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

5

Ndipo aliyense wosankha bwino angathe kukula, kukhala wolimba, wokhwima, wa chimwemwe, wa moyo wochuruka,

koposa china chirichonse chomwe angachiganizire. Moyo wathu utha kukhala wabwino koposa!

Phunziro 2 - Kukonza za Mbuyo

Mawu oyamba: Tonse tinalakwapo, tinalakwitsa, ndi kukhumudwitsa ena m’zaka za m’mbuyomo. Mkhristu aliyense

ayenera kukhala ndi mtima wofuna kukonza zolakwa zake zakale, monga momwe angathere, ndi cholinga choti asakhale

wovutika ndi chikumbu mtima chake, koma akhale ndi ufulu mumtima, kutinso ubale ndi chiyanjano chake ndi Mulungu

chikhale chotseguka kotero kuti athe kuphunzitsa anzake mopanda kudzitsutsa – Machitidwe 24:16; 2 Akorinto 1:12; 1

Timoteo 1:18-19; 1 Petro 3:16; Masalmo 32:1,3,4. Gawo limodzi lofunikira poyambirira pamene Mkhristu akukula

m’moyo wake watsopano, ndilo lokonza ndi kuchotsa zonse zomwe tinaononga chifukwa cha moyo wa machimo

m’mbuyomo. Mu Phunziroli tikhala tikuunikira mitundu itatu ya zoononga zobwera ndi machimo zakale zomwe

ziyenera kuchotsedwa ndi kuiwalidwa.

1. Machimo Omangosanjikizana:

A. Machimo omwe saululidwa ndipo sakhululukidwa, amalekanitsa ndi kulepheretsa munthu kulandira

chisomo cha Mulungu m’moyo wake - Yesaya 59:1-2.

B. Machimo omwe sanamasulidwe amasautsa munthu, amaswa mtendere wake ndipo atha

kumupangitsa kukhala wodwala m’maganizo ndi m’thupi - Masalmo 51:3; 32:3-5.

C. Njira zosathandiza pothetsa machimo:

1) Kuiwala dala, kuyesera kubisa ndi kuthawa mozemba.

2) Kutchula zifukwa zina kapena anthu ena powakanira kuti ndiwo ndi amene akuchimwitsani -

Genesis 3:11-13; Eksodo 32:19-24.

3) Kubisa kapena kukana machimo athu - 1 Yohane 1:8; Ahebri 4:13; Miyambo 28:13.

D. Pali njira imodzi yokha yomwe ndi yokhoza kuchita nayo pothana ndi tchimo lathu, njirayi ndi njira

yomwe Mulungu mwini anapereka.

1) Aoneni machimo anu monga machimodi ndi kuwaulula moona - Machitidwe 3:19; 26:20.

2) Vomerezani machimo anu - Yakobo 5:16; 1 Yohane 1:9; Masalmo 32:5; Miyambo 28:13.

(Vomerani machimo anu pamaso pa iwo omwe adziwa tchimo lanulo, pewani zina zousa

mitima ya anthu.)

3) Funafunani ndipo mupeze, ndipo muvomereze chikhululukiro cha Mulungu (ndi ena omwe

ziwakhudza.)

a. Munthu yemwe anali wakunja ayenera akhulupirire Yesu Khristu monga Ambuye ndi

Mpulumutsi, alape machimo ake, avomereze chikhulupiriro chake mwa Khristu

nabatizidwe - Marko 16:16; Machitidwe 16:30,31; 2:38; 22:16. (Mulungu adapatsa

mwana wake obadwa yekha monga nsembe yotichotsera ife machimo athu.) - Tito

2:13,14; Yesaya 53:4-6; Yohane 3:16; 1 Yohane 1:7).

b. Mkhristu ayenera kulapa, navomereza machimo ake, ndi kupemphera chikhululukiro cha

machimowo. - 1 Yohane 1:9; Machitidwe 8:22.

c Ngati tipitirirabe kudzitsutsa pamene mawu a Mulungu atitsimikizira za chikhululukiro,

izi ziwonetsa kuti:

Page 6: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

6

� sitikhulupirira kapena kudalira Mulungu mokwanira, kapena,

� tikudziwa kuti sitinalape kwenikweni ndi koona, kapena,

� sitinakhululukirebe ena, kapena,

� pali phindu lomwe tikupeza ndi tchimo lomwe tikulisungalo, kapena,

� tikufuna wina woti achite kutithandiza chifukwa tasokonezeka mutu.

4) Tayesani kukhazikitsa dongosolo lobwezera kwa onse omwe munawalakwira ndi kuyanjana

nawo - Levitiko 6:4,5; Ezekieli 33:15; Luka 19:8.

5) Iwalani zakale ndipo ikani mumtima mwanu moyo wadzala ndi chiyero m’malo mwa moyo

wokonda zonyansa wakale. - Luka 9:62; Afilipi 3:13,14; Machitidwe 19:17-20; Mateyu

12:43-45.

6) Ngati Mulungu akukhululukirani, ndiye kuti mwakhululukidwadi! - Aroma 4:7,8; 8:1;

Yesaya 1:18; Masalmo 103:12; Yesaya 38:17; Mika 7:19; Ahebri 8:12 (Mulungu

amakondwera ndi kukhululuka).

7) Mtendere wodabwitsa ndi wopambana umabwera pamene taulula machimo athu kwa Khristu

kuti achite nawo machimowo - Masalmo 32:1,2; Luka 15:17-23.

2. Umboni Wathu Woonongeka.

A. Khalidwe lathu lonyenga limapangitsa kuti ena anyoze Mulungu ndi mawu ake - Aroma 2:21-24; 1

Timoteo 6:1; Tito 2:4,5.

B. Ndi chinthu choopsa kwambiri kupangitsa kuti anthu apunthwe kapena kuwatchinjiriza kuchita

bwino pa uzimu. Chikondicho chidzayesera kuchotsa ndi kukwirira zoipa za mtundu wina uliwonse

ndi zoyambitsa zake zomwe - Mateyu 18:6-10.

C. Pamene mwasinthika m’moyo wanu, chotsalira ndi choti muyesetse kufunafuna chikhululukiro cha

anthu omwe munawalakwitsa m’mbuyomo, ndipo muwadziwitse zakusinthika kwanu, ndi cholinga

chofuna kuyesetsa kuthetseratu umboni woyipa wa masiku anu akalewo.

1) Mukapanda kutero, nanga ngati muli mtumiki wa Khristu, ndipo mwadzidzidzi mukomana

ndi munthu yemwe ali ndi umboni wa moyo wonse woipa womwe munali nawo kale, mutani

naye bwanji?

2) Onetsetsani kuti mwalipira ngongole zanu zonse (ngati simungathe kutero pakali pano

konzani dongosolo lokwana ndi wangongoleyo kuti muone chomwe mungachite

mogwirizana).

3) Mwapadera, yesetsani kukumbukira anthu omwe anali pafupi ndi inu nthawi zambiri omwe

mwina munawakhumudwitsa ndi machimo anu.

a Makolo, mkazi kapena mwamuna wanu, ndi ena apabanja panu.

b Abale ena.

c. Mabwana athu, aphunzitsi athu.

d. Abwenzi, ophunzira anzanu.

e Ndi ena.

Page 7: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

7

4) Khalani okonzeka chifukwa ena atha kukukanani. Pamene inu mwachita gawo lanu lomwe

mungathe, simulinso omangidwa - Aroma 12:18. Tadzingopempherani kuti anthuwo

akhale otheka m’tsogolo.

5) Ngati mwalephera kukomana nawo omwe munawalakwirawo (chifukwa cha imfa kapena

kusamuka), mungopereka nkhani yenseyo m’manja mwa Mulungu, ndipo mumpemphe kuti

akuthandizani kuti muthe kuonana nawo omwe mukuwafunawo (omwe ali ndi moyowo),

ngati kuli kufuna kwake kwa Mulungu.

6) Machenjezo:

a. Mulungu amangoyembekezera zokhazo zomwe ziri zanzeru pamene mukukonza za

umboni wanu. Chitani zomwe muyenera kuchita koma chonde nkhani yokonza zolakwa

zanu za m’buyozi musangoganizira zokhazi ndi kuzitsata koposa muyeso wa nzeru.

Makonzedwewa asakulepheretsani kutumikira Mulungu wanu mu njira zina.

b. Pamene mukuvomereza ndi kusiya zolakwa zanu zakale, musatchule ena omwe

munkachita nawo zimenezi mothandizana. Chifukwa kuvomereza zoipa ndi udindo wa

aliyense pa yekha.

c. Muyenera kusamalitsa pamene mukukonza zolakwa zanu zakale makamaka poonetsetsa

kuti musakambe za zoipa zomwe munachita naye pamodzi pa nthawi yolakwika ngati

zokamba zanu zikhoza kusokoneza moyo wa munthu, (chitsanzo yemwe munachita naye

chigololo kale, koma tsopano ali m’banja labwino). Chonde musagwe mu tchimo

lalikuru pofuna kukonza tchimo lina lakale.

d. Kambiranani pamaso osati pa thenifolo. Yesetsani ngati nkotheka kupewa kulemba pa

kalata.

e. Ngati mutachimwanso, pemphani chikhululukironso.

f. Musachedwetse nthawi yanu yokomana ndi anthu omwe ali ofunika kuti muonana nawo.

g. Poyambirira penipeni konzani zolakwa zazikulu ndi zowopsa, chifukwa chisoni ndi

manyazi zochokera pa zimenezi zimakuza m’maganizo anu nkhani zina zazing’ono

zosayenera kukambidwa.

3. Kuonongeka Kwa Ubale (phunziro lina lidzakhalapo mtsogolo muno).

A. Ngati sitiri pa ubale wabwino ndi anthu ena, (monga momwe tingathere), sitingathe kukhala pa ubale

wabwino ndi Mulungu - Mateyu 5:23,24; Marko 11:25; Ahebri 12:14; Aroma 12:18.

B. Mulungu sadzakhululukira machimo athu ngati ife sitikhululukira anthu ena - Mateyu 6:12,14,15;

18:21-35.

C. Tiyenera kupita kwa omwe anatikhumudwitsa, ndinso kwa iwo amene tinawakhumudwitsa - Mateyu

18:15-17; 5:23,24.

D. Cholingatu sichofuna kupeza “yemwe anayambitsa” ayi, koma kufunafuna mtendere - Mateyu 5:9;

Aroma 12:18.

E. Limbikirani pa gawo lanu la kuonongeka kwa ubwenzi wanuwo, osati za mnzanuyo ayi, koma muone

mbali yanu - Mateyu 7:1-5. Dzichotsereni nokha m’moyo wanu chilichonse chokhumudwitsa -

Page 8: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

8

Mateyu 18:7-9.

F. Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa - Aroma 12:17-21.

G. Mwapadera, onani ubale wanu wakale makamaka iwo omwe munali nawo pafupi nthawi zambiri

m’moyo wanu, monga:

1) Makolo anu, munawakhumudwitsa bwanji?

2) Achimwene anu ndi alongo anu m’banja lanu.

3) Mwamuna kapena mkazi wanu ndi ana.

4) Abwenzi anu akale, kapena amuna kapena akazi anu akale.

a. Ngakhale nthawi zina nkosatheka kubwezeretsa ukwati, nkofunika pa moyo wanu

wabwino wa uzimu kuti muchotse zowawa zonse ndi kuti pakhale bata ndi mtendere

pakati pa inu ndi mzanu wakale..

b. Mulungu samakhala ndi chiyembekezo choti munthu angabwerere kwa mkazi

kapena mwamuna wosakhulupirika amene sakuonetsera poyera mtima wolapadi.

c. Kukhululukira ndi ganizo kapena chisankho cha chifuniro cha munthu mwini, osati

zongomverera m’thupi la munthu ayi. Zilakolako zongomverera m’thupi la munthu

sizingathe kulamulidwa kapena kuwongoleledwa.

Potsiriza: Ngakhale kuti zolakwa zambiri sizingathe kukonzedwanso, ndipo machimo athu onse ayenera kusiyidwa mu

chisomo cha Mulungu, munthu wokhala ndi chikondi, nthawi zonse amamva chisoni pamene akhumudwitsa ndipo

amafunitsitsa kuchotsa chokhumudwitsacho monga momwe angathere. Iri ndi gawo la kulapa. Pamene munthu achita

chomwe angathe mwanzeru kukonza zolakwa zake zakale, ndiye kuti wadziyikira yekha maziko amphamvu

omuthandiza kuti akule ndi kutumikira Mulungu m’moyo wake wamtsogolo!

Phunziro 3 - Kukonza Zokayika Kayika

Mawu oyamba: popeza moyo wa Chikhristu ndi moyo womwe timakhala mwa chikhulupiriro, kukayika

kumatifowoketsa ndi kutilefula kotheratu. Kukayika kumaopseza chipulumutso chathu, chifukwa timatchulidwa oyera

ndi chikhulupiriro chathu – Aroma 1:17; 3:21,22. Kukayika kumasokoneza ife chifukwa timasankha pakati pa zabwino

ndi zoipa ndi chikhulupiro – Aroma 14:23. Kukayika kumaononga mtendere ndi chimwemwe chathu, chifukwa zinthu

zimenezi zimabwera kudzera mu kukhulupirira Mulungu. Kukayika kumatitchinjiriza kuti mapemphero athu asamveke

kwa Mulungu – Yakobo 1:6-8; Mateyu 9:29.

Kukayika sikuti kusakhulupirira. Sichisankho chokhazikika ayi, koma ndi makhalidwe osatisimikizira kapena pakati pa

kukhulupirira ndi kusakhulupirira – 1 Mafumu 18:21. Zitanthauza kukhala wogawika pakati pa maganizo awiri mwa

munthu mmodzi – Yakobo 1:6-8; 4:4-8. Ngati sitikonza titha kupherezera mu kukhala osakhulupirira.

Chikhulupiriro sichimodzi modzi pa kuona kapena kudziwa kwambiri, choncho chikhulupiriro nthawi zonse chiyenera

kuyembekezereka kukhala nako kukayika – Ahebri 11:1; 2 Akorinto 5:7. Komabe chikhulupiriro sichitanthauza

kuyenda molumpha mumdima ayi. Ndi ganizo, ndi chisankho chotsatira njira yomwe munthu wasankha ndi

kuikhulupirira popeza ikugwirizana ndi maumboni omwe tiri nawo. Aliyense, kuphatikizapo wakunja, amakhala nacho

chikhulupiriro. Chikhulupiriro chiri ngati maziko a moyo wa aliyense.

Ngakhale atumiki opambana a Mulungu nawo anakhalapo nazo nthawi zokayikakayika – Mateyu 11:1-3; Luka 1:18-

20; Oweruza 6:36-40; Mateyu 14:28-31; 1 Mafumu 19:3-4; Machitidwe 18:9-10. Choncho monga taonera mu

zitsanzo zimenezi, Mulungu ndi woupeza mtima, wodekha ndi wothandiza ana ake pamene asautsidwa ndi vuto

lokayika (Yesu anagwirabe ntchito pamodzi ndi ophunzira ake okayikakayika) – fanizirani ndi Masalmo 103:13-14.

Page 9: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

9

Mulungu atha kugwiritsa ntchito kukayikira kwathu ngati chida chotiphunzitsira ife phunziro labwino, ngati tikhala

wolimbana ndi vuto lokayika kwa nthawi yaitali. Ichi chitha kutithandiza kukhala ndi chidwi, njala, ndi khumbo lofuna

kukhala ndi Mulungu pafupi. Muyezo woyenerera wa kukayikira nthawi zina umatithandiza kuchotsa moyo

womangolandira chilichonse popanda kuchiyesa mwa malembo.

Pa moyo wathu uno sititsimikiza choonadi chake cha zinthu zonse. Kumvetsa kwathu kuli nawo muyeso ndi malire ake,

ndiponso chikhulupiriro chathu chimakhala chikukulabe – Marko 9:23-24. Ngati Akhristu alekana maganizo pa momwe

amvera ndi kutanthauzira ziphunzitso ndi zikhulupiriro zina zazing’ono, ayenera kuphunzira kugwirira ntchito

pamodzibe basi – Aroma 14. Koma titha kutsimikiza ndi kukhulupirira za zofunika kwambiri kuti tikhale ndi moyo

wokhazika ndi wa mphamvu. Muphunziroli tikuona mitundu yosiyana siyana ya makayikidwe omwe amasautsa

Akhristu. Tidzaona ena a magwero ake ndi chiyambi chake cha makayikidwewo, ndinso momwe tingawagonjetsere

pothandizidwa ndi Mulungu.

1. Kukayika Kwina ndi Kwina Komwe Kumasautsa Akhristu Ambiri:

A. Kukayikira za Chikhristu ndi Uthenga Wabwino monga:

1) Kodi Mulungu alipodi?

2) Mphamvu ya umulungu, kuuka kwa akufa ndi Umbuye wa Khristu.

3) Kodi Baibulo ali mawu a Mulungu ouziridwa ndi Mzimu Woyera, kapena mawu a anthu chabe?

B. Kukayikira za chifuniro cha Mulungu, za chabwino ndi choyipa mu nthawi zosiyanasiyana:

1) Kodi Mkhristu akuloledwa kukhala msirikali wankhondo?

1) Kodi malembo akundipatsa ufulu wokwatiranso kawiri?

2) Kodi ndikalowe ntchito kwina? Kapena ndipitirizebe yomweyo?

C. Kukayikira za chipulumutso changa ndi chitetezo changa cha muyaya monga:

1) Kodi ndiri ndi tchimo losakhululukidwa nalo?

2) Kodi kutembenuka kwanga kunali koonadi ndi kwa chilungamo?

3) Ndingadziwe bwanji ngati malowedwe a Chikhristu anga analidi ochokera kwa Mulungu?

4) Kodi ndalandiridwadi ndi kukhululukidwa ndi Mulungu?

5) Kodi ziphunzitso zomwe ndikutsatira ndi zoona, kapena zabodza?

1. Magwero Kapena Zoyambitsa Zina za Zokayikitsa. (Malingana ndi mndandanda wosanjidwa ndi O.S.

Guinness m’bukhu lake lotchedwa “In Two Minds,” lotsindikizidwa ndi Inter Varsity Press, m’chaka cha 1976,

Mitu “A” mpakana “F”, achokera kwa Guinness).

A. Kusayamika, kuiwala kuti, kodi tinapulumutsidwa ndi chiyani, kuiwala kufunikira kwa Mulungu ndi

kudzimasula kuchoka m’manja ndi ulamuliro wa Mulungu – Aroma 1:21; Masalmo 106:7,13. Njira

yokonzera: Bwererani ku moyo woyamika ndi kudziwa kuti muli wosowa – Luka 15:11-32; Chibvumbulutso

2:4-5.

B. Kusamdziwa bwino Mulungu. Timalephera kumkhulupirira Mulungu chifukwa sitimamdziwa Iye monga

momwe alili.

1) Kumdziwa kwenikweni ndiko kumkonda ndi kumkhulupirira.

Page 10: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

10

2) Momwe tikhalira pamodzi ndi abale, makolo, ndi ena olamulira maudindo osiyana siyana, zimakhudza

momwe timdziwira Mulungu.

3) Momwe anthu amdziko amamtengera Mulungu, zikhozanso kumasokoneza maganizo athu pa kudziwa

Mulungu.

4) Sinkhani za chipembedzo chathu zomwe zimaonetsa momwe timdziwira Mulungu ayi, koma momwe

tichitira mu nthawi yovuta.

5) Kadziwidwe kathu ka Mulungu kamawongoledwa mwa kulandira malembo ndi kupemphera kosaleka,

popempha thandizo la Mzimu Woyera, koma koposa zonse, poyang’ana kwa Yesu – Yohane 14:9.

C. Madziko ndi chiyambi chofooka, kusadziwa za umboni wonena za choonadi cha Chikhristu.

1) Chikhulupiro cha Chikhristu chidasamira ndi kudalira pa umboni wolimba ndi wa mphamvu, ndiponso pa

mbiri yokhala ndi zolinga zotsimikizika zakale kale – Yohane 20:20-21; Luka 1:3-4; Aroma 1:4; 1

Akorinto 15:3-8; Machitidwe 4:18-20; 5:27-33; 21:13.

2) Mkhristu ayenera akhale wokonzeka kukhoza kufotokoza zifukwa zake zomveka za kukhulupirira kwake

- 1 Petro 3:15. Chikhulupiriro chake sichidzachedwa kugwa pamene akomana ndi anthu osutsa

osakhulupira ngati sadziwa zolinga ndi zifukwa zomwe iye amakhulupirira Mulungu (monga momwe

zimakhalira mu sukulu zosapembedza zina).

3) Alipo maphunziro abwino zedi othandiza pa za “Maumboni a Chikhristu” (alembi ndi Josh McDowell,

John Clayton, C.S. Lewis, John R.W. Scott).

4) Anthu a Bereya “amafufuza m’malembo tsiku ndi tsiku” kuti atsimikiza ngati ziphunzitso za Atumwi

zinali zoona - Machitidwe 17:11. Chikhulupiriro nthawi zambiri chimafooka chifukwa chongodalira

kwambiri aphunzitsi popanda kumasanthulako tokha malembo ndi kumatsimikiza ngati Baibulo

likuvomereza.

5) Kumbukirani chikhulupiriro chimabwera ndi kumva kwa mawu a Mulungu – Aroma 10:17.

6) Atumwi anafuna kutsimikizadi zakuuka kwa akufa - Luka 24:11,12,36-42; Yohane 20;19-28.

7) Gawo lina la ubale wathu ndi Mulungu lilipo chifukwa cha zodziwika mu mtima, koma za pa mtima

ziyenera kuweruzidwa and choonadi cha poyera cha Uthenga Wabwino. Za pa mtima zimathandiza

chikhulupiriro chathu, koma simaziko ake ayi.

D. Kusadzipereka kumapangitsa kuti chikhulupiriro chathu chioneka chosalimba.

1) Titha kumadziwa zoonadi zake za Uthenga Wabwino, komanso osadzipereka pogwira ntchito monga

zifunikira - Yakobo 2:14-26.

2) Anthu ena akuopa kudzipereka ndipo amavutika kwambiri pofuna kuti adzipereke ku ntchito ina iliyonse.

Timangofuna kupeza cholowa popanda kugwirira ntchito yake.

3) Wina athe kukhala Mkhristu pongofuna kuchita monga mwa chizolowezi cha anthu ena, kapena kuti

athandizidwe pa zofuna zake zina.

4) Imabwera nthawi imene munthu, mnyamata kapena mtsikana, ayenera kuganizira ngati chikhulupiriro cha

makolo ake chirinso cha iye, ndipo ngati chikhulupirirocho chili chakedi savutika pofuna kudzipereka ku

ntchito ya Mulungu.

5) Chikhristu ndi phangano la pakati pa munthu ndi Mulungu wake lomwe limafuna ndithu kudzipereka.

6) Chikhulupiriro sikungokhulupirira zimene umva ndi kuphunzira, kaya kuona chabe, ayi, koma

chitanthauza ganizo lopanga chisankho chokhala ndi moyo woonetsa ndi womvera chikhulupiriro

Page 11: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

11

chathu – Aroma 1:5; 1 Petro 1:22. Chikhulupiro ndi chinthu chimene titha kuchisankho ndi

kuchiwongolera – Marko 1:15.

7) Tiyenera kulimbikitsa chiphunzitso cha kukhala wophunzira wa Yesu powonjezera pa kutembenuka.

Kudzipereka kwathu kwathunthu ku utumiki mololera kutaya maufulu ena ndi ena chifukwa cha Mulungu

kumapherezera kukulimbika ndi kusakayika kayika – 2 Timoteo 1:12. “Pakuti kumene kuli chuma chako,

komweko udakhala mtima wakonso” – Mateyu 6:21.

E. Kusakula.

1) Chikhulupiro chitha kuoneka ngati chakufa kapena chosalimba chifukwa sitibereka zipatso m’miyoyo

yathu. Palibe chomwe tikuchita.

2) Nthawi zonse pamene tisankha bwino mogwirizana ndi mawu a Mulungu, chikhulupiriro chathu

chimalimbikitsidwa. Nthawi zonse pamene tichita kusaweruzika, chikhulupiriro chathu chimazilara.

Ngati sitimvera ndi kulamulidwa ndi chikhulupiriro chathu, chimatithawa – Luka 16:10.

3) Timatsimikiza za kuitanidwa kwathu ndi kusankhidwa kwathu ndi Mulungu, pokha pamene khalidwe ndi

zochita zathu zakula ndi kufanana ndi Khristu, ndinso pamene timakonda – 2 Petro 1:3-11; 1 Yohane

3:3; 4:17-18; 2:5,29; 3:18-19.

4) Mzimu Woyera ndiye wotsimikizira za chipulumutso chathu, komanso umboni wotsindikizika wa Mzimu

ndi zipatso zake - 1 Yohane 3:24; 4:13; Aefeso 1:13,14; 4:30; Aroma 8:16; Agalatiya 5:22,23.

F. Maganizo Otenga Mtima ndi Zina Zokhudza Umunthu wa Munthu.

1) M’chilengedwa chathu cha uchimo, maganizo otenga mtima amakhala amphamvu otha kulamulira

mphamvu ya momwe timaganizira.

2) Maganizo otenga mtima kawiri kawiri amakhudzidwa ndi zinthu zambiri monga kudwala, momwe thupi

lathu lirili, zakudya, maubale, kulema, ngozi, mavuto osiyanasiyana, zowawa zina, mutu wosokonezeka,

mavuto ndi machimo osaweruzidwa, zotengera ku makolo, maleledwe ndi zina zotere – 1 Mafumu 19:1-

10.

3) Ngati matembenukidwe a munthu ndi ubale wake ndi Mulungu atsamira pa maganizo a kutengeka kwa

mtima koposa kuganiza kozama, nkosavuta kuti munthuyu avutike ndi moyo wokayika kayika chifukwa

cha kusintha kwa maganizo ake akutengeka kwa mtima.

4) Kukayika kubwera chifukwa cha maganizo akutengeka kwa mtima sikungathedwe pa kungoganiza

mozama chabe koma makamaka kungathedwe pozindikira chiyambi kapena gwero leni leni la maganizo

otenga mtimawo – fanizirani ndi 1 Mafumu 19:5,6.

5) Kugwiritsa ntchito chikhulupiriro chathu kawiri kawiri, kumalimbikitsa chikhulupiriro chathu kukhala

chokhazikitsa ndi chosaopsezeka ndi kugwedezedwa ndi maganizo otenga mtima.

6) Maganizo okayika otenga mtima kawiri kawiri amayamba chifukwa chokhala ndi chilakolako chofuna

kusamvera Mulungu ndinso machimo kapena milandu yongokhala mu mtima yosaululidwa.

7) Ngati mufuna kuchita “zofuna zanu” nkosavuta kusakhulupirira.

8) Kutsutsika kumatipangitsa ife kukayikira ngati Mulungu anatilandiradi. Ndipo pokana ndi kuchotsa

zolinga za Mulungu pamodzi ndi mawu ake kuli ngati kukana chiweruzo chake pa ife.

Page 12: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

12

9) Nthawi zina anthu amaopa kukhulupirira, chifukwa iwo ali ovulazika m’maganizo pa zinthu zomwe

akomana nazo, kapena kukhumudwitsidwa ndi zofooka za umunthu wawo, kotero kuti moyo wawo

wonse umayenda poganizira zimenezi basi. Uthenga Wabwino uwoneka ngati wongogupulira – Luka

24:41. Maganizo omwe iwo akhazikikapo akhale monga fano loononga chikhulupiriro chawo. Ali nacho

chilakolako chofuna kukhulupirira, koma sakhoza konse chidwi. Kuchiza mabala ndilo yankho

lenileni. Komanso pamodzi ndi kumudandaulira munthu wotereyo kuti ayesetse kuona ndi kuganizira za

moyo mu njira ndi nzeru zina zosiyana ndi zimene ali nazo panozi.

10) Nchinthu chofunika kuti tidzisiyanitsa pakati pa kukayikira koyenera ndi kwabwino, ndi kukayikira

kopitirira. Maganizo otenga mtima atha kukulitsa zinthu zazing’ono ndi kukhala zazikulu zoti

nkutigwetsa.

11) Pamene maganizo otenga mtima ali ndi mphamvu yotilepheretsa kutenga choonadi ndi cholinga cheni

cheni, nkoyenera kupempha thandizo kwa munthu wina yemwe amatha kudziletsa ku zotengeka tengeka

za m’maganizo, kuti iye athandize pa nthawi imeneyi kufikira pamene umunthu wathu wabwerera ndipo

tikuganiza bwino onga kale.

11) Ngati munthu wakhazikika m’moyo ndi khalidwe lolephera kapena kumangokayika kayika pofuna

kuzindikira nzeru zina, kulephera kubweretsa maganizo omveka pa ntchito ndi m’banja lake, mwina

ayenera kuonana ndi dokotala woti amlangize pavutoli.

G. Kufuna kudziwa zinthu zomwe nthawi yake yoti tizidziwe siyidafike - Yohane 13:7

H. Kulephera kudikira kuti nthawi ya Mulungu ifike.

I. Kudalira ntchito za malamulo, osati chisomo cha Mulungu. Sitimakhala angwiro kokwanira kuti

tilandiridwe ndi Mulungu mwa ife tokha. Tisadalire ntchito zathu zoti tilandiridwe ndi Mulungu chifukwa cha

zimene tinachita - Aroma 3:20. Tiziphunzira kudalira chisomo cha Mulungu mwa Khristu.

3. Zolembera Zoonjezera pa Kuthana ndi Kukayika kayika.

A. Kumbukirani Satana anali wambanda kuyambira pa chiyambi, ndipo sanaima m’choonadi, pakuti mwa iye

mulibe choonadi. Amanama kumapangitsa anthu kukayika kayika - Yohane 8:44; Mateyu 13:24-30, 36-43.

B. Satana amakondwera ndi kukhumudwitsa anthu powachititsa kuti aziganiza kuti achimwe kopitirira koti

ngakhale chisomo cha Mulungu sichingathe kuwapulumutsa – 2 Akorinto 2:5-11.

C. Satana amakonda kulowa m’mitima yathu ndi kutipangitsa kuti tione ngati Mulungu sali woyenera ulemu,

amatipangitsa kuti tilephere kuganiza bwino za Mulungu wathu – Genesis 3:1-5.

D. Kumbukirani kuti Khristu ndi wopambana kuposa Satana ndiponso ndi wamphamvu zoposa posa zedi -

1Yohane 4:4; 3:8,19,20; Aefeso 4:8-10; Akolose 2:15.

E. Mulungu amadziwa kuti ife tiribe nzeru, ndipo wotiyitana kuti tipemphe nzeru – Yakobo 1:5. Ngati munthu

wodzipereka kotheratu kwa Mulungu, wachita chisankho chake moonadi ndi mosamala ndipo wapemphera

kufuna nzeru, ayenera akhazikika mu chikhulupiriro popeza njira yomwe iwoneka yopambana kwa iye,

inakonzedwa ndi Ambuye.

F. Pewani “kukhulupirira mphamvu ya chikhulupiriro chanu.” Mulungu ndi yekhayo woyenera kukhulupiridwa

kotheratu!

Mawu Otsiriza: Njira yopambana yopewera kukayika ndi kumanga zolimba chikhulupiriro chanu, m’malo

mongolimbana ndi zokayika kayikazo. Ngati maganizo anu onse ali pa zokayika kayika, ndiye kuti sali pa Mulungu

amene ali tsinde kapena maziko a chikhulupiriro chanu chachibadwidwe.

Page 13: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

13

Phunziro 4 - Kugonjetsa ndi Kuthana ndi Ukapolo (1)

Mawu oyamba: Pamene tchimo kapena khalidwe la mtundu wina uliwonse loyipa lakhazikika kufikira pa muyezo woti

simungthenso kulisiya, pamene simungathenso kukhala ndi mphamvu zotha kulamula ndi kuwongolera tchimolo, koma

ilo ndilo m’malo mwake lilamulira moyo wanu onse, pamenepo ndiye kuti tsopano mwagwa mu ukapolo uja. Mu bukhu

la Aroma 7:14-15, Paulo akufotokoza za ukapolo wa mtundu umenewu.

Ukapolowu uli m’miyezo miyezo; tchimo mwina litha kumakulamulani pa muyezo wooneka waung’ono kapenanso

muyezo waukulu. Ukapolowutu umamuononga munthu mosiyanasiyana wina umaononga munthu kuposa unzake

molingana ndi mphamvu zake. Ukapolo wongosuta fodya wamba umaononga munthu mocheperako mphamvu

pofanizira ndi ukapolo wotsuta fodya wamkulu (chamba). Mitundu ina ya ukapolo imaoneka ngati “yaulemu ndi

mtendere ndiponso yosakhumudwitsa anthu kuilandira ndi kuivomereza” koposa ina. Kawirikawiri ife sitimatsutsa ndi

kudzudzula munthu wosachedwa kupsa mtima kwambiri monga momwe timachita ndi wachiwerewere (ngakhale kuti

kupsa mtima msanga kumaononganso kwambiri).

Koma mitundu yonse ya ukapolo ndi yowopsa ndipo iyenera kuthedwa ndi kugonjetsedwa, chifukwa:

1. Ukapolo ndi chinthu choti chimangoukira ukirabe mtsogolo chomwe chimadzapheredzera ku kuumitsa mtima

ndi imfa ya ku uzimu – 2 Atesalonika 2:10-12.

2. Pamene tili pansi pa ulamuliro wa uchimo tilibe mtendere, chimwemwe ngakhale kudzisungira ulemu wathu

kumene.

3. Sitirinso omasuka kokwanira koti tingathe kumtumikira Mulungu kowona.

Zitsanzo zina za ukapolo womwe timamangidwa nawo ndi monga: uchidakwa, mankhwala ozunguza bongo, uhule,

chigololo, chiwerewere, kuwerenga ndi kuonera zolaula m’mabuku ndi wailesi ya kanema, kuyang’ana wailesi wa

kenama kosalekeza, kusakaza chuma, mchezo, kupsa mtima msanga, kukwiyakwiya, madyaidya, zoimbaimba, ulesi,

kudera nkhawa, kudzigomera, kudzitcha dolo, kudzipatsa ukatswiri, kukonda ntchito koposa banja ndi Mulungu, ndi

zina zotere.

Mu phunziro lina kutsogoloku, tiphunzira njira zenizeni zotithandiza kupulumuka ku ukapolo wosiyanasiyana womwe

tiutchule. Koma muphunziro loyambali tiona za zoonadi za malembo pa nkhani yaikulu ya ukapolo ndi momwe

tingapulumutsidwire.

1. Uchimo umanyenga nulonjezera ufulu kwa anthu, koma potsiriza umamkoka munthu mu uchimo – 2

Petro 2:19; Genesis 3:1-6; Ahebri 3:13; Yohane 8:44. Onani zitsanzo izi:

Mankhwala ozunguza bongo ndi mowa zimalonjeza zisangalalo zosiyanasiyana kwa wozitenga ndi kugwiritsa

ntchitoyo, komanso kumathandiza kupewa zinthu zina monga manyazi, mantha ndi zina zotere, koma potsiriza

pake zimabweretsa uchidakwa wosatha ndi wokhazikika. Komanso woononga kotheratu mphamvu ya kaganizidwe

ndinso thupi lonse la munthu. M’malo mwake mavuto amangochulukirabe koposa m’malo mothetsedwa.

Chiwerewere ndi uhule pamodzi ndi dama zimalonjeza chikondi ndi chisangalalo, koma zimangotulutsa manyazi,

kuchotsa umunthu wako ndipo sizingabweretse chibale ndi ubwenzi wa nthawi yaitali.

Kutengeka mtima ndi kugula “zinthu zatsopano” kumatha msanga, ndi kumusiya munthu mu ngongole zazikulu,

ndipo zotsatira zake ndi zoti amafuna kugula zinthu zinanso zoti zimuiwalitse ngongoleyo.

A. Uchimo umatikoka kudzera mu zilakolako zathu - Yakobo 1:14; 1 Yohane 2:15,16.

B. Kwa amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake - Yohane

8:34; Aroma 6:16; 7:14-24.

Page 14: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

14

2. Mulungu samafuna kuti ife tikhale kapolo womangiriridwa ku china chilichonse cha thupi – 1 Akorinto 6:12.

3. Yesu amatimvera chisoni ife ndipo akulonjeza kutimasula - Mateyu 9:36; Masalmo 103:13,14; Luka 4:18,19;

Yohane 8:32; 2 Timoteo 1:7; Aroma 8:15; Agalatiya 5:22,23.

4. Atha kupulumuka ku nsinga ya ukapolo wamtundu ulionse – 1 Akorinto 6:9-11.

5. Njira zina zodziwika zomasukira ku ukapolo.

(Palibe njira yosabvuta yothananira ndi ukapolo, komabe chodziwika nchoti njira iripo).

A. Zindikirani ndi kuvomereza chofuna chanu - Luka 15:17-19; 2 Timoteo 2:26.

B. Tembenukani ndi kulapa mtima moonadi - Luka 13:3; Yakobo 4:7-9.

1) Vomerani kuti zachitika chifukwa cha inu eni; musanene kuti zachitika chifukwa cha ena kapena zinthu

zina. Dziwani kuti kusankha ganizo lenileni lotsiriza kuli m’manja mwanu (ukapolotu utha kukhala ngati

matenda mu njira zina, koma ukapolo umadza chifukwa cholakwitsa posankha ganizo lenileni la umunthu

wanu).

2) Iwalani zakale, yeretsani m’nyumba mwanu - Machitidwe 19:18,19.

3) Musapereke mwayi m’pang’ono pomwe womasekerera ndi kusewera ndi zilakolako za uchimo – Aroma

13:14.

C. Pewani anthu, malo ndi zochitika chitika zomwe zimakukokeraninso ku moyo wakale wa uchimo wochotsa

chiyero chanu - 1 Akorinto 15:33; 6:18; 1 Atesalonika 5:22. Sankhani maganizo, anthu, malo ndi

zochitachita zomwe zingakupatseni ufulu wapumphu – Ahebri 10:24-25.

D. Sinthani maganizo - 2 Akorinto 10:4,5; Miyambo 4:23.

1) Phunzirani kudana ndi uchimo - Masalmo 8:13.

2) Phunzirani kukonda chiyero ndi chilungamo - Mateyu 5:6.

3) Phunzirani kuthana ndi kuchotseratu maganizo oyipa pamene angoyamba kumene mu mtima mwanu

asanamere mizu.

E. Khalani ndi maphunziro a Baibulo, okonzedwa mwa dongosolo labwino, okhala ndi makonzedwe okhwima

bwino mwatsatanetsatane nthawi ndi nthawi, tsiku ndi tsiku. Musataye nthawi ndi kuganizira za moyo wakale

wathupi, koma m’malo mwake dyetsani moyo wanu watsopano wa uzimu. Pemphani thandizo la Mzimu

Woyera - Aroma 8:13; Luka 11:13; Aefeso 5:18.

F. Kulani ndi kumdziwa Yesu, ndi kumkonda kuti chidwi chanu chofuna kumkondweretsa chikulirebe kuposa

chidwi chongofuna kudzikondweretsa tokha. Ichitu nchofunikadi – Yohane 12:32; 2 Akorinto 5:14; 1 Yohane

4:19.

G. Bweretsani zolinga zazikulu zatsopano ndi zifukwa zokwanira zotsimikizira moyo wanu watsopano; fufuzani

ndi kutulukira zisangalalo zatsopano ndi zokondweretsa zatsopano zomwe sizititengera ku chionongeko. (Pa

gawo limeneli mpofunika thandizo la ena anzeru).

H. Pempherani ndi kuphunzira bwino kuti muthe kutulukira ndi kumvetsa bwino chomwe chimayambitsa moyo

wa chionongeko womwe umatimanga mu ukapolowu kotero kuti muthe kuzigonjetsa, kuzipewa ndi kuzisiya

ndinso kupitirira mtsogolo, pokhala wangwiro mu uzimu. Ngati simutha kufufuza ndi kutulukira zomwe

zimayambitsa zilakolako zimenezi kapena kutengeka kumeneko, ngakhale mutamenyetsa mutu pansi chotani,

Page 15: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

15

sipangapezeke njira yothawira ndi kugonjetsera zimenezi. Onani izi:

Chilakolako cha uchimo? Kufuna ubale? Kuthawa? Kusowa chochita, kusowa chisangalalo? Kuukira?

Kusowa zina chifukwa cha maganizo otenga mtima? Kusadzidalira? Zoyambitsidwa zina za thupi? Zina

zotere.

I. Dzazani moyo wanu ndi maganizo abwino ndi okoma kuti mupewe kukhala pa mayesero obwerera m’buyo –

2 Petro 2:20-22; Mateyu 12:43-45.

J. Khalani ndi mnzanu yemwe mudzidalirana naye, penanso kuwerengerana naye, lowani mu gulu lomwe

cholinga chake ndi kulimbikitsana ndi kulangizana m’moyo uno - Yakobo 5:16; 1 Atesalonika 5:11.

K. Konzani bwino khalidwe la moyo wanu wa tsiku ndi tsiku ndi kasungidwe ka ukhondo ndi moyo wathupi

lanu, kuti kulimbika kwanu kupitirirebe mtsogolo mosavutirako. (Kusunga mwambo mu dera limodzi

kumathandiza kuti gawo lina lichite bwino.)

L. Konzani bwino moyo wanu wauzimu kwapumphu monga momwe mungathere m’njira iriyonse kuti mulandire

chisomo chokwanira ndi chithandizo chokwanira chochokera kwa Mulungu mu nthawi yanu yolimbana ndi

uchimo: muzipemphera ndi kuwerenga malembo pafupi pafupi, kuchotsa ndi kuiwala zolakwa zonse zakale,

kukonza ndi kubwezeretsa maubale onse amene anaonongeka, chotsani maganizo onse oukira ndi kugalukira

pamodzi ndi kusamvera Mulungu

M. Musayambe ntchito ya chigonjetsoyi nthawi imodzi ayi, koma yambani m’magawo, monga kuyambirira ndi

ukapolo wake womwe uli wovutitsitsa koposa wina uliwonse, kenako wofookerakowo.

Mawu otsiriza: Kutuluka kuchokera mu ukapolo sichinthu chongochitika mwa kanthawi kamodzi kochepa ayi, koma

ndi m’chitidwe womwe umatenga nthawi ndithu. Pophatikizapo kulimbana ndinso kupirira. Komatu kulimbanaku kuli

ndi phindu lalikulu, koma ngati tikhala ndi maganizo olekana ndi amenewa ndiye kuti tingodzibweretsera chionongeko.

Monganso zimatenga nthawi ndithu kuti munthu alowe ndi kukhazikika mu nsinga za ukapolo chimodzimodzinso

kutuluka kudzamtengera nthawi yaitalinso. Ngati munthu amakonda kusankha kumachita chinthu chimodzimodzi

mobwerezabwereza, kenako chimadzakhala chizolowezi kapena khalidwe lake lokhazikika, ndipo potsiliza khalidwelo

limadzapanga moyo wathu wodziwika nawo tsiku ndi tsiku. Ukapolo umabwera ndi kukhazikika kudzera mu

kusasankha bwino kwa zoyenera kuchita zathu ndiponso ufulu; womasuka ku ukapolo umabwera kudzera mu kusankha

mosamala bwino zoyenerera kuchita mobwerezabwereza. Ndipo ngati molimbikira kuyesetsa kuchita bwino, kenako

zimayamba kuoneka monga zosavuta kwambiri mpaka mutafika pomasuka kwambiri monganso poyamba paja.

Phunziro 5 --Kugonjetsa ndi Kuthana ndi Ukapolo (2)

Mawu oyamba: Muphunziro lachinayi lija tinaona za zoonadi zenizeni za malembo pa nkhani ya ukapolo ndipo

tingapulumukere kuchokamo. Koma tsopano tiona mitundu ingapo ya ukapolo ndi njira zinagapo zomwe

zingatithandize ife pothana ndi ukapolo umenewu. Mu phunziro limeneli pokhala ndi lalifupi sititha kuphunzira

mokwanira bwino kwenikweni. Ngati vuto la munthu ndi lalikuru kotero kuti likusautsa umunthu wake, ntchito

yake, ubale wa m’banja mwake, kapena kutumikira kwake kwa Mulungu, ayenera apemphe malangizo kuchokera

kwa mlangizi wobvomerezeka (chenjezo: Onetsetsani kuti mlangiziyo ndi wokhulupirika mu uzimu). Koma mfundo

zotsatirazi zikhoza kukuthandizani kuona pang’ono:

1. Zothandiza Zina Zodziwika:

A. Munthu aliyense yemwe amangidwe ukapolo ndi vuto la zilakolako za zinthu zosiyanasiyana, nthawi

zonse amakhala wosowa chochita, ndinso kusowa mtendere. Munthu aliyense ayenera kukhala

wokhutitsidwa kwa muyeso wakuti, ndinso kudziwa cholinga m’moyo wake, chokondweretsa kapena

kukwaniritsa zokomana nazo, okhala nacho cholinga chokhalira ndi moyo. Munthu wosowa chochita ndi

wosowa mtendere amayetsetsa kuchita chirichonse chofuna kumthandiza kukwaniritsa zosowa zake.

Page 16: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

16

Pamene asankha kudzipezera njira zolakwika monga zomthandiza ku ukapolo wakewo ndi pamene

ukapolo ndi ulamuliro wa zilakolako umakhazikika, ndipo amaonongeka kwambiri koposa kale. Ziripo

njira zina zambiri zomwe Akhristu amasangalalira ndi kukhalira ndi chimwemwe chokwanira mwa

Chikhristu, ndi kumamva kukoma moyo popanda kudziyika mu ukapolo wa zilakolako za dziko. Izi ndi

zomwe amatanthauza Paulo m’malembo opezeka pa Aefeso 5:18-19

B. Pamene tilole chikondi, chimwemwe, mtendere ndi zipatso zina za Mzimu wa Mulungu kukhala

mkhalidwe lathu, yesero lofuna ndi kubvomera zilakolako za chinyengo zomwe zimatimanga nsinga za

ukapolo, limakhala kutali nafe. “Choonadi chidzakumasulani” -Yohane 8:32.

C. Mfundo zambiri zomwe zimagwiritsidwa ntchito pa mtundu umodzi wa ukapolo, zomwezonso zimagwira

ntchito ku mitundu ina.

2. Mitundu yina ya ukapolo yodziwika:

A. Kupsa mtima, kuwawidwa.

1) Momwe zimaonongera uzimu: Kusakhululukirana kumatchinjiriza chisomo cha Mulungu kwa

munthu wopsa mtima ndi wowawidwa - - Mateyu 6:12,14; 18:21-35. Kuwawidwa ndi chinthu

chochitika mopitirira ndipo kungathe kutiononga zedi.

2) Momwe zimaonongera maganizo a pansi pa mtima ndi thupi lonse:. Matenda ambiri amabwera mu

thupi lathu ndinso ku maganizo athu a pansi pa mtima chifukwa chozolowera kuwawidwa mtima ndi

kupsa mtima zambiri.

3) Kuwawidwa kodziwika kwambiri pakati pathu kumaoneka pakati pathu ndi makolo, achimwene ndi

alongo athu, abale athu, amuna kapena akazi athu, ndi abwenzi athu chifukwa cha kupsetsana mtima

kwa kale. Kuwawidwa kumeneku kumagwiritsiridwanso kwa anthu ena omwe poyamba

sizimawakudza.

4.) Munthu amatha kudzisungira yekha likumve la zowawidwa zambirimbiri zakalekale zopanda

kuziona ndi kukonza. Kuwawidwa kumeneko kumayambikanso pamene wina watisusula. Timakhala

ngati watiponda pa chilonda, kapena galu wachiwewe, kaya nkhuku ya pa mazira. Moyo umenewu

umatipangitsa kuti tilephere kupirira pamene zina zatisautsa koposa m’mene tinaliri pa chilengedwe

pathu. Kuthana kwake ndi khalidwe limeneli kuli, kodi munthuyo ayang’anizane maso ndi maso ndi

vutolo, aliziundikire ndi kulilandira, ndipo alichotse ndi kuliyiwaliratu.

5.) Anthu ambiri amawawidwa wawidwa mtima chifukwa cha chizolowezi chomwe chinayambika kale

adakali ana.

6.) Tiyenera kuzindikira kuti tonse timalakalaka ndi kufuna chikhululukiro ndi chifundo, ndipo tiyenera

kuwachitira enanso zimenezi - Aroma 3:23; Marko 11:25. Takhazikikani pa ganizo la momwe

Mulungu anachitira chifundo inuyo.

7.) Munthu wowawidwa wawidwa mu mtima ayenera kusiya kutaya nthawi pomangoganizira za

khalidwe la ena, koma azindikire zomwe chizolowezi chakechi chochita ku mbali yake

kusakondwako. Anthu enanso nthawi zonse sadzatha kuchita wangwiro ndipo sangathe kusiya

kulakwitsa. Gawo lalikulu lothana ndi zimenezi liri m’manja mwathu. Ife eni ake ndi amene tiri ndi

ntchito yonse yokonza zimenezi.

8.) Munthu yemwe wangozolowera kukwiyakwiya amadzipweteka yekha. Akungololera kulamulidwa

ndi kuyendera zochitachita za anthu ena. Adziwe kuti ali nawo wosankha kusachita kapena

kudzilamulira kuti zisamukhudze.

9.) Pamene ndi kulapa tchimo lowawidwa kapena kupsera mtima anthu ena ndi kuyamba kuyeretsa ndi

Page 17: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

17

kulamula mzimu wanga, thandizo la Mzimu wa Mulungu limayamba kulowera, ndi kulowetsa

m’malo mwa kuwawidwako, chipatso chake cha mtendere - Agalatiya 5:22,23; Ahebri 12:5-11.

10.) Phunzirani kuthana ndi mkwiyo pamene ungoyamba kumene, pamene sunafike pokhwima , poti

mutha kulamulira. Musakusungire mumtima ayi, koma chotsani potsatira dongosolo lomwe

Mulungu amatiphunzitsa – Aefeso 4:26-27. Taonani maphunziro otsatira kumunsi.

11.) Zindikirani ndi kulandira ntchito ya “ufulu wanu wachibadwidwe” pamene mukomana ndi vuto

lakupsa mtima. Yesu, mwakufuna kwake yekha analola kuvula ufulu wake wachibadwidwe ndi

kungosamala zoti anthu ena alandire chisamaliro ndi chipulumutso - Afilipi 2:5-11. Pamene “mufa

kuthupi”, simudzathanso kuika kukhoza za momwe anthu ena amachita nafe, chifukwa cholinga

chathu chidzangokhala ndi kutsamira pofuna kuwapulumutsa iwo mwa Yesu basi. Tingathe

kuchizidwa ku matenda akupsaipsa mtima pophunzira “kutaya moyo wathu” kuti tidzaupezenso –

Mateyu 16:24-25.

12.) Kukhululukira ndi ganizo lomwe munthu amasankha, lomwe limaoneka pochitidwa ndithu,

sikungomva m’thupi chabe. Ndi chinthu chimene Mulungu akulamulira. (Simungalamulire

zongomverera m’thupi ayi.)

13.) Gwiritsani ntchito magawo a m’malembo ndi dongosolo lake lomwe pofuna kukonza zolakwa za ena

kwa inuyo.

a. Pitani kwa olakwayo mwa chifatso ndi mtima wodekha ndi kukamuuza vuto lake - Mateyu

18:15; Agalatiya 6:1,2.

b. Mpempherereni ndi kumudalitsa iye - Aroma 12:14; Mateyu 5:44b.

c. Sichabwino kubwezera choipa - Aroma 12:17-21. Lekerani Mulungu kubwezerani.

B. Nkhawa ndi Mantha

1.) Momwe zimaonongera uzimu: izi ndi zosiyana kwambiri ndipo zimasutsana ndi chikhulupiriro –

chomwe chiri chofunika kwambiri pokondweretsa Mulungu - Ahebri 11:6; Afilipi 4:6,7; Luka

18:1; Marko 4:40.

2.) Zimaononga thupi ndi maganizo a pansi pa mtima: mitundu yambiri ya matenda a thupi ndi a

m’maganizo a pansi pa mtima. Mphamvu zathu zimayamwidwa ndi kuonongeka pamene nthawi

yathu yambiri tikhala tikumangodera nkhawa m’mitima yathu. Chizolowezi chomangokhala ndi

mantha chathu kumangopitirira ndipo zitatero titha kuonongeka ku uzimu.

3.) Tiyeni tiphunzire kutula nkhawa zathu pa Yehova nthawi zonse ndipo osaziganiziranso – 1Petro

5:7. Tidzichitabe zimenezi mpaka chitakhala chizolowezi chathu. Mutha kuchita bwino ndi nzeru

imeneyi. Pamene mantha aja akufikiraninso, tangokumbukirani kuti “nkhani imeneyi ndampatsira

ndi kumusiyira Mulungu.”

4.) Zindikirani kuti kuzolowera kudera nkhawa kuli monga “fano”, chifukwa chizolowezi cha moyo

umenewu chimapangitsa munthu kumangoganizira za iye yekha mwini, zokhazo

zongomkondweretsa iye basi. Munthuyo amalephera kutumikira Mulungu ndi kupindulira

okondedwa ake. Tayani khalidwe limeneli ndi kunena motsimikiza mtima kuti: “ndapereka ndi

kusiya zonsezo m’manja mwa Mulungu ndipo ndiri ndi chikhulupiriro chonse cha zotsatira zake.”

Ngati chomwe ndi madera nacho nkhawa ndi kuchiopacho chochitika, ndiyenera kungochilandira

popeza chochitika kwa Mulungu ndi chifuniro chake. Sindidzavutika ndi kuchiganiziranso.

5.) Zindikirani kuti zambiri zomwe timaziopa ndi kudera nazo nkhawa sizimakhala zoona, koma

chifukwa chomangoopabe mopitirira, kenako zimatha kukwaniritsidwa. Taonani Yobu 3:25, ndipo

Page 18: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

18

mufanizire nkhani imeneyi.

6.) Yankho lenileni loyambirira la nkhani imeneyi ndilo lokhala ndi chidwi chodziwa Mulungu. Iye

ndiye yankho. Iye ndiye woyenera chikhulupiriro chathu chonse – Masalmo 27:1. Sitisowanso wina

ayi. Iye amafuna kusunga bwino miyoyo yathu. Koma tiyenera kumudziwa Iye kuti tikhulupirire

chimenechi.

7.) Taphunzirani kuika maganizo anu onse ndi kuyang’ana pa Mulungu nthawi zonse, pamodzi ndi

malonjezo ake, osati kumangoyang’ana pa mavuto anu kokha. - Mateyu 14:25-31.

8.) Tingathe kupanga ganizo losankha kukhulupirira Mulungu. Sikungomva chabe m’thupi kwanu ayi.

Koma kupanga chisankho ndithu chomwe Mulungu atilamulira kusankha.

9.) Mungathe kulamulira mtima wanu kuti ukhale chete ndi kumvetsera maganizo ndi ulamuliro wanu -

Masalmo 131:2; Yohane 14:1.

10.) Kudzitangwanitsa, makamaka potumikira Mulungu kumathandiza kuchepetsa mantha ndi nkhawa

zomwe zomakhala zikungoyenda m’maganizo mwathu pamene tingokhala duu osachita kanthu.

11.) Nthawi zinanso pali mankhwala ena, makamaka operekedwa ndi anthu oyenerera moyenerera

angathe kuthandiza kuyembekezera pamene munthuyo kuyesa kuphunzira ndi kudzilolera kuti

ayambe moyo wabwino watsopano, komatu sibwino kumwa mankhwala amenewa kwa nthawi

yaitali.* Chifukwa mankhwala ena ali ndi zovuta zina zomwenso zikhoza kumatsautsa. [*Nthawi

zina m’thupi mwathu mumavuta ndipo timadwala, kotero kuti kumakhala kofunika kumwa

mankhwala kwa kanthawi. Tiyenera kuchita monga momwe kufunikira chimodzimodzi ndi momwe

timachitira pomwa mankhwala a matenda a shuga.]

C. Zilakolako za Zonyansa ndi Makhalidwe Okhumba ndi Kukonda Zinthu Zosavomerezeka.

1) Uhule uli ndi zigawo zambiri, kuyambira ku (kukeha), kutulutsa umuna mwadala mwa iwe wekha,

kuseweretsa maliseche, kuganiza zachilendo, chiwerewere chodziwika, kuonera zithunzi zolaula ndi

za umaliseche, ngakhale kuwerenga kumene, uhule, kugonana amuna kapena akazi okhaokha,

kudzipereka kuti muonetsedwe m’macheza, maso ofuna kuona umaliseche, kuseweretsa ana

powasautsa m’chiwerewere, kugonana ndi nyama, kugwirira ndi kubvutitsa, ndi zina zotere.

Ngakhale ukapolo wa mtundu umenewu anthu ambiri amautenga ngati woipitsitsa kuposa

maukapolo ena onse, palibe chousiyanitsa ndi ukapolo wina ulionsewo. Mulungu adzakhululukira

onse achita tchimo la zilakolako zimenezi, ngati atalapa ndi kubwerera kuti Iye, ndinso

adzawathandiza kuthana ndi kulekana nayo moyo wotengeka ndi kugonjetsedwa ndi ukapolo wa

zilakolako zimenezi.

2) Ukapolo umenewu uli ndi chionongeko chachikulu zedi. Makhalidwe okonda ndi kukhumba zinthu

zosavomerezekawo, amalekanitsa munthu ndi Mulungu – Ahebri 13:4; 1 Akorinto 6:9,10. Ukapolo

umenewu umatsegulira munthu ku moyo womadwaladwala m’thupi mwake ndinso m’maganizo a

pansi pa mtima, koma umaononga ubale wabwino wa m’banja womwe ukadathandiza kudzakhala

m’moyo wabwino ndi wokomakoma kwaphumphu ndi wotetezeka. Ukapolo umenewu umachotsa

kudzisungira ulemu, umayambitsa manyazi ndi moyo wotsutsika, ndiponso kupepusa onse pamodzi,

iye womangidwa ndi ukapolo wa mtundu umenewu, ndi anthu onse omwe amagonjera ndi kulolera

kuti zilakolakozi ziwasangalatse ku zofuna zawo.

3) Kodi anthu amakokeredwa bwanji ku ukapolo wa uhule kapena nkhuli ya chiwerewere?

a. Podziona ngati wosafunikira, wachinyamata amatha kudzipereka ku khalidwe lochita za

dama kapena zinthu zosavomerezeka pa umunthu.

b. Anthu osowa anzawo ndi opanda chitetezo omwe sanayambe akondedwapo ndi

Page 19: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

19

kulandiridwa, amakhala ndi njala yofuna kukhala ndi abale, ndipo amafunafuna ubalewo

podzera ku kupereka matupi awo ku chiwerewere. Anthu ochita zosavomerezeka pa

umunthu, nthawi zonse amangofuna kulandiridwa ndi kukhala pa ubwenzi wogulitsana ndi

kuchita chigololo.

c. Kukhala womalingalira mozama ndi kumalota mwa njira ina za kugonana, kumayamba

chifukwa chofuna kuiwala ndi kuchotsa kusakondwa ndi kusowa chochita. Pomamvetsera

nyimbo za mu wailesi, wailesi ya kanema, zowerenga za dziko ndi zina zotere, timatha

kupeza maganizo ena oyamba kutipatsa chikoka cha chiwerewere. Zimayamba

kusangalatsa, ndipo kenako maganizo onse amoyo wathu amangomangiririka kuzungulira

zomwezo. Imeneyi ndi njira yapafupi yotilowetsa kumoyo wa ukapolo wozolowera kuona,

kumvetsera ndi kuwerenga za umaliseche ndi zolaula. Munthu ukazoloweranso zimenezi

ndiyenso wapeza njira yolowa nayo ku ukapolo wokhala ndi chizolowezi chochita zinthu

zosavomerezeka pa umunthu, ndiponso zachiwawa ndi kuzunza.

d. Kusowa chikondi chochokera kwa bambo kumapangitsa mwana wamkazi kufunafuna

chosowa ndi choyenera kwa amuna ena molakwika. Kusowa chikondi chochokera kwa mayi

kumapangitsa mwana wa mwamuna kufunafuna chosowa ndi choyenera kwa akazi ena

molakwika. Kafukufuku waonetsa kuti ngati bamboo kapena mayi akana kulandira ndi

kugwira udindo wawo atha kupangitsa kuti anawo adzingofuna kukhala ndi mnzawo

wachitengedwe chifanana ndi chake. Izi zimayambitsa ukapolo wozolowera kugonana

pakati pa mwamuna ndi mwamuna mnzake ndinso mkazi ndi mkazi mnzake.

e. Nthawi zambiri ana amagwa mu tchimo la ukapolo wa chiwerewereli malingana ndi

mazunzo omwe amakomana nawo kunyumba. Choncho alangizi okhwima nzeru,

amachiyesa chanzeru kulangiza banja lonselo m’malo mwa wovutika yekhayo.

f. Masiku a makono ano chikhalidwe chathu munjira ina, chimavomereza moyo wochita

zosavomerezekazi chifukwa cha “ufulu wa chibadwidwe” wochuluka, pali maganizo ofuna

kudzisangalatsa kwa kanthawi, kungololera kupeza phindu popanda kuganizira za udindo

ndi zotsatira zake, ndi kungozolowera kudzikondweretsa ndi chiwerewere ngati chimake

chenicheni cha moyo.

g. Zosangalatsa ndi zokondweretsa za kanthawi kochepa chabe za chiwerewerezi, ziri ndi

chikoka cha chikuru kwa anthu momwe zakhala zikuchitira.

4.) Kuti munthu athawe ukapolo wa nkhuli ya chiwerewere, iye ayenera kusintha maganizo

a. ndi zikhulupiriro zina za kufunika kwa umunthu wake, maubale ake ndinso aganizire mozama

za

b. nkhani yogonana malingana ndi chifuniro cha Mulungu.

5.) Ukapolo umenewu ungasintha pokhapokhapo pamene mukomana ndi Yesu Khristu, ndi

kutembenukadi moona kuti apeze mphamvu yomuthandiza kupulumuka ndi kuthawa ukapolo wa

chiwerewerewu. Ku chitana chiwerewere amuna okhaokha kapena akazi okhaokha, malingana ndi

akatswiri, akuti ndi ukapolo wopanda mankhwala. Koma anthu ogwidwa ndi ukapolo umenewu

utha kuyeretsedwa, ndi kumasulidwa m’dzina la Yesu. Taonani 1 Akorinto 6:9-11, ndipo

mufanizire.

6.) Pamene munthu akhutitsidwa ndi zofuna za chiyero ndi maubale olungama, ndiponso pamene

munthu adzimvetsa yekha bwino, pamenepa nkhuli ya chiwerewere siyikhalanso monga chinthu

chowopseza moyo wake.

7.) Mukaona munthu wobadwa mokongola, musapitirize maganizo anu poyamba kumusirira ndi

kulakalaka mutachita naye chiwerewere ayi. Kusirira koyipa komwe, Yesu akunena mu bukhu la

Page 20: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

20

Mateyu 5:28. Kukhudza kuganizira, osati kuzindikira kokha, kuyamikira za maonekedwe a

munthu sitchimo ayi – umu ndi momwe Mulungu anatilengera. Zotsatira za kuyamikira kumeneku

ndizo zomwe zingakuchimwitseni kapena ayi. Kumangolapalapa ndi kuvomereza zinthu zomwe

zinalengedwa choncho, ndi kukhala kwake, zingadzakupatseni chizolowezi chomangoganizira

chiwerewere m’malo mothandiza munthuyo kumasuka ku tchimo la nkhuli ya chiwerewere.

Kuzolowera kudzitchula wolungama ndi woyera kwambiri kutha kukugwetsani mu ukapolo

wodzinyenga ndi kudzitenga ngati nokha olungama, ndipo izi zidzakuletsani kutumikira Mulungu.

8.) Pamene munthu atulukira kuti ali ndi maganizo osirirasirira, iye ayenera ayambe nthawi yomweyo

kupemphera kuti akhululukidwe, avomereze, ndipo atembenuzire maganizo ake kuzinthu zina

zabwino. Ndi bwino kutaya maganizo oipa ndi kulowetsa m’malo mwake maganizo olungama

m’malomo, njira imeneyi imathandiza koposa kumangolimba nazo osasiya nthawi zonse.

Kumangoti, lero walapa, mawa walapanso, choncho, choncho, izi zimapangitsa kuti zilakalakazo

zisaiwalike mumtima mwanu.

9.) Munthu asayembekezere kuti angamasuke ku ukapolo wa nkhuli ya chiwerewere ndi kuchita

zosavomerezeka pa umunthu, ngati alibe chidwi chofuna kusiya kudzisangalatsa ndi zokoka

mtima zoyambitsidwa ndi nyimbo za muwailesi, kuwerenga zachabe, kuonera televishoni,

maubale achabe, malo azisangalalo ndi zizolowezi zocheza ndi adama – 1 Akorinto 6:18; Genesis

39:19.

10.) Khazikitsani chizolowezi chomachotsa ndi kuthana ndi makhalidwe pa nthawi yomwe angoyamba

kumene, pa nthawi yomwe sanafike pomera mizu - Yobu 31:1.

11.) Pamene mumtenga munthu ngati munthu, ndiye kuti simudzamuona ndi kumtenga munthuyo ngati

thupi chabe. Ganizirani mozama ndi kumtenga munthuyo ngati munthu ndipo mumzindikire kuti

ndi chifanizo cha Mulungu, m’malo mongoganizira zochita naye chiwerewere

12.) Ngati muli pa umbeta ndipo muli nazo mphamvu zofuna kugonana ndi mkazi zomwe zikuvutitsa,

tangoyesani kumachita masewero osiyanasiyana, kaya ntchito zina ndi zina zotere.

13.) Njira ina yothandiza ndi yodzipereka kwa mbale wina wodalilika ndi wokhulupirika kuti

akulimbikitsani kuthana ndi ukapolo umenewu – Yakobo 5:16. Mukhale wowerengera mbaliyo za

moyo wanu.

D. Mankhwala Ozunguza Bongo ndi Mowa -

1) Momwe zimaonongera uzimu: kutayika m’maganizo, kuononga kachisi wa Mulungu, kutayika

kwa chiyanjano ndi Mulungu, kuononga ndi kusokoneza ena - Mateyu 22:37; 1 Akorinto

3:16,17; 6:19,20. Kumwa mankhwala ozunguza bongo kuli chimodzimodzi ndi kuipa kwa

kuledzera – Miyambo 23:29-35; 1 Akorinto 6:12.

2) Momwe zimaonongera maganizo a pansi pa mtima ndi thupi: kumangidwa

kulamulidwa mavuto amangokulirakulirabe, osathetsedwa, thupi ndi maganizo zimaonongeka.

Nkosavuta kubvulala, kapena kupha, kapena kuphedwa ndi ngozi zina. Potsiriza pake kupenga

kenako imfa.

3) Zochititsa kuti munthu amangiririke ku ukapolo wotenga mankhwala ozunguza bongo:

a. Kukakamizidwa ndi anzawo amsinkhu wawo.

b. Kuonetsa kuti “akula tsopano.”

c. Kugalukira / Kuukira.

Page 21: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

21

d. Kuthawa moyo wopanda chisangalalo.

e. Chidwi chofuna kudziwa ndi kuona gwero la zinthu.

f. Kukakamizidwa ndi ogulitsa omwe amaonetsetsa kuti akugulitsa ndi cholinga

chokwaniritsa chizolowezi chawo.

g. Kukhala wopanda zoganiza zirizonse zapansi pa mtima, kusadzidalira wekha,

kuwawidwa chifukwa chosowa mtendere ndi moyo wa tsiku ndi tsiku.

h. Kukodwa ndi ukapolo wosuta fodya, mankhwala ozunguza bongo, mowa ndi zina

zoledzeretsa kwa makolo athu.

i. Kuyanjana ndi athu okodwa ndi ukapolo onga umenewu.

4.) Anthu omwera mankhwala ozunguza alikufuna kuthawa kapena kuiwala moyo, koma Mulungu

atiphunzitsa tiyenera kufungatira ndi kulimbika pa moyo wathu. Tiyeneranso kuutenga moyo

ngati wabwino, ngakhale pamakhala zovuta zina, chifukwa Mulungu ali nafe ndipo ali ndi

cholinga chabwino, komanso zokwaniritsa za moyo wathu.

5.) Mankhwala oledzeretsa ndi mowa amangopitirira kutsata moyo womangozungulira wosatha

wopsa. Mavuto amapangitsa munthu kulowa mu nsinga za ukapolo wina zomwenso

zimangoonjezera mavutowo. Mavutowo amangoukiraukirabe ndi zina zotere. Taonani

zowonetsedwa za mu maphunziro wa izi:

6.) Alangizi amati, njira yoopsa ndi yopambana yogonjetsera ukapolo umenewu “ndi yongosiya

nthawi yomweyo”. Inde padzakhala masiku ena omva kupweteka chifukwa cha chibaba, kenako

sabata zingapo, ndiponso kenako miyezi ingapo yovutika mwakuti. Pali mankhwala ena omwe

kasiyidwe kake kamafuna malangizo a dokotala. Kusiya zimenezi kuli kwa mtengo wapatali ndi

kwa phindu loposa kupweteka komwe tingomve pamene tikusiya. Munthu ayenera kutsimikizira

ndi kuika mtima wake wonse pa ganizo lake lalikuru lofuna kusiya ndi mphoto yake atatha

zimenezi.

7.) Munthu atha kupambana kapena kulephera pa maganizo ake ofuna kusiya kutenga mankhwala

ozunguza bongo ndi zoledzeretsa molingana ndi anzake amsinkhu wake, kapena amene

amakhala nawo pafupi nthawi zambiri ndi zinthu zomuzungulira. Pali magulu ena a nyimbo ndi

zina, malingana ndi chibadwidwe chawo amalimbikitsa kutenga zozunguza bongo ndi nkhuli ya

chiwerewere. Palinso magulu ena monga “Alcoholics Anonymous,” ndi chigwirizana chomwe

chimathandiza kumasula munthu ku nsinga zimenezi.

8.) Kuti munthu athe kugonjetsa ukapolo umenewu, ayenera kusinthika mu zokhulupirira zake za pa

moyo wake wa iye mwini, ndi za pa umunthu wake wa iyenso mwini. Taonani mndandanda wa

zinthu khumi ndi ziwiri zoperekedwa muphunziroli zokhudzana ndi uchiledzelele zomwe

zimagwiritsidwa ntchito mu ntchito zina za maukapolo ena.

9.) Chikhristu chikuchita bwino ndi kupambana pothandiza anthu ndi kumasula ena omwe alephera

kusiya ukapolo wotenga mankhwala ozunguza bongo ndi zoledzeretsa pogwiritsa ntchito njira

zina ndi magulu wamba ena. Pali magulu ena monga “Teen Challenge,” omwe achitako bwino

mpaka 80% kumapita mtsogolo, pamene magulu wamba ena amaungochita bwino pang’ono

penipeni pangofikira 5% kapena 10%. Koma magulu a Chikhristu amapambana chifukwa

amaphunzitsa munthu kusintha moyo wake wonse mwa Uthenga Wabwino.

E. Ukapolo Wosakaza Ndalama Pogula Mopitirira Muyeso

1.) Momwe zimaonongera ku uzimu: umbombo ndi dyera ziri monga kupembedza mafano pamaso

pa Mulungu - Akolose 3:5. Ukapolo wadza chifukwa cha ndalama, umatitchinjiriza kuti tisathe

Page 22: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

22

kutumikira Khristu wathu ndi chuma chathu, kuononga umboni wathu chifukwa cha ngongole

ndi kusokonezeka kwa zinthu. Kugula zinthu ngati njira yothetsera mavuto kuli monga thandizo

lopanda choonadi kwa munthu wa umbombo ndi dyera – ndipo mchitidwe umenewu

umangopitirira osatha konse.

2) Momwe zimaonongera maganizo a pansi pa mtima ndi thupi, munthu umataya ulemu wa iwe

mwini, kulephera kuchita zinthu zina zako ndi za pa banja pako, kupanikizika ndi kudera

nkhawa, kuchulukirabe kwa ngongole ndiponso kutaya mwayi wokhulupiridwa.

3) Zizindikiro Zina za Ukapolo Wodza Chifukwa Cha Ndalama. Kutanganidwa kwambiri ndi

ndalama m’malo mwa Mulungu, kunyenga kuti mupeze chomwe mufuna, kungogula ndi

cholinga chofuna kuchotsa kusungulumwa , kusapereka mwa ufulu kwa Mulungu, kulephera

kuthandiza anthu, kulephera kulipira ngongole zina, ndalama kuthera pa njira mwezi usanathe,

kulephera kusungira zodzathandiza mtsogolo, kumangokhalira ngongole pofuna kupeza

zofunikira za tsiku ndi tsiku, ndi zina zotere

4) Mfundo Zothandiza Pogonjetsa Ukapolo Wosakaza Chuma -

a. Tulukirani ndipo mugonjetse muzu wake weniweni wa vuto umeneli: kusowa mtendere

wa mumtima ndi kusowa chochita; kumangokhala wopanda khalidwe kwa moyo wako

monse; kusadziwa mfundo zabwino za kasamalidwe kachuma; kusatetezeka chifukwa

chokhumba zinthu nthawi isanakwane; kunyada, kufuna kukondweretsa anthu;

kusakhutitsidwa chifukwa chomvera malonda olengezedwa pa wailesi ndi m’manyuzi;

kudzikonda; kusowa chidziwitso cha za uzimu; ndi zina zotere

b. Khazikitsani ndi kuzolowera khalidwe labwino lokhala ndi moyo wokhutitsidwa ndi

zomwe muli nazo, kukwanitsidwa kwenikweni sikuli mu zinthu zomwe tiri nazo ayi,

koma ndi khalidwe lodziwa chomwe chili chofunika kwa munthu – Afilipi 4:11-13; 1

Timoteo 6:6-9.

c. Sinthani zikhulupiriro zanu pa choonadi chenicheni, polingalira za chuma, pa kuwerenga

za choonadi cha mawu a Mulungu – Masalmo 119:105; Yohane 8:32. Pamene choonadi

cha Mulungu chikopa khalidwe la moyo wanu, momwemonso mudzayamba kulemekeza

choonadi chenicheni, osati ndalama zokha ayi.

5.) Malangizo Othandiza Kusamala Kagwiritsidwe Ntchito ka Ndalama.

a. Yambani mwadikira kanthawi musanagule chomwe mukufunacho, monga tsiku limodzi.

b. Yambani mwagwirizana pa banja panu pa za muyezo wa chinthu chomwe mukufuna

kugulacho musanakambirane.

c. Khalani ndi maganizo ndi dongosolo lothetsa mangawa pa nthawi yakuti.

d. Musagwiritse ntchito ngongole pa zinthu zofunika msanga, za tsiku ndi tsiku.

e. Kumbukirani kuti chinthu chotchipitsidwa mtengo sichingakusungireni ndalama

pokhapokhapo, mutachigula.

f. Onongani makadi onse otengera ngongole ngati mukulephera kuchita nawo bwino.

Muzilipira ngongole yonse mwezi uliwonse kapena kungosiya kuwagwiritsa ntchito

kumene.

g. Pewani maulendo okagula zinthu m’gulu la anzanu.

Page 23: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

23

h. Musamachuluka zonena kapena kuwiringulawiringula pofuna kugula zinthu.

i. Pewani kugula m’masitolo akuluakulu pokhapokhapo, ngati pali pofunikiradi, ndipo

simungachitire mwina.

j. Phunzirani kusiyanitsa pakati pa zinthu zofunika ndi zosowekadi. musanagule

chirichonse, tadzifusani, Kodi chinthu chimenechi chikusowekadi?

k. Dzazani moyo wanu wonse ndi zonse zabwino zamphumphu zokondweretsa Ambuye.

F. Kudya Mopitirira Muyezo -

1.) Chionongeko cha uzimu: Kuononga kachisi wa Mulungu, matupi athu - 1 Akorinto 3:16,17;

6:19; kuchepetsa umboni wa Chikhristu; kupanda khalidwe kumakhazikika m’miyoyo yathu

ndiponso kulowerera mbali zina za ukapolo - 1 Corinthians 6:12.

2.) Chionongeko cha thupi ndi maganizo: Mabvuto a umoyo; kutaya ulemu wa umunthu wathu,

zimabvutisa ubale wa ukwati wathu.

3.) Kudyaidya kumakhuzananso ndi kusakondwera, kuwawidwa kapena kupsya mtima. Khalidwe

lotere limakulirabe ngati tipitirira osasiya. Pamenepa munthu afunika kulimbika kupeza

mtendere ndi chimwemwe cha Khristu m’kati mwa mtima koposa kusangalatsidwa ndi kudya.

4.) Nthawi zina munthu amakhala wodyaidya chifukwa anazolowera kuyambira umwana wake.

Pamenepo ayenera aphunzire kudziletsa. Patsogolo tiri ndi phunziro lonena za kudzisungira

ulemu ndi mwambo.

5.) Nthawi zina bvuto la thupi pa zina za umoyo limapangitsa munthu kukhala ndi chilakolako

chakudya kwambiri. Pamenepo pafunika kuthandizidwa ndi mankhwala ataonana ndi dokotala

wodziwa za mabvuto otere.

6.) Munthu angathandizidwe kupulumuka ku ukapolo wa mtundu wotere ngati chidwi chake

chofuna kusiya zimenezi chilimbikitsidwa.

a. Kulani m’chikondi cha Khristu. Tingathe kuchita zinthu zambiri chifukwa cha Yesu,

zomwe sitingathe kuchita pa tokha.

b. Ganizirani zomwe zimabvutitsa anzathu chifukwa cha ukapolo wotere.

c. Ganizirani mozama pa za mphotho zimene muyembekeza kukhala nazo pochita

chodziletsa pa nkhani ya dyera.

d. Kuika maganizo pa zinthu zina zimathandiza koposa kungolimbana nthawi zonse ndi

maganizo a dyera.

G. Ukapolo wa Kumaonera Zithunzi za Wailesi (TV addiction):

1) Chionongeko cha uzimu: Uwu ndi ukapolo wina woopsya ndi waukali chifukwa

umaoneka wosangalatsa kwambiri, wooneka ngati wosavulaza, koma umabweretsa

mavuto osaneneka pa moyo wathu. M’menemo timaphunzira zambiri za dziko lapansi

zosathandiza Mkhristu, zina za osakhulupirira, zonyenga, za mzimu wadama wa nyengo

ino zimene zimagwira maso athu maora ochuruka patsiku liri lonse ndikuyamba kusintha

maganizo athu kuti tifune zimene tikuonerazo. Pamodzi ndi zodetsa za uzimu ndi za thupi,

palinso kuononga kwa nthawi yocheza ndi banja, nthawi yotumikira Mulungu imatayika,

Page 24: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

24

nthawi yolumikizana ndi kulankhulana imaonongeka, kusakwanitsidwa chifukwa cha za

malonda olengezedwawo komanso za anthu ena osayenera kutsanziridwa pa khalidwe

lawo m’moyo mwanu ngakhale mwa ana anu. Kufoka ndi kufa kwa uzimu kumadza mwa

kuonera zithunzi za pa wailesi kopitirira. Pamenepo choipa chimayamba kukhala chinthu

chosaopsya ndi chololedwa kwa ife, ndipo timayamba kukhala akhungu osaonanso

chimene chichitika pa ife.

2) Chionongeko cha maganizo ndi thupi: Kusowa chilimbikitso cha thupi,

kusadzikhulupira tokha; kusakhutitsidwa; mchitidwe wa kumenyana ndi kutsutsika

m’mtima.

3) Aliyense asachedwe kudziwa chionongeko cha ukapolo wotere, adzutsenso

chikumbumtima chake, nayambe kuona zopindulitsa zoposa zosoweka m’moyo mwake,

pamenepo ayambe kulimbana ndi gwero lenileni lomupangitsa kudzikondweretsa

kopitirira ndi zithunzi za wailesi.

4) Aphunzire kuti mwa chisomo cha Mulungu, moyo weniweni ndi wabwino koposa

kumalowera ndi mbiri zoganiziridwa ndi ena zoturuka pa wailesi yakanema.

5) Tayesani kuchitanso zochita zanu zina m’banjamo zimene munazisiya nthawi yaitali.

Muzasangalatsidwa ndi kutsitsimuka kwambiri.

6) Mabanja ena amaika malire ake otha kuonera zithunzi za wailesi, monga maora ochepa

sabata imodzi.

7) Televishoni pa yokha siyoipa ayi, koma ‘’ngati ikubweretserani zovuta zina ndiye

ndiyoyipa,’’ monga anenera Bill Gothard, ndipo ndikoyenera kuichotsa - Mateyu 18:7-10.

Iyitu sinkhani yamasewera. Mwa uzimu nkhani imeneyi ndi ya ifa kapena moyo, khani ya

muyaya.

H. Kudzitcha wochita bwino (Ungwiro):

1. Chionongeko cha uzimu: Kutsutsika chifukwa chokhala ndi zoyembekezera zosatheka;

kutaya mwayi wina chifukwa chotaya nthawi ndi mphamvu; kufooka mwa uzimu;

kupembedza mafano kumene kumatilekanitsa ife ndi Mulungu; kulephera kulandira

chisomo cha Mulungu; kulephera kukhululukira.

2) Chionongeko cha thupi ndi maganizo: Matenda osiyanasiyana a m’maganizo ndi

m’thupi, amatopetsa kwambiri, ndinso kupangitsa kuchita zinthu mokokowa.

3) Munthu waungwiro ayenera kumakonza zinthu zikhale bwino koposa ziliri. Munthu

wochita zaungwiro ndiye amene samatsiriza ntchito imene aigwirira.

4) Khalidwe la ungwiro, limayambika pa umwana wake wa munthu kumene makolo ake

amakondwera naye pokhapo pamene achita bwino. Sanalandiridwa mwa iye monga mwa

iye yekha.

5) Pokhala munthu wosalandiridwa ndi anzake amayetsetsa kupeza chitetezo kuti

alandiridwe mwa kupanga zinthu zabwino kopambana.

6) Munthu woziyesa wangwiro afunika kumvetsetsa zoona zina zingapo:

a. Chisomo cha Mulungu chimalandira amene alakwa ndi kuperewera m’moyo wake.

b. Pokhala woziyesa wangwiro nkosatheka munthu kutumikira Mulungu koma

kutumikira za iye yekha. Chifukwa kudziyesa wangwiro kumalekanitsa utumiki wake

Page 25: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

25

wa kwa Mulungu ndi ena, ilitu ndi monga fano.

c. Pa kuyetsetsayetsetsa, amachepetsa kupindula kwake m’moyo wake wauzimu.

7) Munthu angathe kuphunzira kuchepetsa zomwe iye mwini amadziyembekezera kuchokera

kwa iye mwini ndi kuyamba kuchita monga wobvomerezeka. Ndipo pang’ono ndi

pang’ono zidzazolowereka.

8) Monga munthu amakonza maganizo a ulemu wa iye yekha, atha kuonanso kuti si

chanzeru kumachita moti anthu amutche wangwiro, woposa ena.

Potsiriza: Mulungu afuna tonse tikhale omasuka pa zimene zimabweretsa masautso, chionongeko ndi ukapolo

m’moyo mwathu. Thandizo la Mulungu lilipo. Mitundu yina ya ukapolo ilipo imene sitinakamba, koma malangizo

amene taphunzira angathandizenso mabvuto enawo.

Magawo Khumi ndi Awiri a Zidakwa Zosadziwika (Alcoholics Anonymous).

1. Tidabvomereza kuti tidalephera kudzitchinjiriza ku mowa kotero kuti tinalephera

kulamulira miyoyo yathu.

2. Kenako tidadzakhulupirira kuti pali mphamvu yoposa yathu yotha kubwezeretsera umunthu

wathu ndi maganizo oganiza bwino.

3. Tidaganiza zobwezeretsa cholinga ndi miyoyo yathu ku chisamaliro cha Mulungu, pamene

tinali kuyamba kumumvetsa.

4. Tidayamba kudzifufuza mopanda mantha ndikudziturukira mwa ife tokha pa moyo wathu

wochita zosavomerezeka ndi umunthu.

5. Tidavomereza kwa Mulungu, kwa ife eni, ndi kwa olengedwa anzathu ena onse za choonadi

chenicheni cha zolakwa zathu.

6. Tinali wokonzekera kuti Mulungu atichotsere zolakwika zonsezi za khalidwe lathu.

7. Modzichepetsa tidamupempha kuti atichotsere zofooka zathu.

8. Tidalemba mndandanda wa anthu onse omwe tidawalakwira ndi kuwakhumudwitsa, ndipo

tidali ndi chidwi chofuna kukonzanso ubale wathu ndi iwo onse.

9. Tidalinganiza ndi kukonza zonse zomwe tidawalakwira anthuwo monga mwa kutheka

kwake, kupatula zokhazo zomwe ngati tikadachita nazo zikanawasautsa mumtima kapena

kuononga ena.

10. Tinapitirira kumadzifufuzabe ndipo pamene tinatulukira kuti tinali wolakwa tinali

kuvomereza.

11. Mwa pemphero ndi kulingalira tikonzense chikumbumtima chathu kulumikizana ndi

Mulungu, monga tidamvera Iye, tizipempherera chidziwitso cha chifuniro chake kwa ife ndi

mphamvu zotithandiza kutero.

12. Titakhala ndi chitsitsimutso cha uzimu kupyolera mwa zigawo zimenezi tidayeserera

kutengera uthenga umenewu kwa onse omangidwa munsinga za ukapolo wa uchidakwa,

ndikumachitachita mfundo zimenezi mu zochita zathu zonse za nthawi ndi nthawi.

Kuchokera ku: ”The Sexual Addiction” zolembedwa ndi Patrick Carnes, Ph. D. Sililoledwa kukoperedwa kupatula

kwa okhawo a pa sukulu kapena ofuna kuphunzira paokha.

Phunziro 6 – Kubvula Umunthu Wakale

Malonje: Pambuyo pa machimomu pali ukapolo umene ndi wofalikira kwa anthu onse. Pambuyo pa machimo, pali

bvuto la uchimo. Munthu wochimwa ndi mdani wa Mulungu, wopikisana, wofuna kukhala wosalamulidwa ndi

Mulungu, woyang’anira moyo wake. Ali ndi moyo wochimwa umene umakana kumvera Mulungu, pokha pokha pa

zofuna zake. Khristu anatimasula ku moyo wakale, wopikisana ndi Mulungu komanso kutipanga ife kukhala

zolengedwa zatsopano, wobadwanso mwatsopano, wokhala ndi makhalidwe atsopano ngati Mulungu, zimene

Page 26: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

26

zimakondwera kuti Mulungu akhale Mulungu. Amabvomereza umulungu wa Yesu Khristu pa moyo wawo.

1. Tisanatembenuke, Tinali “m’thupi” Kapena Tinali “ochimwa” –Aroma 7:5.

A. Moyo wochimwa ndi woipa pamaso pa Mulungu ndipo sungathe kumvera kapena kuyamikira

choonadi chake – Aroma 8:7-8 7:14-25; 1 Akorinto 3:1,2; 2:14.

B. Zimenezi zakhala zoonadi kuyambira pa ugwa kwa Adamu ndi Hava amene anafuna kukhala

“milungu,” wosalamulidwa ndi Mulungu – Genesis 3. (Ku mbuyo kwawo kunali Satana, yemwe

anagwa chifukwa cha kudzikuza ndi kuukira – 1 Timoteo 3:6; onaninso Yesaya 14:12-14; Ezekiel

28:11-17).

C. Moyo wochimwa umalimbana ndi mzimu, kuti ife tisamvera mzimu – Agalatiya 5:17.

D. Mwa “thupi” (lotanthauzidwa umunthu wochimwa), Paulo satanthauza thupi lenileni ayi, koma moyo

wogalukira umene umalamulira munthu wochimwa.

E. Chipatso cha moyo wochimwa ndi moyo woipa womwe umaononga zabwino zonse - Agalatiya 5:19-

21. Matsizirizo ake ndi imfa ya muyaya - Aroma 7:5b; 8:13a; Agalatiya 6:8.

F. Moyo wochimwa utha kukhala wopembeza kapena wolemekezeka pamene ukukondweretsa thupi

koma sungamvere Mulungu mu Masautso enieni chifukwa cholinga chake ndi kukondweretsa thupi.

G. Makhalidwe ena omwe angakuzindikiritseni moyo wochimwa:

1) Umadzikhulupirira wokha osati Mulungu.

2) Umadzikondweretsa wokha osati kukondweretsa Khristu – Afilipi 2:21.

3) Umadzilemekeza wokha osati Mulungu.

4) Umakana zimene zimatsutsana ndi chifuniro chake.

5) Umagwiritsa ntchito chipembedzo ndi Mulungu osati kugwiritsidwa ntchito ndi Mulungu.

6) Umachita ntchito zauzimu chifukwa cha dyera osati chifukwa cha Mulungu.

7) Umakonda malamulo ndi zochita za thupi osati za chilungamo cha mu mtima.

8) Sumadziwerengera kwa wina aliyense.

9) Umatsutsana ndi ena chifukwa cha zofuna ndi zokhumba zake.

10) Umakhazikika pa zinthu za pansi pano.

H. Moyo wochimwa sungathe kukonzedwa koma ndi woyenera kuphedwa.

2. Umunthu Wakale “umapachikidwa” (umaphedwa), pamene munthu abwera kwa Khristu – Aroma 6:6.

A. Ubatizo ufanizidwa ndi kuikidwa m’manda kwa moyo wathu wakale, ndi kuuka ku moyo watsopano

– Aroma 6:3-5; Akolose 2:11-12.

B. Mu ubatizo timalumikizana ndi Khristu mu imfa yake, kuikidwa komanso kuuka kwake - Aroma 6:3-

6; Agalatiya 2:20; Akolose 2:20; 2 Timoteo 2:11.

C. Kupyolera mu kulapa ndi mu ubatizo, “timafa ku machimo athu”, koma timakhala amoyo ku

Page 27: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

27

chilungamo –Aroma 6:11; Akolose 3:3; Agalatiya 5:24.

D. Timafa osati ku machimo okha komanso ku “umunthu wathu wakale” – Mateyu 16:24; onani Afilipi

2:6-7. Zimenezi ndizo zipanga nkhani yaikulu ya phunziroli.

3. Umunthu Watsopano Umabadwa mwa ife Pamene Tatembenuka.

A. Tinabadwa mwatsopano kuti tilowe mu ufumu wa Mulungu – Yohane 3:3-6; Onani Tito 3:5.

B. Mbewu yomwe imabala moyo watsopano ndi Mawu a Mulungu - 1 Petro 1:23.

C. Sitikhalanso ndi moyo wathu m’machimo chifukwa mbewu imeneyi imakhala mwa ife - 1 Yohane 3:9.

D. Ndife “zolengedwa zatsopano” – 2 Akorinto 5:17.

E. Chifanizo cha Mulungu chiri kukhala mwa ife – Akolose 3:9-10; Aefeso 4:24; 2 Petro 1:4.

F. Mzimu Woyera atithandiza ife kukhala ndi makhalidwe a Yesu – Agalatiya 5:22,23; 4:19.

G. Mitima yathu imafewetsedwa ndipo imapangidwa kuti igonjere chifuniro cha Mulungu – Ezekieli

11:19-20; Masalimo 40:8; Yeremiya 31:33.

H. Zimenezi zikhoza kutheka pokha pamene munthu pa kutembenuka kwake wakhudzidwa ndi chisoni

chifukwa cha machimo – Masalimo 51:17.

I. Makhalidwe a moyo watsopano:

1) Moyo wa chikondi chosadzikonda – 1 Akorinto 13:4-7.

2) Moyo wodzipereka ndi wogonjera kwa Khristu monga Ambuye wa gawo lirilonse la moyo –

Aroma 10:9; 2 Akorinto 10:5; Yeremiya 29:13. Mzimu wokonzeka kugonjera chifuniro.

3) Wobvomereza udindo wa Khristu kuti ndi woyenera kulamulira pa moyo wa munthu aliyense.

4) Ndi wokonzeka kudziwerengera kwa ena ndi kugonjera chifuniro cha atsogoleri a Mulungu.

5) Wokonda zomwe zikondweretsa Khristu, wosakonda zinthu zomwe Khristu adana nazo

kapena zofooketsa anthu ena.

6) Wokonda kugwira ntchito osati wongokondweretsedwa.

7) Ndi wokhudzidwa ndi chipulumutso cha ena osati zinthu za yekha.

8) Ali ndi malamulo a Mulungu pa mtima pake osati olembedwa okha.

9) Amakonda umodzi ndipo amakhala bwino ndi ena.

10) Ndi bwenzi la Mulungu, womvetsa chifuniro cha Mulungu, wokonda zomwe Mulungu

akonda ndi kudana ndi zomwe Mulungu adana nazo – Yohane 15:15.

11) Ndi wokhazikika pa zinthu za kumwamba ndi Mulungu.

J. Kugonjera kwatunthuku ndi chisankho chomwe munthu amapanga kuyambira pa chiyambi, koma

kudzipereka ku kumaukiraukira pamene munthuyu akula mu uzimu nazizindikira bwino.

Page 28: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

28

4. Ngakhale Umunthu Wakale Umafa pa Kutembenuka Mtima, nthawi ndi nthawi umayesabe kuuka ndipo

uyenera “kuphedwa” - Akolose 3:5.

A. Monga momwe dziko la Kanani linaperekedwa kwa Aisrayeli, iwo anayenera kumenya nkhondo kuti

aligonjetse kuti akhalemo mwa mtendere, chimodzimodzinso umunthu wathu wakale.

B. Mulungu amalemekeza ufulu wa umunthu wathu. Anatipatsa mwayi wakusankha chabwino ndi

kukana choipa, ndimo takulira kuti tifanane naye. Ngati Mulungu akanatipanga ife kuti tidzichita

zabwino zokha zokha mosasankha, sitikanakhala anthu ayi, koma makina.

C. Tiyenera kuganizira kawiri kawiri kuti matupi athu adzitumikira chilungamo osati chisalungamo –

Aroma 6:12-13. Tiyenera kuganizira kutaya choipa chonse ndi kubvala zabwino – Aefeso 4:22—5:4;

Akolose 3:5-14.

D. Mzimu Woyera amatithandiza kufetsa uchimo – Aroma 8:13.

E. Kudziletsa kapena kudzikanira zinthu ndi kosakwanira kugonjetsa umunthu wathu wakale woipa –

Akolose 2:20-23. Ngakhale malamulo sangathe kuligonjetsa - Aroma 8:3.

F. Zinthu zoyenera kuganizira popachika umunthu wakale:

1) Khalani wokonzekera kupirira.

2) Lolani Yesu kuti akhale Ambuye wa chirichonse pa moyo wanu (Akhristu ambiri satero).

3) Phunzirani kuti mumpange Yesu kukhala Ambuye ndi kuti agwire ntchito pa chipembedzo

chanu, mu ntchito ya mpingo, pamoyo wanu wa tsiku ndi tsiku, pa moyo wanu wa pa banja,

pa ntchito yanu, pamoyo wa mu dziko lanu, pa ndalama zanu, pamoyo wanu wa ku sukulu,

ngakhale pa ubale wanu wa umunthu ndi zina zotero.

4) Gonjetsani maganizo oipa pa nthawi yomwe afika kwa inu – 2 Akorinto 10:3-5.

5) Dyetsani moyo wanu watsopano ndipo iphani moyo wanu wakale:

a. Pemphero ndi kuphunzira Baibulo.

b. Osaleka kusonkhana limodzi ndi mpingo - Ahebri 10:24,25.

c. Ganizirani kwambiri pa moyo ndi ziphunzitso za Yesu - Ahebri 12:2.

d. Pemphani thandizo la Mzimu - Luka 11:13; Aroma 8:13.

e. Dulani chiri chonse chomwe chimadyetsa umunthu wanu wakale –Ahebri 12:1.

f. Koposa zonse, yang’anirani moyo wanu. Pamene musankha maganizo abwino, moyo

wotere umakulirakulira - Miyambo 4:23.

g. Ganizirani kuti Yesu angamve bwanji mutabwerera m’buyo kutsata umunthu wanu

wakale komanso anthu ena omwe amakuonani ngati chitsanzo - Ahebri 6:6.

6) Ziletseni mwa uzimu, ndipo pangani makonzedwe a moyo wanu.

a. Phunzirani kusala kudya - Masalmo 35:13.

b. Ganizirani ndipo phunzirani kunena kuti ayi, ku chiri chonse chomwe chingaononge

Page 29: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

29

moyo wanu wa uzimu.

c. Pangani zofunika zanu kukhala zolimba.

d. Kuti muonetse kudzipereka kwanu kwa Khristu, pangani izi:

1. Sonkhanani limodzi ndi mpingo nthawi iri yonse yomwe mpingo

ukusonkhana ndipo musaganizire zokhala kwina pa nthawi imeneyi.

2. Perekani za chikhumi za zopindula zanu kwa Mulungu mwa ufulu.

3. Lemekezani makolo anu mwa kuwachezera kawiri kawiri, kapena

kulankhulana nawo mwa njira iri yonse. Chotsani zovuta zonse zomwe

zingakhalepo pakati panu.

4. Pezani nthawi ya padera yowerenga Baibulo ndi kupemphera.

(Anthu omwe amafuna kukhala pansi pa malangizo awa ndi omwe amakula pa moyo

wawo wa Chikhristu).

e. Khalani okonzeka kudziwerengera kwa atsogoleri anu, (ngati nawonso atsata Khristu

ndi mawu ake), pamodzi ndi okhulupirira anzawo (monga pa gulu lothandizana).

f. Kusafuna kuti mudziwerengere pa maso pa anzanu ndi kugawana nawo malangizo,

kumaonetsa kuti moyo wake, wodzikonda, wotsutsana uja sunapachikidwe pa

mtanda.

Potsiriza:: Ngakhale pamafunika kuti Mulungu apirire nanu, komabe moyo wakale wotsutana ndi wodzikonda umatha

kuchotsedwa. Alipo anthu otizungulira amene adziperekadi kwa Khristu. Palibe chinthu chopambana ndi chosangalatsa

kwambiri kuposa moyo wa Chikhristu wodzipereka, wofanana ndi Yesu.

Phunziro 7 – Kukhazikitsa Moyo Wodziletsa

Malonje: Kodi mungathe:

- Kusunga ndalama chifukwa cha zinthu zina zobwera mtsogolo?

- Kukhala ndi nthawi yokhala chete ndi Mulungu?

- Kupewa kuchita miseche pamene mwamva kanthu?

- Kupita ku mapemphero mwa changu?

- Kukambirana ndi mnzanu za Khristu pamene ndi kovuta kutero?

- Kupereka kwa Mulungu zipatso zoundukula za zopindula zanu?

- Kusunga chiwerengero mu bukhu lanu la cheke?

- Kuchita ntchito kunyumba m’malo oonera kanema?

- Kupita kwa munthu yemwe mwamulakwira kukapempha chikhululukiro?

- Ziletseni zakudya, zakumwa, komanso zosangalatsa?

Page 30: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

30

- Musalole chikondi kuti chisokoneze moyo wanu?

- Gulani zosoweka ndipo Lipirani zofunika musanaononge ndalama zanu?

- Musalole kuchedwetsa ntchito pa zinthu zina zobvuta kuzichita?

- Dzipatseni nthawi yoti mupumule ndi kuyanjana pamodzi ndi banja?

- Chotsani maganizo anu pa zinthu zoipa?

- Khalidwe lanu locheza ndi anthu likhale lokhazikika?

- Yankhulani ndi kuchita moyenera ngakhale kufatsa kwanu kukuyesedwa?

- Kupita kukagona ndi kudzuka nthawi yoyenera?

- Tsekani kanema yanu kapena sinthani ndi kupita kwina pamene zoonetsedwazo ndi zosayenera kuonera?

- Onani momwe nthawi ikuyendera, kapena osafulumira pa msewu koposa lamulo la pa msewu?

Anthu ambiri omwe ali ndi mphatso zambiri, amakwaniritsa zochepa ndi kuzunzika kwambiri, amakhala ndi

moyo wosakondwa chifukwa amalephera kudzilamulira okha. Ndi chifuniro cha Mulungu kuti tidzilamulira moyo

wathu, ndipo Mulungu mwini amadzilamulira yekha – 1 Akorinto 14:33; Yakobo 1:13. Ngati tikule kuti tikhale ngati

Iye, tidzatha kudzilamulira m’miyoyo yathu - Agalatiya 5:22,23. Ndi kotheka kuti munthu atha kukhala ndi moyo

wodziletsa. Kusadziletsa ndi chizolowezi ndipo zizolowezi zoipa zitha kusinthidwa ndi zizolowezi zabwino. Ngati

tingaphunzire kudzilamulira tokha, tidzaturukira chinsinsi cha moyo wokondwa.

1. Kusadziletsa Kumatilepheretsa Zinthu Zambiri.

A. Timalephera zinthu zofunika chifukwa sitingathe kuchita zinthu zomwe ife sitimafuna kuchita, kapena

sitingasiye kuchita zimene tinazolowera kuchita.

B. Sitingapeze nthawi kapena ndalama zogulira zinthu zofunika chifukwa timaononga nthawi kapena

ndalama pa zinthu zongomkondweretsa zimene sitingathe kuzisiya – Miyambo 23:21; 6:10; 21:25.

C. Timatopa ndi kukhumudwa chifukwa cha chisokonezo cha mu moyo wathu wosadziletsa.

D. Ubale wathu ndi anthu ena umasokonezeka chifukwa cha moyo wathu wosadziletsa.

E. Tikhoza kugwa mu uchimo chifukwa chosadziletsa - 2 Petro 2:14a; 1 Akorinto 7:5; 2 Samuel 11.

F. Timalephera kupeza zinthu za mtengo wapatali chifukwa timalephera kukana zinthu zimene

zimatsutsana nazo – Genesis 25:29-34; Ahebri 12:16,17; Numeri 20:2-12.

2. Kudziletsa Kumapatsa Mphoto za Mtengo Wapatali.

A. Kudziletsa ndi kudzilemekeza ndi zinthu zogwirizana. Munthu wodziletsa amakhala bwino pa moyo

wake ndipo umakhala wotetezedwa.

B. Kudziletsa kwanu pa chinthu chimodzi kudzafalikira zinthu zina pamene mzimu wodziletsa

udzakhazikika mwa inu.

C. Munthu wodziletsa amapindula mu chiri chonse chomwe iye achita cha thupi ngakhale cha uzimu.

D. Pamene mulamulira moyo wanu, muli ndi udindo wophunzitsa kapenanso kulamulira anthu ena.

Page 31: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

31

E. Kudziletsa kumakuthandizani kuti muthawe zoipa kuti musakodwe kapena kuonongeka nawo.

F. Kupyolera mu kudziletsa, mutha kupitirira kuchita zabwino osati mu nthawi za mtendere zokha koma

ngakhale pamene inu mwatopa. Mwayesedwa kapena mwapanikizika, mudzakhalabe msilikali

wodalirika.

3. Zimene Zimapangitsa Kusadziletsa:

A. Ngati makolo sanamulangize mwanayo nthawi ndi nthawi adakali wamng’ono, zotsatira zake

mwanayo saphunzira kudziletsa yekha. (Atha kuphunzirabe njira zatsopano).

B. Kukhala ndi makhalidwe osadziletsa pa nthawi ya padera.

C. Mzimu wodzilamulira kapena wotsutsana.

D. Kubadwa ndi khalidwe losadziletsa (zimenezi zikhoza kukonzeka).

E. Kudwala.

4. Ndi Chifuniro cha Mulungu kuti ife Tikhale ndi Moyo Wodziletsa.

A. Kudziletsa ndi gawo limodzi la Uthenga Wabwino wolalikidwa ndi Paulo – Machitidwe 24:24-25.

B. Akulu, amene ali chitsanzo cha Akhristu ena ayenera kukhala odziletsa - 1 Timoteo 3:1-3; Tito 1:6-8.

C. Tikuphunzitsidwa kugwiritsa ntchito nthawi ndi mwayi wathu moyenera - Aefeso 5:15.

D. Tiyenera kuonjezera kudziletsa pa changu chathu kuti tisagwe - 2 Petro 1:5,6.

E. Tiyenera kudziletsa pa chiri chonse chimene ife tichita - Miyambo 10:5; Akolose 3:23.

F. Mawu a Mulungu amati tiyenera kulamulira moyo wathu kuposa kulanda mudzi - Miyambo 16:32.

G. Mulungu amatipatsa ife mzimu wake umene umatithandiza ife kudziletsa ngati tigwirizana ndi Iye –

Agalatiya 5:22-23; 2 Timoteo 1:7.

5. Kudziletsa Unali Moyo wa Akapolo Olimba a Mulungu:

Yosefe - Genesis 39:6-12

Daniel - Daniel 1:8; 2:26-30; 6:10

Davide - 1 Samuel 24

Mose - Eksodo 34:28

Ezekieli - Ezekieli 24:15-18

Paulo - 1 Akorinto 9:12-27

Yesu - Mateyu 4:1,2; Mariko 1:35; Yohane 17:19; Luka 9:44,57; Mariko 10:32-34; Yohane 12:27,28;

Mariko 14:36; 1 Petro 2:23

6. Magawo Ofunika Kudziletsa:

Page 32: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

32

A. Maganizo.

B. Zinthu zotitenga kwambiri (monga mkwiyo, mantha, manyazi).

C. Moyo wopembeza.

D. Kusamala ntchito.

E. Ubale

F. Zochimwira

G. Ndalama

7. Njira Zothandizira Munthu Kudziletsa:

A. Onetsetsani zimene kusadziletsa kukuchita pa moyo wanu, moyo wa ena komanso kwa Ambuye,

(osatsutsa zinthu zina kapena anthu ena chifukwa cha mavuto omwe akhoza kubwera pa moyo wanu

chifukwa cha kusadziletsa kwanu). Onani chithunzi chimene kudziletsa kungabweretse pa moyo wanu.

Zimenezi zikhoza kukuthandizani ndipo cholinga ndi magwero ake enieni a moyo wodziletsa.

B. Phunzirani makhalidwe osiyana siyana omwe kudziletsa kumachititsa munthu, (chifukwa chiyani

msilikari wophunzira nkhondo amayamba kudziletsa polangizidwa? Ndi chifukwa chiyani wophunzira

amawerenga kuti alembe mayeso? Ndi chifukwa chiyani mnyamata yemwe ali m’chikondi amakonza

za tsiku lokomana ndi bwenzi lake?) Kudziletsa ndi njira yokhala ndi cholinga osati umisiri ayi.

C. Lolani chilango cha Mulungu chipangitse moyo wanu kukhala wodziletsa. Pemphani Mulungu kuti

akuthandizeni kudziletsa pa moyo wanu. Phunzirani kuzilanga nokha Mulungu asanakulangeni –

Ahebri 12:5-11; 5:8; Aroma 5:3,4; Yakobo 1:2,3; 1 Akorinto 11:31.

D. Konzani dongosolo la pa moyo wanu (kagwiritsidwe ntchito ka nthawi, zopambana, zolephera,

zokhumudwitsa ndi zina), kwa masabata atatu. Pezani moyo wosapindulitsa ndi umene kuononga

makhalidwe anu ndipo muukonze.

E. Phunzirani malamulo a kagwiritsidwe ka ntchito komanso ndalama.

F. Phunzirani malangizo a kudziletsa kumene mutha kukula nako pa moyo wauzimu (mu bukhu lomwe

mutu wake ndi “Celebration of Discipline”, Richard J. Foster anatchula kulingalira, pemphero,

kusala kudya, kuphunzira mawu a Mulungu, kufewa, kukhala pa wekha, kugonjera, utumiki, kulapa,

kupembedza, kutsogoleredwa ndi kukondwera).

G. Fufuzani msampha womwe umakulepheretsani kuyenda m’njira ndipo pezani njira ngakhale yovuta

kuti muthane ndi m’chitidwewu – Mateyu 18:8-9

E. Sankhani malo amodzi a moyo wanu omwe akusowa chilangizo ofunika kuyamba nawo. Pamene

mukuyesa kulangiza moyo wanu, mudzakula mu uzimu ndipo moyo wanu wonse udzathandizika.

Mukamalangiza moyo wanu mukhoza kukula kwambiri pa moyo wanu wa uzimu - Mariko 4:25.

Zitsanzo zina mwa zinthu zothandiza:

1) Mulungu akhale woyamba pa chuma chanu. Mwa pemphero lingalirani zopereka gawo la

chuma chanu. Mutalandira ndalama zanu, chotsani gawo lina ndipo sungani pa malo pomwe

sizingaonongeke pogulira zinthu zina ndipo perekani pamene mwayi woyamba wapezeka.

3) Pezani nthawi pa tsiku yopemphera komanso kuwerenga Baibulo. Sankhani nthawi yoti

singasokonezedwe ndi china chiri chonse. Zimenezi zikhale zoyamba ndipo chotsani zina

Page 33: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

33

zochita kuti nthawi ipezeke. Lembani ndi kuika pa galasi la malo osambira kapena pena pali

ponse kuti mukumbukire za chinthu chimenechi. Ngati mulephera kukwaniritsa pa nthawiyi,

musapite kukagona mpaka mutapemphera.

3) Ganizirani za ubale wanu ndi munthu wina umene suli bwino. Pempherani ndi kuganizira

chomwe chikulekanitsani. Ganizirani mwa malemba komanso mu mzimu wa chikondi zimene

Mulungu akufuna kuti inu muchite – Mateyu 18:15; 5:23-24; Agalatiya 6:1-2. Ngakhale ndi

zovuta, komabe yetsetsani kukomana naye munthuyo ndi kukambirana za ubale wanu.

4) Ngati muli ndi ntchito yaikulu, ya padera kapena lipoti lofunika monga pa 10 December

pafunika kuwerengera nthawi yomwe mungamalize ntchitoyo popanda kupanikizika.

Khazikitsani nthawi monga mu October ndi mu November kuti muone ngati ntchitoyo ifika

kumapeto ake, pafunika kuyetsetsa kutsatira ndondomeko yoyenera ndipo zochita zina ndi

zofunika kuzichotsa.

I. Zipanikizeni nokha kuti mukwaniritse zolinga zina zake zokhala ndi malire a nthawi zawo.

J. Khalani ndi moyo woyamba chinthu ndi kuchimaliza. Konzani nthawi yogwira ntchitoyo pa kalendala

yanu. Komanso pangani magawo a ntchito yanuyo. Konzani dongosolo lakuti gawo lakuti likhale

itatha pofika tsiku lakuti.

K. Ngati mumalephera kukwaniritsa zinthu, yambani kuchita bwino pobwereranso kuti uchite zimene

munazilepherazo. Chitani lamulo loti chinthu chofunika muyambe kuchigwira poyamba yamba. Ikani

nthawi zokhazikika kuti muchite zinthu zina mtsogolomo.

L. Chotsani zotchinjiriza zonse kuti mukomana ndi zowawa ngati mulephera kudzilamulira nokha. Mwa

chitsanzo, osamuuza munthu wina kuti akudzutseni ngati mwalephera kumva belo lanu.

M. Ziyamikireni nokha chifukwa mwapambana mu kudziletsa, koma osati mu zinthu zimene zolimbana

ndi zolinga zanu.

N. Konzani dongosolo la tsiku ndi tsiku la moyo wanu kuti ukhale wa phindu. Mwa chitsanzo, pitani

mukagone mwa changu kuti mudzazuke mofulumila tsiku linalo. Dzukani mwa changu kuti muyambe

ntchito zanu mwa changu.

O. Phunzirani miyoyo ya anthu odziletsa ndipo phatikanani nawo oterewo.

P. Phunzirani kusiyanitsa zofunika ndi zosafunika.

Q. Yetsetsani kuchita zinthu zomwe mumaziopa, ndipo mantha adzakuchokerani.

R. Osaleka kufunafuna njira zoletsera moyo wanu, chifukwa nthawi zina mudzalephera. Makhalidwe

akale samalekedwa mwachangu mpaka mutayamba makhalidwe atsopano. Tonse tiyenera kudziletsani

moyo wathu wonse.

S. Koposa zonse kulani kuyandikira Yesu. Chikondi cha pa Iye chidzakuthandizani kudziletsa koposa

china chiri chonse.

Potsiriza: Kudziletsa kumakupangitsani inu kukhala msilikali wodalirika amene sangagonje mu nthawi ya mayesero.

Kulangika kwa lero kukuthandizani kukonzekera pa zochitika za mtsogolo. Kulangika ndi gawo limodzi la kusunga

moyo.

Phunziro 8 - Kuphunzira Kulamulira Zikhumbitso Zotitenga Kwambiri -

Page 34: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

34

Malonje: Kodi mungathe :

--Kuonetsa zolinga ndi zodandaula kwa anthu mofatsa popanda kutaya zotetezera?

--Kulimba mtima kulankhula za kukhosi kwa anthu?

--Kunena kuti ayi komabe ndi kukhala wosapanikizika?

--Kusaopa za kumene zikhumbitso zanu za mphamvu zingakutsogolereni?

--Kufotokozera alendo za inu?

--Kupanikizika popanda mimba ndi mutu wanu kupweteka?

--Kukambirana ndi anthu za maganizo anu popanda kuopa za momwe angayankhire?

--Kuonetsa chikondi popanda kukhumudwa?

--Kusakhala ndi zosangalala ndi zokhumudwa pa moyo wanu?

Zotitenga mtima kwambiri zikhoza kukhala zovuta nthawi zina komabe siziri zoipa. Zinalengedwa ndi

Mulungu ngati gawo limodzi la chikhalidwe chathu ndipo Mulungu nayenso ali ndi zimene amatengedwa nazo.

Zotigwirira mtima ndi chinthu chomwe chimangitsa ife kumayenda, mtundu umene sangalatsa moyo. Zikhumbitso ndi

mphatso yaikulu kwa ife ngati tizilamulira bwino ndipo tiyenera kuzilamulira osati izo kutilamulira ife - 1 Akorinto

6:12. Zikhumbitso zosalamulidwa kapena kugwiridwa bwino zikhoza kutipuwalitsa ife ndipo zikhoza kutiononga. Ndi

zofunika kuti Mulungu azilamulira zikhumbitso zathu.

1. Zikhumbitso Zathu Zikhoza Kutithandiza Kuchita Zabwino. Mwa chitsanzo:

A. Changu chophunzitsa anthu otayika - Aroma 9:1-3; 10:1.

B. Kubweretsa mabanja pamodzi mu ukwati - Genesis 2:24; 29:18,20.

C. Kuonetsetsa kuti makolo akusamala ana awo - Yesaya 49:15.

D. Changu pogonjetsa zoipa - Yohane 2:13-17; Machitidwe 17:16,17.

E. Ntchito za chifundo - Luka 7:11-15; Mateyu 8:2,3.

2. Mavuto Ambiri Amabwera Pamene Zikhumbitso Zathu Zitilamulira Ife.

Mavuto ochitika chifukwa cha zikhumbitso zosalamulidwa:

A. Kukhumudwa - 1 Mafumu 19:1-5; 2 Akorinto 2:7.

B. Matenda a maganizo - 1 Samueli 18:6-11.

C. Matenda a thupi - Masalimo 32:3-5.

D. Kukana chikhulupiriro; kutsutsana ndi Mulungu - Machitidwe 5:17,18; Masalimo 37:1,8; 73:2,3,13-

15.

E. Mipatuko ndi kusweka kwa ubale - Miyambo 29:22.

F. Machimo a mitundu yonse, monga:

1) Madama - Genesis 37:3,4; 2 Samueli 13:1-19.

2) Kupha - Genesis 4:3-8.

3) Kudzipha - Mateyu 27:3-5.

4) Kuledzera.

5) Ziphuphu, khungu la uzimu - Mateyu 26:65.

Page 35: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

35

G. Kutayika kwa maganizo kawiri-kawiri chifukwa cha zikhumbitso zakale zosungika m’kati.

H. Matenda a m’maganizo. Mwa chitsanzo:

1) Kugonjera anthu nthawi zonse, ngakhale umamva kuwawa pa tsogolo.

2) Kumachite zonse m’malo moti mubvomerezedwe ndi anthu – mawu athu, machitidwe athu,

ngakhale zobvala zathu..

3) Kuchita za bwino, ndi kulonjeza kuchita za bwino mpaka zitakuchulukira.

4) Kuopa kunena poyera, kuopa kuzunzika kapena kukanidwa.

5) Kupewa kukhudzana kapena kuyandikana kwa maganizo poopa kupwetekana kapena

kukanidwa.

3. Mulungu Afuna ife Tizilamulira Zikhumbitso Zathu. Zimenezi ndizo mbali imodzi ya chipulumutso

chathu.

A. Tiri kulamulidwa ndi kulimbikitsidwa kuti tizilamulira zikhumbitso zathu - Yakobo 1:19,20; Aefeso

4:26,27; Afilipi 4:6,7; Miyambo 16:32.

B. Mzimu wa Mulungu umatithandiza ife kudziletsa - 2 Timoteo 1:7; Agalatiya 5:22,23.

C. Mawu a Mulungu amatipatsa nzeru kuti tigonjetse zikhumbitso zathu.

1) Kupsa mtima, kumva kuwawa:

a. Dzilamulireni mwa changu zisanakule - Aefeso 4:26,27.

b. Mwa ulere perekani ufulu wanu monga Yesu anachitira - Mateyu 16:24; Afilipi 2:7.

c. Khululukirani monga mufunira kukhululukidwa - Mateyu 6:12; Aefeso 4:32.

d. Kambiranani - Mateyu 18:15; 5:23,24.

e. Perekani kupsa mtima konse kwa Mulungu ndipo mulekereni kubwezera kukhale

kwake - Aroma 12:17-21.

2) Nkhawa ya mantha:

a. Zindikirani kukhulupirika kwa Mulungu, dziwani kuti afuna kukuthandizani - Aroma

8:31-39.

b. Phunzirani kupereka mantha anu onse kwa Iye mwa pemphero ndi kusatenganso,

ndipo mkhulupirireni ndi mtima wanu wonse - Afilipi 4:6,7; 1 Petro 5:7.

3) Manyazi, kapena kudzitsutsa:

a. Kuzindikira kuti Khristu anapereka dipo wake wa machimo athu kotheratu - Yesaya

53:4-6.

b. Kuzindikira kuti Mulungu amafuna kukukhululukirani - Masalimo 103:11-14; Luka

15:21-24.

Page 36: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

36

c. Kubvomereza kulakwa poyera, ndi kukhala ndi udindo pa zochita zanu - Yakobo

5:16.

d. Perekani kwa mwini wake zinthu zotayika - Luka 19:8,9.

e. Kubwera kwa Mulungu kutikhululukire - Machitidwe 3:19.

f. Kudzikhulukira wekha.

g. Kukhululukira ena kuti nawenso ukhululukidwe - Mateyu 6:12-15.

4. Magawo Othandiza Kuletsa Zikhumbitso Zathu:

A. Taganizirani ngati mukufunadi kumasulidwa ku mphamvu ya zikhumbitso. Anthu ena amakondwera

ndi kuzimvera chisoni, malingaliro obwezera, ndi zina zotero. Anthu ena amagwiritsa ntchito mavuto

awo a m’maganizo pokopa ena, kapena kuti akondedwe, kapena kuthawa kukhudzidwa. Ena samafuna

kutaya chizolowezi cha zikhumbitso m’malo moti amasulidwa ku ukapolo.

B. Taganizani kuti muyenera kugonjetsa zikhumbitso zanu chifukwa cha Yesu.

C. Zindikirani kuti nokha simungathe kopanda thandizo la Mulungu, motero funani mzimu wa Mulungu.

1) Pemphani mzimu - Luka 11:13; Aefeso 5:18.

2) Sungani bwino mawu a Mulungu omwe ndi lupanga la mzimu – Aefeso 6:17.

3) Yandikanani ndi anthu a Mulungu kuti muyanjane nawo, akulimbikitseni komanso

mupembedze nawo limodzi - Ahebri 10:24,25; Yohane 7:37-39.

4) Sungani thupi lanu ndi moyo wanu woyera motero kuti mzimu akondwere kukhala mwa inu -

1 Akorinto 3:16,17; 6:18-20.

D. Dzilimbikitseni nokha mwa thupi ndiponso mu uzimu kuti muthe kuusamala.

E. Onjezerani zolinga zanu kuti mudziwe chimene zikhumbitso zanu zikuchita ku moyo wanu, wa ena

ndiponso kwa Ambuye.

F. Ganizirani za mtendere, kukondwa ndi kulemekezedwa, komanso ubale wokonzeka womwe

mungakhale nawo ngati mutadziletsa pa zikhumbitso zanu.

G. Phunzirani kuchita ndi zikhumbitso zosiyana pamene zaoneka ndi pamene kuli kosavuta kuzisamala.

H. Zindikirani kuti pamene inu mulora kuti zochita za anthu zilamulire zikhumbitso zanu, muli pansi pa

ulamuliro wawo osati wanu ayi.

I. Chotsani zikhumbitso zongosungika zokhudzana ndi maganizo opweteka akale.

1) Zikhumbitso zathu za makono zichokera ku zinthu zotionekera kale. Zina mwa zinthu zomwe

zinatichitikira zinali zopweteka. Mwina tikhoza kusunga zikhumbitso zimenezi ndi kukhala

zonyala. Pamene zikhumbitso zathu zanyala, zimadzaonekanso ngati zokhumudwitsa, zaukali

ndi zodwalitsa kapena zosakhazikika, kapena kutaya mtima.

Zitsanzo za zinthu zina zotigwedeza zakale:

- Kusasamala kwa makolo

- Kusatha kwa makolo kupereka chikondi

- Kulakwa kwa makolo kotiphweteka kapena kotiyipitsa

Page 37: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

37

- Kulekana kwa makolo

- Kutaya kwa kholo kapena mmodzi pa banja

- Kuipitsidwa kapena kusautsidwa pa chigololo.

- Kutha kwa chikondi kapena kulekana

- Kugwa kwa chikhalidwe

- Kukana kowirikiza

- Luntha la uchifwamba

- Kusowa kwa zinthu zofunikira pa moyo

- Ngozi yaikulu yoononga miyoyo ya anthu kapena zinthu

2) Izi zimaoneka monga zopweteka pozikumbukira ndi kuziganizira.

3) Zikhumbitso zimenezi pamodzi ndi luntha sizinagwiridwe mu njira ya Ambuye ndi kuthana

nazo kapenanso sizinakhudzidwe mu njira imene chilengedwe chimafuna. Ziyenera

kutulutsidwa ndi kuthana nazo ndipo ziyenera kukhuzidwa mu njira ya malembo. Ziyenera

kutulutsidwa poyera ndi kuonedwa kuti zimenezi zitheke. Mwa njira imeneyi ndi pamene

zikhumbitsozi zingasiye kupereka mavuto.

- Chisoni chosagwiridwa bwino.

- Kuchita mantha kapena kugundika kosaloledwa

- Kholo losakhululukidwa

- Tchimo losabvomerezedwa ndi kuperekedwa pamaso pa Mulungu kuti uyeretsedwe

- Chiyanjano chopewedwa

Onani bukhu la mtengo wapatali lotchedwa Making Peace With Your Past, lolembedwa

ndi H. Norman Wright (Fleming H. Revell Co., Old Tappan, NJ, 1985); ndi The Healing of

Memories, lolembedwa ndi David Seamands.

6. Kuyang’ana pa Kutaya Mtima ndi Chiyembekezo (depression): (Zotengedwa ku maganizo a Dr. C.

Wayne Briggs)

A. Zoyambitsa:

1) Makhalidwe – Ndi kangati kamene inu mumachita zimene mumakonda kuchitazo?

2) Kutayika kwa zinthu zokondedwa – kutaya kwenikweni kapena kuganiza chabe, kapena

zoloseredwa.

3) Zinthu za chikhalidwe – chikhalidwe chotengera, mbiri ya banja, kusiyana kwa mankhwala

ena a m’bongo, kuchepa madzi m’thupi, hypoglycemia, kugona kosakwanira, chifuwa,

zotsatira za mankhwala, opereshoni, zochitika za chisawawa, kansala ndi zina.

4) Kuzizidwa kodza chifukwa cha kupanika - kulimbana, kugwirira, kukhuzidwa ndi umbanda,

ngozi, chisoni cha kulira maliro, ndi zina zotero.

5) Zikhulupiriro – Kuganiza kopanda chiyembekezo, kuganiza mogonja.

6) Zikhumbitso zosamasulidwa ndi kuthedwa bwino – kupsa mtima, kulakwa, chisoni, ndi zina

zotero.

7) Ubale wa munthu ndi mnzake - kusintha, kusowa, kufunika kwa kugawana kwa zikhumbitso

ndi kusamalira. Mavuto a ubale.

8) Kupanda zolinga zoyenera – kupanda zolinga, zolinga zokwaniritsidwa kale, moyo wopanda

Page 38: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

38

matanthauzo.

9) Kusakhazikika kwa umunthu – makhalidwe okhalitsa Osaganiza bwino.

10) Matenda a mu ubongo – kutaya mtima kukhoza kukhala kwachiwiri pa matenda a mu ubongo

owononga thupi lonse (Psychosis).

B. Zizindikiro za kukhumudwa kapena kutaya mtima:

1) Kukhala ndi nkhawa, kupanda chiyembekezo, kukhumudwa, kusowa mtendere, kukwiya pa

zinthu zochepa. Kupanda chidwi mu zochitachita. Mutha kupsa mtima kapena kukhala ndi

nkhawa.

2) Kugona pang’ono kapena kwambiri, kudzuka isanakwane nthawi, kapena kugona movutikira.

3) Kubvuta kulingalira, kusowa mphamvu yosankha kapena kumbukira kochepa.

4) Kusowa chidwi kapena chikondwerero m’malo a chisangalalo kapena m’zochitachita zomwe

munazikonda kale.

5) Kutopa, kuchepetsa mphamvu kapena kutopa kawiri-kawiri.

6) Kuona kusafunika, kudzipeputsa, kusakwanira, kulakwa kosayenera kapena kudzinyoza.

7) Kuchoka pa gulu.

8) Kuchepetsa ntchito, kupindula kwa kunyumba.

9) kupsa mtima kapena mkwiyo wopitirira.

10) Kusatha kubwezera ndi kuyamika kapena mphatso ndi chimwemwe.

11) Misozi, kulira kapena kufuna kulira.

12) Maganizo ofuna kufa, kukhumbira kufa, maganizo odzimangirira.

13) Maganizo odzimangirira kapena kuyerekeza kumene (ngakhale kamodzi kokha).

14) Maganizo oipa oganizira za mtsogolo, kupanda chiyembekezo, kumva chisoni chifukwa cha

moyo wako, kapena kuipidwa ndi zochitika za kale.

15) Kusintha mu chilakolako kapena mu sikelo pamene munthu sakudya mokwanira.

16) Kusachangamuka ndi kusalankhulalankhula, kusakhazikika. Mitsempha, kugwirizana kapena

kuchepetsa kulankhula kuposa kale. Kapenanso kulankhula kapena kuchita mofulumira.

17) Kuchepetsa kwa zochitika za chilakolako, (nthawi zina kuonjezera kwa zochitikazi).

18) Kuonjezera kwa kupweteka kwa thupi kapena moyo wa mavuto.

19) Kulowa pansi pa kudzikonza kwa thupi, maonekedwe, kusamala pakhomo.

Ngati munthu sakugona maola asanu ndi limodzi usiku kapena ali ndi maganizo ofuna kudzimangirira

kapena akuganiza atafa, kuthandiza mwa ukatswiri ku kufunika mwa changu. 95% ya milandu ya

kukhumudwa imatha kuchizika ngati munthuyo atathandizidwa mwa changu.

Page 39: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

39

C. Zothandiza kugonjetsa kukhumudwa:

1) Unikani bwino m’thupi, mankhwala ndi zakudya. Masewero olimbitsa thupi ndi abwino

ndipo amathandiza. Musaiwale zochitika ndi mankhwala monga, kaffeine (kofe),

kutsemphana ndi zakudya zina.

2) Chitani zolimbitsa thupi tsiku ndi tsiku ndipo khalani ndi nthawi yaikulu yopumula.

3) Chitani zinthu zimene zimakusangalatsani kuchita. Phunzirani kugwira ndi kuteteza

kupanika.

4) Kukambirana zauzimu ndi pemphero ndi kofunika; ndipo kukambirana mofatsa bwino ndi

wina yemwe angapereke maganizo oyenera nkofunika.

5) Maganizo osakonzeka bwino ndi ofunika kuthana nawo pamene munthu angathe. Ngati

kukhumudwa sikukusintha pa masabata awiri, mankhwala ndi ofunika.

Bukhu lobvomerezeka Happiness Is A Choice, lolembedwa ndi Frank B. Minirth, M.D. ndi

Paul D Meier, M.D. (Baker Book House, Grand Rapids, Michigan, 1978). Zimapezekanso pa

vidio (zisanu ndi imodzi za ola limodzi).

Phunziro 9 - Kuyamba Moyo Wodzilemekeza Wathanzi -

Mawu Oyamba: Ambiri a ife sitimadzikonda tokha. Timadzifanizira ndi ena ndipo timakhumbira titafanana nawo.

Sitimaganizira kuti anthu ena atha kutikonda kapena kutilandira – iwo angatilandire bwanji pamene pali zirema zambiri

za ife? Tiona ngati anthu amatikonda kapena ayi. Moyo wodzipeputsa ndi bvuto la anthu ambiri ndipo limayambitsa

mavuto enanso, ndi poyang’anana ndi kudzikuza. Munthu akamadziona ngati ali wabwino koposa anthu ena (Aroma

12:3), ndiye kuti “wodzikuza” ndi “wodzimva.” Koma si kawiri kawiri pamene timazindikira kuti munthu yemwe

amadandaula za moyo wake nadzipeputsa ndi “wodzimva” kapena wodzala ndi maganizo a za iye yekha. Kukhala ndi

moyo wathanzi wodzilemekeza ndi gawo lina lofunika pa ufulu wa uzimu wa mtendere ndi wofunika.

1. Kudzipeputsa Kumabweretsa Mavuto ena Monga:

A. Mantha ndi nkhawa, kusowa kudzikhulupirira.

1) Kuchita manyazi, kusatha kupanga ubale.

2) Kusatha kudzitsimikizira wekha.

3) Kusatha kupanga zinthu bwino chifukwa choopa kulephera.

B. Kumafuna kuonetsa chinthu china.

C. Mankhwala ndi kumwa mankhwala ozunguza bongo.

D. Makomo ovutika ndi kuukirana.

E. Kusatha kupereka chikondi chifukwa cha njala yopitirira ya kulandira chikondi.

F. Uhule, kutsatira makhalidwe onyansa komanso kusakhulupirika kwa pa banja pofuna

kulandiridwa.

Page 40: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

40

G. Matenda a maganizo.

2. Zoopsa Zina Zochitika Chifukwa cha Kudzipeputsa:

A. Kulola kudzipeputsa pa moyo wanga kukhale kudzichepetsa konama.

B. Kuganiza kuti chifukwa makolo anga kapena zochitika zina pa moyo wanga zinaononga

makhalidwe anga, sindingakhuzidwe pa zochita ndi zosankha zanga.

C. Kuganizira kuti kusintha pa moyo wodzilemekeza ndi kumene kungandichiritse m’mabvuto anga

onse.. Maganizo athu sungatipulumutse, koma Khristu yekha ndiye angathe.

D. Kuganizira kuti Mulungu sangandigwiritse ntchito chifukwa wotsikirapo poyerekeza ndi ena.

3. Zizindikiro zoti munthu adzipeputsa (zotengedwa kuchokera ku Institute in Basic Youth Conflicts

Textbook).

A. Kukhudzidwa ndi maonekedwe a kunja (zovala, zokometsera, zina).

B. Kuipidwa ndi zolakwa zake kapena zirema.

C. Maganizo ofuna kuti unali wina wake kapena utakhala munthu wina.

D. Kuzidzudzula wekha.

E. Kusatha kukonda ena mokwanira.

F. Manyazi opitirira.

G. Kusamalira kopitirira.

H. Kugwiritsa kwambiri ntchito ndalama, kuti ukondweretse anthu.

I. Kunyada kapena kudzionetsera.

J. Kusiya zofunikira zeni-zeni chifukwa chofunafuna zinthu zoti ziwakondweretse anthu.

K. Kukhudzidwa chifukwa chofuna kubisa zirema.

4. Zina Zimene Zimapangitsa Kudzipeputsa:

A. Zolakwa za makolo pamodzi ndi zooneka zina pa banja.

1) Kufuna zambiri kuchokera kwa ana mwa changu.

2) Kufuna zochepa.

3) Kuyerekeza molakwa.

4) Kunena kapena kunyoza zokhudza maonekedwe a mwana kapena kulephera kwake.

5) Kusasamala polankhula zimene zimatsatira kukanidwa kapena kusafunika.

6) Kukondera mwana wina pa anzake.

7) Kusowa mwambo, makhalidwe osakhazikika.

Page 41: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

41

8) Kusowa chilangizo chopitirira.

9) Chilango chosayanjanitsika.

10) Kutopa ndi kupanikizika pa nthawi – popanda nthawi ya ana.

11) Mzimu wovuta ndi woweruza.

12) Kulephera kulemekeza zochitachita zina zabwino.

13) Kulephera kuonetsa chikondi ndi kubvomerezana, ndi kumuonetsa mwanayo kuti iye ndi

wa mtengo wapatali.

B. Nyengo zina za moyo, monga:

1) Zaka za unyamata.

2) Zaka za ukulu

3) Zaka za ukalamba

C. Bodza kapena kusakwanira kwa njira zina zofalitsira uthenga mu chikhalidwe chathu, monga:

1) Kuoneka bwino kwa thupi

2) Luntha pochita masewera olimbitsa thupi

3) Nzeru

4) Chuma

5) Achinyamata

6) Mphamvu

D. Milingo yonama pofuna kulinga ubwino wa munthu..

E. Kupunduka.

F. Kutha chidwi chifukwa cha kugwiriridwa ndi kugonana mosayenera.

G. Kulekana banja.

H. Kulephera, kapena kusiya sukulu, maphunziro ndi zina.

I. Matenda a mu ubongo ndi m’maganizo.

J. Mchitidwe wodzinena wekha mosayenera. (Mwa chitsanzo: "Nthawi zonse ndimalephera zinthu

zofunika." "Palibe wina angandikhumbire." "Nidipo nditafuna kukhala ndi abwenzi, ndikudziwa

kuti adzandikana.")

5. Choonadi China Chomwe Chingatimasule ndi Kutithandiza kuti Tizidzilandira Tokha (Yohane

8:32):

A. Chikhumbo khumbo chakuti anthu adzitilandira ndi kumationa monga oyenera si cha mphamvu

kwambiri (mwina koposa chigololo). Titadziwa chikhumbo khumbo chimenechi, tikhoza

kudzilamulira tokha.

Page 42: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

42

B. Sitimadziona tokha poyera. Timaziona mosalingana ndi momwe ife tiriri.

1) Chifukwa timaganiza zoipa za ife eni, timaganiza kuti anthu ena amaganizanso motero za

ife. Nthawi zina timawerenga mawu okana mu zochita za munthu pomwe palibe.

2) Anthu ambiri samationa ife monga timadzionera tokha.

3) Anthu ambiri okongola ndi odziwika samadziona mwa njira imeneyi.

4) Anthu ambiri amadziona monga osafunika ndi opanda nzeru kusiyana ndi momwe aliri.

C. Anthu ambiri omwe inu mumawasirira ndi kuganiza kuti ndi okhazikika, ndipo ali mphatso ali ndi

chikaiko chomwe inu muli nacho.

1) Munthu yemwe mumamusirira akhoza kumakusirirani inunso.

2) Munthu yemwe mukumuopa kukomana naye akhoza kumaopa kukumana ndi inunso.

3) Mukhoza kumadandaula poganizira za zimene ena akuganiza ndipo mwina iwonso akhoza

kumadandaula chifukwa cha maganizo anu.

D. Nkosafunika kuti inu mudzilira chifukwa cha zolakwa zosakonzeka pomwe mwina mukhoza

kudzuka ndi kukhala ndi moyo wokondwa.

E. Kukhuzidwa kwa chifukwa cha kusafunika kwanu kukhoza kuchepetsa maonekedwe anu okongola

ngati munthu, ndipo ufulu ukhoza kukupangani inu kukhala wokongola.

F. Kupweteka kwa kudzichepetsa kumabweretsa khalidwe limene limaononga kudzilemekeza. Mwa

chitsanzo:

1) Munthu yemwe ali ndi sikelo yochepa amazipeputsa yekha, ndipo amadya kuti

azisangalatse yekha ndipo amaonjezera bvuto lake.

2) Munthu yemwe amaledzera kuti aiwale za kusowa mtendere kwake, amaonjezera bvuto la

kuchepa kwa ulemu wake.

3) Munthu yemwe amafuna kukondweretsa anthu, pamene ayang’ana m’mbuyo amaona kuti

wadzipusitsa yekha.

G. Kukanidwa ndi munthu kapena anthu, si chitsimikizo cha kusafunika kwanu. (Mwa njira ina,

kukanidwa ndi anthu ndi chizindikiro cha kufunika kwanu - Luka 6:26).

H. Kudzibvomereza wekha sikusonyeza kuti ulibe “zolakwa." Umadziwa zolakwa zako ndipo

umadziwanso “kupambana” kwako.

I. Umunthu ndi kukongola kwa mkati ndi kokondweretsa anthu poyerekeza ndi kukongola kwa kunja

- 1 Petro 3:3-6; Miyambo 15:30; 31:30.

J. Kudzilemekeza ndi kofunika pokhala ndi ukwati wabwino ngakhalenso pofuna ubale wabwino.

Munthu yemwe amadzikonda yekha sayenera kuyerekeza kuti akhoza kukhala wooneka. Akhoza

kulankhulana, kupereka chikondi, ndipo sasowa kabvomerezedwa kwa padera, kapena safunika

kutengedwa ngati mwana ndipo saganizira za kukanidwa.

K. Milingo ya padziko lapansi ya umunthu ya kufunika kwa munthu imakhala yonyenga ndi

yosakwanira. Tiyenera kutsegulidwa maso athu ndi Mulungu kuti tione chimene chiri chofunika -

2 Akorinto 4:4; Yohane 8:32.

Page 43: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

43

L. Ngati ife sitikondwera ndi maonekedwe athu, ndiye kuti tikudana ndi Mulungu yemwe anatilenga

ife ndi cholinga - Yesaya 45:9; Aroma 9:20; Masalimo 139:13-16; Eksodo 4:11.

M. Mulungu akhoza kulemekezedwa ndi ntchito yake kukwaniritsidwa kupyolera mu kufooka kwathu

- Aroma 8:28; Yohane 11:4; 9:1-3; 2 Akorinto 12:7-10.

N. Mavuto athu akhoza kutisintha ife kukhala anthu wokonzeka, angwiro - 1 Akorinto 11:28-33;

Ahebri 5:8; Aroma 5:3,4.

O. Kufanizira moyo wathu ndi wa ena ndi kupusa. Ndi kufunika kwathu pamaso pa Mulungu

kumene kuli ndi ntchito - 2 Akorinto 10:12; Aroma 2:29b; Yohane 5:44.

P. Mulungu amafuna kukongola kwa mkati - 1 Samueli 16:7; 1 Petro 3:3,4; Mateyu 5:3-11;

Agalatiya 5:22,23; Masalimo 29:2.

Q. Ndinapangidwa mu chifanizo cha Mulungu - Genesis 1:26,27 – ndipo ndi kupangidwanso

ngakhale ndinachimwa - Akolose 3:10; Yesaya 61:3; Aefeso 2:10. "Mulungu sanamalize ntchito

yake ya pa ine tsopano."

R. Moyo weni-weni si kukhala ndi chuma ayi - Luka 12:15.

S. Moyo ndi wofunika chifukwa Yesu amakhala mwa ine - Agalatiya 2:20; 4:19.

T. Tidzapangidwa okongola ngati Yesu - 1 Yohane 3:1,2.

U. Yesu anali ndi zifukwa zambiri pa moyo wa dziko lapansi zimene zikanampangitsa Iye kuona

kusafunika koma sanatero - Yesaya 53:2,3; Mateyu 13:53-58; Yohane 7:5; Marko 3:21; John

1:46; Luka 9:58; Agalatiya 3:13.

V. Ambiri mwa atumiki otchuka a Mulungu anali ndi zolakwa kapena mavuto omwe

akanawapangitsa kukanidwa:

1) Yosefe - Genesis 37:3-36; 39:20

2) Yakobo - Genesis 32:30,31

3) Elisa - 2 Mafumu 2:23

4) Yefita - Oweruza 11:1

5) Gideoni - Oweruza 6:15

6) Mose - Machitidwe 7:23-29; Eksodo 4:10

7) Paulo - 2 Akorinto 12:7-9; 10:10

8) Zakeyu - Luka 19:2,3

9) Timoteo - 1 Timoteo 5:23

W. Palibe chiwalo cha thupi la Khristu chimene chiri ndi mphatso zonse - 1 Akorinto 12:4-31; Aroma

12:4-8.

1) Chiwalo china sichiyenera kuchita nsanje ndi mphatso za chiwalo chinzake - 1 Akorinto

12:14-18.

Page 44: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

44

2) Palibe chiwalo chomwe ndi chosafunika - 1 Akorinto 12:21-26.

3) Ziwalo zomwe zimaoneka ngati zopanda ulemu zimenezi ziri ndi ulemu woposa kwa

Mulungu - 1 Akorinto 12:22-24.

4) Popeza mphatso zimaperekedwa ndi Ambuye monga mwa nzeru ndi chifuniro chake,

sikuyenera kumfunsa chifukwa sanandipatse ine mphatso ina - 1 Akorinto 12:11,18.

X. Mulungu sanyozetsa munthu chifukwa cha zaka, mtundu, umuna kapena ukazi, umphawi,

umasiye, kupunduka, ndi zina. - 2 Akorinto 4:16; Miyambo 16:31; Agalatiya 3:28; Masalimo

72:12; 68:5.

Y. Munthu wina aliyense ndi wofunika chifukwa ndi m’modzi yekha.

Z. Chofunika kwambiri ndi chakuti, Mulungu amaona munthu wina ali yense monga wofunikira.

1) Anapereka mwana wake kuti adzatiombole ife - Yohane 3:16; Aroma 5:8. Akanakhoza

kuchita zimenezi kukanakhala kuti munali inu nokha pa dziko lapansi pano - Mateyu

18:10-14.

2) Mulungu amakhuzidwa ndi aliyense wa ife ndipo amatikonda - Luka 12:6,7; 1 Petro 5:7;

Luka 12:32; Yohane 13:1; Luka 22:14,15; 2 Petro 3:9.

3) Mulungu amafuna ubale wathu, ndipo ndi wofunika nkuona timamutchula “Atate” -

Eksodo 33:11; Yakobo 2:23; Yohane 15:15; 2 Akorinto 6:17,18.

4) Mulungu amafuna kuthandiza kufooka kwathu, kuombola ndi kusintha munthu wina ali

yense - Agalatiya 4:19.

5) Mulungu amafuna kutipatsa ife chiri chonse chomwe timapempha - Mateyu 7:7-11.

6) Mulungu amatilandira ife ngakhale timalephera monga kholo lokonda mwana wake

limachitira - Luka 15:11-32.

7) Mulungu amakufunani ndi kukuitanani kuti mukhale wake. Ali ndi cholinga pa moyo

wanu. Palibe moyo, ngakhale wabwinja umene sungapangidwe kukhala wangwiro ngati

utagonjera kwa Mulungu - Yesaya 1:18; 2 Akorinto 5:17; Yohane 1:12.

6. Sitepe zina Zofikira Moyo Wathanzi Wodzilemekeza:

A. Phunzirani muyezo wofunikira kwa Mulungu, ndipo musadziyese nokha ndi miyezo ya dziko

lapansi yosakwanira.

B. Onjezerani ku kudziletsa kwanu. Kudziletsa kufanana ndi kudzilemekeza.

1) Ikani zitsanzo zabwino. Khazikitsani zolinga.

2) Ikani zinthu zina zokuthandizani kukumbukira makhalidwe anu atsopano ndipo Konzani

moyo wanu kuti uziyenda molingana ndi zolinga zanu zopambana zimene ziri za bwino.

3) Yambani moyo wolongosoka:

a. Nthawi yopita kukagona ndi nthawi yodzukira.

b. Gwirani ntchito musanasewele.

Page 45: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

45

c. Zochita zanu zikhale zolingana.

d. Malo a china chirichonse ndi china chirichonse pa malo pake.

e. Kudzilamulira.

f. Ikani nthawi ya padera yoti mukwaniritse zolinga zanu.

C. Dzikhululukireni nokha monga momwe Mulungu amakukhululukirani. Bvomerezani zomwe

Mulungu anachita chifukwa cha machimo anu. Dobisoni anati, "Pangani ubwenzi ndi moyo

wanu." Ndi kwabwino kuti ndine munthu- Masalimo 103:8-14.

D. Konzani zolakwika zokonzeka (monga kakonzedwe ka tsitsi, khungu, bvuto la malankhulidwe,

mano, kulemera kwa sikelo, maonekedwe a nkhope, mayendedwe, kasamalidwe ka zovala,

chidziwitso ndi zina.).

E. Funani njira zotumikira nazo Mulungu kupyolera mu zolakwa zanu zosasinthika - 2 Akorinto

12:7-10. Zimenezi zikhoza kusintha momwe mumaonera zinthu.

F. Pangani zinthu zomwe mungathe kuchita bwino. Maganizo anu a kukwaniritsa zinthu

adzakuthandizani.

G. Tumikirani anthu ena ndipo ziperekeni ku utumiki. Chikondwerero chomwe mungakhale nacho

poona Khristu akukhazikika mwa ena ndi kusanthulika kwa miyoyo yawo, chikhoza kukusinthani

moyo wanu ndi zomwe mumaganiza - Aroma 15:1-3. Moyo wodzadzidwa ndi Chiombolo cha

mtumiki wa Khristu ndi wabwino.

H. Yang’anani pa zokhoza zanu osati pa zolephera zokha ayi. Pezani nthawi ndipo lembani zokhoza

zanu zonse.

I. Lemekezani makolo anu monga momwe malembo anenera. Ndipo muzadzilemekeza nokha

kwambiri.

J. Osaleka kuchita zinthu zimene munaziyamba, ngati kungatheke.

K. Siyani kuyankhula koipa ndi kuononga. Mwa chitsanzo: "Palibe chomwe ndimakhoza. Palibe

yemwe amandikonda. Aliyense amaganizira tchimo langa akandiona. Kuti ndiyankhule ndi anthu

ndikudziwa kuti ndikhoza kulankhula zoipa."

Zifunseni nokha ngati pali umboni wa zinthu zimene mumadziuza nokha. Ganizirani kuti

choonadi chingakhale chotani. Chotsani mawu odzipeputsa ndipo muikepo mawu odzilimbikitsa.

Ziuzeni nokha kuti ndinu wofunika ndi kuti mukhoza, ndipo muli ndi mphatso monga wina ali

yense. Muoneni Yesu akuonetsa chikondi ndi kuyamikira kwake kwa inu (zimenezi si

zongoganizira chifukwa amachitadi).

L. Mwamuna ndi mkazi ayenera kulimbikitsana monga momwe ankachitira ali pa ubwenzi.

M. Chitani zomwe ziri zoona ndipo thawani machimo, ndipo muzadzilemekeza nokha.

N. Gwirizanani ndi Mulungu pokonza moyo wanu wa m’katimo kukhala wokonzeka - Agalatiya

5:22,23.

O. Nthawi yambiri iperekedwe poyanjana ndi anthu a m’banja la Mulungu, amene amakonda ndi

kulandila anzawo.

Page 46: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

46

P. Zioneni nokha m’maso a Mulungu.

Potsiriza: Mukamadzikonda nokha kokwanira, mukhoza kudziiwala nokha ndipo mudzayamba kuganizira za ena

ndi zovuta zawo. Ndipo mudzakhoza kuchita zinthu molimba mtima chinsinsi chifukwa cha Khristu.

PHUNZIRO 10 - KUCHITA MOYENERA NDI A ULAMULIRO

Mawu oyamba: Kodi Mulungu, pamodzi ndi aulamuliro ake omwe Iye adawasankha, angakhale ndi mphamvu

yondilangiza ine momwe ndingamakhalire? Ichi ndi chinthu chofunika choyamba chomwe munthu aliyense ayenera

kuchiunika asanayambe usinkhu wa mu Chikhristu chake. Kugalukira pamodzi ndi moyo wofuna kukhala womasuka

ndi gawo lomwe ambiri a ife timalimbana nalo m’moyo wathu wofooka. Limeneli ndi tchimo lomwe mkati mwake

mumatulukanso machimo ena ambiri. Khumbo lofuna kukhala womasuka kuchoka kwa Mulungu ndi lomwe linagwetsa

Satana ndi makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava. Nkhani yomvera aulamuliro imalowa magawo onse m'moyo

mwathu ndipo limakhudzana ndi kukondwera kwathu, momwe tingakhalire bwino ndi chipulumutso chathu.

“Nditha kuchita chomwe ndifuna.” “Palibe yemwe angandiuze chochita” “Ndisiyeni ndichite zofuna zanga.” Izi

zikuonetsa malingaliro a anthu ambiri omwe ali m’gulu lofunafuna kukhala pa okha osalamulidwa ndi wina aliyense

koma okha. Kukwiyira aulamuliro, kuganiza kuti nchanzeru kuchita zinthu mozembera, kunyoza ndi kupusitsa anthu

ochita zovomerezeka ndi khalidwe la umunthu, zikupangitsa kuti Akhristu azimva kuwawa lero. Mkhristu ayenera

kumakhala wolimba mtima ndi wokonzeka kuoneka mosiyana ndi ena onse. Potsata Yesu, tiyenera kuvomera mphamvu

za Mulungu kuti tilamulidwe naye, kuti tichotse timakhalidwe tina ndi tina totsalira ta moyo wogalukira. Kukula

kumayamba ndi mtima wosweka, wogonja ndi wodzichepetsa pamaso pa chifuniro cha Mulungu: Masalmo 51:17;

Mateyu 18:3-4.

Pamene takonza bwino za kudzipereka ndi kudzichepetsa kwathu kwa akulu olamulira, kupambana kosiyanasiyana

kumatiyandikira.

1. Mphamvu ndi ulamuliro wonse umayambira kwa Mulungu – 1 Timoteo 6:15; 2 Mbiri 20:6; Yesaya 44:6;

Mateyu 4:10; Danieli 4:17; 1 Petro 5:6.

2. Mulungu anakhazikitsa maulamuliro ena ochepera mphamvu a padziko lapansi pano. Aroma 13:1

A. Makolo: Aefeso 6:1-3; Akolose 3:20

B. Mwamuna monga mutu wa banja: Aefeso 5:22; Akolose 3:18.

C. Aphunzitsi: Miyambo 5:13.

D. Anthu achikulire: 1 Petro 5:5a

E. Atsogoleri a mpingo: Ahebri 13:17; 1 Timoteo 5:17; 1 Atesalonika 5:12-13.

F. Oyang’anira ntchito zina: Aefeso 6:5; Akolose 3:22.

G. Olamulira boma: Aroma 13:1-7; 1 Petro 2:13-17; Tito 3:1-2.

3. Kukana Kumvera Ulamuliro Wokhazikitsidwa ndi Mulungu kuli chimodzimodzi ndi kukana kumvera

Mulungu. Aroma 13:2; Mateyu 10:40.

A. Timamvera aulamuliro okhazikitsidwa ndi Mulungu osati pokhapokha pamene iwo ali ochita zabwino

pokha ayi, koma chifukwa cha lamulo “la kumvera aulamuliro.” 1 Petro 2:18; Mateyu 23:1-2.

1.) Iwo omwe ali ndi mphamvu zotilamula ife, ayenera kulamula mwa kumvera Mulungu komanso

monga otumikira iwo amene awalamulirawo. Komabe kaya amatsata zimenezi, kaya satsata, izi

sizingathe kusintha lamulo limeneli lomvera ndi kugonjera. Tafanizirani ndi 1 Petro 3:1-2.

B. Pamene aulamuliro a dziko lapansi ali ofunikira kudzudzulidwa:

Page 47: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

47

1.) Musataye lingaliro ndi mtima wanu wa ulemu ndi kudzichepetsa.

2.) Mutenge ndi kuyang’ana cholakwa chakecho pamodzi naye mosamala malamulo

komanso mwa ulemu wonse.

3.) Yesani kudandaulira ndi kupempha kwa akulu ake a munthuyo ngati nkofunika koma izi

zichitike mutayamba mwakomana naye munthuyo maso ndi maso. Mateyu 18:15-17.

4.) Pempherani kwa Mulungu yemwe angathe kuchita naye – Miyambo 21:1

C. Ngati aulamuliro wa dziko aonetsa kutsutsana ndi Mulungu poyera pa lamulo lina, tiyeni tikumbukire

kumvera Mulungu wathu. Machitidwe 4:19; 5:29.

(Chenjedzo: Khalani odzipereka ndi odzichepetsa m’malingaliro ndi makhalidwe m’zonse. Kulakwitsa

kwa olamulira dziko kusatipatse ife chilolezo choti tiukire. Kupitiriza kupereka ulemu ndi kumvera

m’zonse kungathandize kupereka mwayi woti wolakwayo athandizidwe, komanso kuti ife tikhale

otetezeka.)

4. Kugalukira Kumaononga Anthu -

A. Mulungu amadana ndi kugalukira 1 Samueli 13:27-30; Deuteronomo 21:18-20

B. Mulungu amalanga ogalukira ndi osapereka ulemu – Numeri 16:1-35; 1 Samueli 15:10-23; 2 Mafumu

2:23-24.

C. Pamene tiukira olamulira, pomwepo timakhala ngati Satana, monga chigawenga choyamba ndi

chodziwika. Yesaya 14:12-14.

D. Adamu ndi Hava adalephera nachimwa chifukwa anafuna kuti akhale ngati milungu. (kumasuka

kuchoka kwa Mulungu weniweni) Genesis 3:4-6.

E. Mulungu samathandiza onyada, koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa ndi aulemu. Yakobo 4:6

F. Kukana kumvera akulu aulamuliro kwathu kumapangitsa anthu kuti anyoze Mulungu ndi chiphunzitso

chake. 1 Timoteo 6:1

G. Kusamvera ndi kugalukira kwathu ku ulamuliro woikika kumatichotsa ife ku chitetezo cha Mulungu

ndipo timakhala osatetezedwa ku ukapolo wa Satana.

H. Kugalukira kwa njira imodzi kumabalanso kugalukira ku njira ina mu moyo wathu. Ngati munthu

agalukira makolo, ndiye kuti amaukiranso aphunzitsi, akulu ampingo, olamulira dziko ndi Mulungu.

I. Kugalukira kwanga kumachititsa kuti enanso aukire. Luka 17:1-2

J. Nthawi zambiri kupanda chikhulupiriro, kumachokera pa kupanda chidwi chofuna kukhala pansi pa

ulamuliro wa Mulungu.

K. Kukhala ndi moyo womangopitiriza kugalukira kumapangitsa munthu kuonongeka – Miyambo 29:1

Lamulo iri la uzimu liri chimodzimodzi ndi malamulo a chilengedwe cha dziko lapansi.

5. Kumvera ndi kudzipereka kumabweretsa moyo wabwino ndi chisangalalo.

A. Kwa iwo akumvera, zawo zimayenda bwino - Deuteronomo 5:29; Aefeso 6:1-3.

B. Mchitidwe wachifundo ndi wofuna kumvera umamkondweretsa Mulungu – 1 Petro 3:3-6.

Page 48: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

48

C. Kumvera pamene udakali wamng’ono kumathandiza pamoyo wa munthu wonse mpaka atakula – Maliro

3:27; Miyambo 22:6; Luka 2:51-52.

D. Kumvera kumatitengera ife ku ufumu wa Mulungu – Mateyu 18:3-4.

E. Pamene timvera aulamuliro tiri ngati Yesu - Luka 2:51-52; Mateyu 17:24-27; Yohane 5:30; Luka

22:41-42; Ahebri 5:8.

F. Tiri ndi ulamuliro ngati tikhala pansi pa ulamuliro (potumikira) Mateyu 8:9; 20:25-28.

G. Kudzipereka kwathu kwa iwo otilamulira ife mwa Mulungu sikutanthauza kuti tiyiwale udindo wathu

wa umunthu pa chisankho monga zichitikira ndi enawo. Ichi sichabwino.

6. Zoona Zina za Ulamuliro ndi Kumvera

A. Kugalukira kungathe kuchokera ku kunyada, pa kukhulupirira bodza za otilamulira, ndi kwa munthu

wobvulazidwa, wokhala ndi mzimu wowawa – Genesis 3:4-5; Ahebri 12:15. Kwa ambiri, kugalukira

kudayamba powawidwa mtima ndi kumenya makolo awo.

B. Kumvera kwenikweni kuyenera kumayambira mkati mwa mtima ndi m’maganizo athu – 2 Akorinto

10:3-5; Aroma 6:17; Mateyu 5:20-22,27,28.

C. Ngati ndiribe chikhulupiriro choti chinthu china chiri choncho chifukwa cha chifuniro cha Mulungu,

kuchichita chinthucho ndi uchimo kwa ine – Aroma 14:23. Chomodzimodzi ngati ndikhulupirira kuti

chilipo chinthu china chomwe Mulungu afuna kuti ndichite koma ine osachita chimenecho, limeneli ndi

tchimo kwa ine. Yakobo 4:17

D. Munthu atha kukhala wotakataka ndi chipembedzo koma pomwe asali womvera Mulungu ndi

aulamuliro – Mateyu 15:8-9; 7:21; 23:23-24.

E. Nsembe yomwe Mulungu amaifuna poyamba ndiyo mtima wosweka, wogonja ndi womvera – Masalmo

51:16-17; Yakobo 4:4-10; 1 Samueli 15:22.

F. Kumvera Mulungu sikutanthauza kuziyika pa ukapolo kapena kudzichotsera khalidwe lako lobadwa

nalo laufulu wako monga munthu. Zoona ndi zoti umenewu ndi ufulu wokhala munthu weniweni

wamphumphu. Mkhristu amamvera chifukwa iye wasankha kutero. Iye adakalibe munthu ndipo akhoza

kudzifotokoza yekha monga munthu makamaka poonetsetsa kuti achite zimenezi mwa ulemu.

G. Kumvera, osati kugalukira ndi chidzindikiro cha kukhwima. Aliyense angathe kugalukira ndi kumenya

kaya kukana ulamuliro. Sionse ali ndi nzeru, mphamvu ndi kudziletsa kuti akhale omvera.

7. Magawo Othandiza pa Kumvera

A. Khalani ndi chidziwitso ndi cholinga chabwino pa za Mulungu. J.P. Phillips analemba bukhu lotchedwa,

Mulungu wanu ndi wochepachepa, (Your God Is Too Small). Pamene muyamba kuona ulemerero wake,

nzeru, ukulu ndi ubwino, ulemu ndi kumvera kumakula.

Kumbukirani: Chidziwitso ndi cholinga chathu cha pa Mulungu zimayenda mofanana ndi momwe

timawaganizira makolo athu, makamaka atate athu. Ngati ubale pakati panu ndi bambo wanu sunali

bwino, ndiye kuti umu ndi momwenso adzakhalire maganizo anu pa Mulungu. Muyenera kumasula

maganizo anu pa Mulungu, kuchokera ku zolakwika zomwe zimadza chifukwa choganizira momwe

atate anu, makolo anu kapena ena onse aulamuliro amakuchitirani pano pa dziko.

B. Konzani zolakwika pakati pa inu ndi makolo anu. Lapani uchimo wonse wogalukira ndi wakusamvera.

Page 49: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

49

Ubale umenewu ndiwo umakhala chiyambi cha ubale wonse wa kwa aulamuliro, makolo anu,

maulamuliro adzakukumbutsani za makolo anu ndipo mudzavutana nawonso. Ngakhale makolo anu

anamwalira kapena ali kutali koti simungathe kufikako mutha kulapa kwa Mulungu chifukwa chokhala

ndi maganizo olakwika amakolo anuwo.

C. Chotsani maganizo abodza adziko lapansi, onena kuti kumvera ndi kulemekeza aulamuliro ndi kwa

chabe. Siyani maganizo abodza ndi kutenga oona okha.

1) Zolembedwa ndi atolankhani a nyuzi ndinso chikhalidwe chathu chimakondwera ndi khalidwe

logalukira.

2) Zindikirani kuti zomwe timaona ngati “ufulu wopanda malire” sizenizeni ayi..

3. Zindikirani kuti kumvera a ulamuliro ndiwo maziko a mtendere, bata ndi kukhala mosangalala.

D. Dziwani kuti kugalukira kuli ndi mizimu yake yomwe tsinde lake liri mu moyo wathu wakale, wathupi

wa machimo. Zimenezi zimatsatira zija za Adamu ndi Satana. Kumvera ulamuliro kuli ngati gawo lija

lomwe linapezeka pamene munthu “apachika umunthu wake wakale.” Aroma 6:6-14. Lapani ndi kusiya

moyo wanu wonse wakugalukira wosafuna kulamulidwa ndi wina aliyense.

E. Onetsetsani bwino pa za ubale wanu ndi za a ulamuliro kuti muone ngati pali zizindikiro zoti mwina

muli ndi maganizo a kugalukira, kunyoza ndi kukana kuwamvera kapena chipongwe.

Mwa chitsanzo:

1) Kwa makolo:

< Ku wa zembera.

< kuwatenga ngati otivutitsa.

< Kungomvera pang’ono.

< Kukhala wopanda nawo nthawi ndi ntchito

< Kusayeserera kukondweretsa ena.

< Kuba, ndinso kumangoseweretsa katundu wa eni ntchito monga galimoto, njinga, ndi zina

zotere.

< Kunyoza zikhulupiriro zawo potsatira nyimbo zachabe, malaya osayenera kapena abwenzi

achabe.

2.) Kwa mwamuna wa m’banja:

< kusungira kuwawidwa mumtima m’malo molumikizana.

< Kudelera udindo wake wolangiza ana ake kuti asunge mwambo.

< Kumdzudzula kwa ana kapena pamaso pa anthu ena.

< Kumkana kumbali ya kugonana monga njira yomulanga kapena yomlamula.

< Kumupangitsa kuti asinthe mfundo zake kudzera mu zochitika monga matenda amthupi

ndi m’maganizo koma monyenga.

3.) Kwa aphunzitsi:

< Kusakhala wokonzeka kokwanira pomvetsera, kuchita zomwe zikukondweretsani.

< Kugwira ntchito yomwe aphunzitsi apereka mosakwanira.

< Kumangochedwabe ku kalasi.

< Mafunso ongofunsidwa ndi cholinga chofuna kusokoneza.

< Khalidwe losamvetsera ndi losalongosoka.

4.) Kwa atsogoleri a mpingo:

< Kuwadzudzula kumbali m’malo mokambirana nawo maso ndi maso.

< Kupereka uphungu kwa anthu wowapangitsa kuchita mosiyana ndi pempho la

Page 50: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

50

atsogoleri.

< Kuwakola atsogoleri ndi mafunso osakhulupirika.

< Kumangoyang’ana zolakwa zokha za atsogoleri, kuiwala kuthokoza pa zabwino

zawo.

< Kusavomereza akawaitana kuti achite nawo.

5.) Kwa mabwana/oyang’anira ntchito

< Kuchita zopusa pamene palibe akuyang’anirani

< Ntchito yogwiridwa mosakwanira yosalongosoka.

< Kuchedwa.

< Kunamizira kudwala koma usakudwala.

< Kuwaneneza monyoza.

< Kudzudzula akuyang’anirani pamene bvuto ndi lanu.

< Kusayeserera kukondweretsa ena.

< Kuba, komanso kugwiritsa ntchito katundu ndi zida za pantchito popanda chilolezo.

6.) Kwa aulamuliro a boma:

< Kusasamala malamulo a pa msewu chifukwa palibe wina yemwe akukuonani.

< Chinyengo popereka za msonkho.

< Kusasamalira malamulo.

< Kunyozera, kudzudzula mwa chipongwe popanda ulemu.

F. Pamene muona nkhani yokhudzana ndi kumvera ikubwera, bvomerani ndipo mverani mosavutika.

Nthawi zonse pamene muchita zimenezi, chizolowezi chokonda kumvera kwa aulamuliro

chimalimbikitsidwa.

G. Pezani njira zokhazikika zoti muzichita nako kumvera ndi ulemu.

H. Sankhani kumvera mokondwera, mwa chisomo chabwino. Ichi ndi chisankho chomwe muli nacho.

I. Monga momwe mungathere, yesetsani kupewa kuyanjana ndi anthu okhala ndi mtima wokonda

kugalukira nthawi zonse. Ogalukirawa, monga zigawenga, amakonda kupeza anzawo ndi

kumalimbikitsana nawo.

J. Mudzifufuze nokha kuti mutulukire ngati maonekedwe, zochitachita ndi khalidwe la moyo wanu

lionetsa kuti ndinu wogalukira kwa mumtima. Chotsani zonsezi, koma zindikirani kuti ganizo

lenilenilo la mkatilo ndilo loyenera kuthana nalo.

K. Siyani moyo wogalukira pa ndime iriyonse yomwe mwafika, ndipo londolaninso njira yanu

yokuthandizani kubwezeretsa maubale. Onani magawo a kugalukira (olembedwa ndi Gothard) awa:

1) Kusalumikizana.

2) Kusayamika, kuganizira kwambiri pa zotikhumudwitsa koposa zabwino zomwe

talandira.

3) Unkhutukumve (kusamva, kukanirira zolakwika).

4) Kuyeretsa choipa ngati chabwino.

5) Kuweruza ena.

6) Mukaona zoopsa zimenezi, bwererani!

Mawu otsiriza: Mulungu, pamodzi ndi iwo omwe iye anawasankha ali ndi udindo ndi mphamvu yotilangiza ife

momwe tingamakhalire. Ichi chiyenera kukhala chinthu chosangalatsa, chifukwa Mulungu amangotifunira zabwino

ndi zaufulu zokha. Kugalukira moyo wathu. Pali mankhwala amodzi okha ochizira kugalukira, ndiwo kulapa basi.

Pamene moyo wathu wa unkhutukumve watha, ndipo tiri okonzeka kumvera; pamene cholinga m'moyo wathu chiri

kukondweretsa Mulungu, pamenepo ndiye kuti tikuyamba tsopano kukhala ndi moyo!

Page 51: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

51

PHUNZIRO 11 - Kupanga Chisankho, Kukhazikitsa Zolinga

Mawu oyamba: Munthu wosakhwima m’maganizo nthawi zonse amafuna kuti “akhale naye keke wake komanso

kumudya.” Amafuna kumudya, koma ngati adya, ndiye kuti sakhala nayenso kekeyo. Iye amafuna kuti asunge keke

wakeyo, koma ngati atero, ndiye sangamudyenso kekeyo. Simuyenera kulowerera moyo wosuta chamba ndikumwa

mankhwala oledzeretsa kapena kuchita zosutsana ndi umunthu ndipo kenako ndikuononga moyo wanu. Chomwe

muyenera kuchita ndicho chokhala ndi zokhumba zosiyanasiyana ndi kumafuna kuzikwaniritsa zonse ngakhale ziri

zotsutsana zokha, ndi kumalephera kusankha njira imodzi ya m’moyo wanu. Popanda zolinga ndi maganizo a

masankhidwe abwino, mumangoyenda popanda cholinga chenicheni ndipo mumangokwaniritsa zochepa chabe.

Ndipo nthawi imangotayika.

Munthu wokhwima maganizo amakhala wokonzeka kutaya keke wake ndi cholinga chake choti adye kekeyo. Iye

amalolera kupereka kapena kuononga zolinga zazing’onozing’ono ndi cholinga choti afikire ndi kukwaniritsa

zolinga zazikulu zikulu. Ndipo pamene wapanga chisankho chomaliza cha zolinga zenizeni zomwe afuna kuchita,

ndi pamene amatha tsopano kuyenda molunjika ndi molondola kuloza kuzolinga zakezo.

Chikhalidwe chathu chamakono sichinathe kutipanga kuti tikhale okonzekera dongosolo limeneli. Takhala anthu

oonongeka, ochita zomwe tifuna ndi cholinga chofuna kukwaniritsa zilakolako zathu zonse nthawi imodzi. Kusunga

mwambo sikulinso monga imodzi mwa mfundo zathu zofunika kwambiri. Kuganizira kwambiri za chitetezo chathu

ndinso kuchita bwino m'moyo wathu wa tsiku ndi tsiku kwadetsa maso athu. Sitidziwa kuti tiri pa nkhondo yofuna

kupulumutsa uzimu wathu. Munkhondo, zisankho zikhale zomveka bwino.

1. Kukayikira pa Zolinga Zathu Zotsutsana Kumatifooketsa ndi Kutionongera Mwayi Wosiyanasiyana Wamtengo

Wapatali. Tikutsimikiziridwa ndi Mulungu kuti Tichite Chisankho Chathu ndi Kumtumikira Iye.

A. Eliya anawatsimikizira Aisrayeli kuti asankhe – 1 Mafumu 18:21.

B. Yoswa anawatsimikizira Aisrayeli nati, “Koma ine ndi a m'nyumba mwanga tidzatumikira Ambuye” -

Yoswa 24:15.

C. Mose anawayalira anthu njira zosiyanasiyana za moyo ndi imfa – Deuteronomo 30:15.

D. Yesu anamutsimikizira wachuma wachinyamata kuti aike Mulungu patsogolo osati chuma - Mateyu

19:16-26.

E. Yakobo akutichenjeza ife zokhala ndi mitima iwiri – Yakobo 1:6-8; 4:4-10.

F. Aisrayeli anayeserera kutumikira Mulungu ndi mafano panthawi imodzi ndipo anaonongedwa –

2 Mafumu 17:33,41; Zephaniya 1:5.

G. Akorinto anayenera kusankha pakati pa chikho cha Ambuye ndi chikho cha ziwanda – 1 Akorinto

10:14-22.

2. Antchito Opambana a Mulungu Amadziwa Chomwe ali ndi Chomwe iwo Akhalira.

A. Yesaya – “Ndine pano, nditumizeni” – Yesaya 6:8.

B Ezara anadzipereka ku kuphunzira, kuonera ndi kuphunzitsa malamulo a Mulungu kwa Aisraeli –

Ezara 7:10.

C. Nehemiya anakonzekera kumanganso zipupa za Yerusalemu – Nehemiya 1:2,3; 2:5.

D. Mariya wa ku Betaniya anasankha kumvetsera pamene Yesu anali kuphunzitsa – Luka 10:38-42.

E. Asodzi anayi aja anasiya ntchito yawo ya usodzi panthawi yomweyo yomwe kunafunika kutero ndi

Page 52: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

52

kutsata Yesu nakhala asodzi a anthu. – Mateyu 4:18-22.

F. Yosefe anathawa kuchokera m’nyumba muja m’malo mogonjera kukunyengedwa ndi mkazi wa Potifala –

Genesis 39:6-12.

G. Zolinga za Paulo pamoyo wake zinali zotengera unyinji, monga kukadathekera, kwa Khristu, kulalikira

zokha za mtanda, kulandira Yesu, kumdziwa iye, ndi kulowa naye mu msautso wake ndi kuuka kwake –

1 Akorinto 9:19; 2:1,2; Afilipi 3:7-14.

3. Yesu Ndiye Chitsanzo Chathu Chopambana pa za Kupanga Chisankho ndi Kukhazikitsa Zolinga.

A. Kumwambako, Yesu asanabadwe pano pa dziko lapansi anakonzekera ndi kupanga chisankho chopita

ku dziko lapansi lino kukudzachita cholinga cha Mulungu pokhala nsembe ya machimo athu –Ahebri

10:5-7.

B. Ali pa msinkhu wa zaka khumi ndi ziwiri (12) za kubadwa, Yesu anafuna kukhala m’nyumba ya Atate

wake kuchita ntchito yake. Luka 2:41,42,49.

C. Anatsimikizira kuti nabatizidwe kuti ayambe utumiki wake, ndi kupewa zochitika zina zosakhala

m’cholinga chake zomwe Satana anapereka pa nthawi ya mayesero ake ija – Mateyu 3:13-17; 4:1-10.

D. Yesu anali wozindikira bwino za cholinga chake m’moyo wake ndi utumiki wake – Luka 4:18-21;

19:10.

E. Nthawi zonse anali kuunikira za kuchita cholinga cha Mulungu, kutsiriza bwino ntchito yake

ndi kupita pamtanda womwe unakonzedwera iye – Yohane 6:38; 4:34; 9:4; Mateyu 20:28; 16:21;

Luka 12:50; Yohane 12:27.

F. Iye anadziyeretsa kuti nawonso omtsatira ake akhale ndi miyoyo yoyeretsedwa – Yohane 17:19.

G. Pamene nthawi yopita ku Yerusalemu ndi ku mtanda inakwana, iye “anazitsimikizira kukonzeka

kuloza nkhope yake” kupita ku Yerusalemu – Luka 9:51.

H. Poti mwina angayesedwe ndi lingaliro lofuna kubwerera m’mbuyo kapena kusintha maganizo, iye

anayenda patsogolo pa khamulo – Marko 10:32.

I. Ngakhale anali nacho chithunzithunzi cha mazunzo a mtanda m’munda wa Getsemane, iye anasungabe

mfundo yake yomangika yochita cholinga cha Mulungu – Marko 14:36.

4. Nkofunika Kwambiri Kukhala ndi Zolinga ZOYENERA za Moyo Wanu. Zolinga Zosayenera

Zimakupangitsani kuti Mutaye Moyo Wanu.

A. Cholinga choyamba komanso chopambana kwambiri kwa Mkhristu aliyense chidzikhala kukweza

ulemerero wa Mulungu kwakukulu ndithu – 1 Akorinto 10:31; Kukonda Mulungu ndi mtima wonse,

ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse.- Mateyu 22:37-38.

B. Cholinga chachiwiri chopambana ndicho chakuti “kukonda mnzako monga udzikonda iwe mwini” –

kusapangitsa wina kuti apunthwe – Mateyu 22:39; 1 Akorinto 10:32-33.

C. Zolinga zina zofunika:

1) Funafunani ufumu wa Mulungu musanafune china chiri chonse – Mateyu 6:33.

2) Lolani Yesu awale kuchokera m’mitima mwanu – Agalatiya 2:20; 4:19; Mateyu 5:13-16; 2

Akorinto 3:18.

Page 53: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

53

3) Khalani odzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi zipatso zake – Aefeso 5:18; Agalatiya 5:22-23.

4) Bvulani munthu wakale ndi kubvala watsopano – Aefeso 4:22-24.

5) Pitirizani kuphunzira ndipo mutatha kumvetsa zoyamba nazo za uthenga wabwino kukafike

ku kukhwima ndi kukhala ngati Khristu – Ahebri 6:1-3; Aefeso 4:13-15.

6) Khalani ndi mtima wofuna kuwombola ndi kudzikana nokha, monga mtumiki, monga unali

ndi Yesu – Afilipi 2:5-8; Mateyu 16:24.

7) Mukhale odzazidwa ndi mawu a Mulungu ndi kuwagwiritsa ntchito moyenera – Akolose 3:16;

2 Timoteo 2:15.

5. Kulephera Kupanga Chisankho cha Mulungu kuli Monga Kupanga Chisankho Chokana Mulunguyo. –

Mateyu 12:30. Pali zisankho zina zomwe munthu aliyense amafunikira kuchita. Mwa chitsanzo, tonse tiyenera

kusankha pakatipa:

A. Ubwenzi ndi dziko lapansi, kapena ndi Mulungu – Yakobo 4:4.

B. Kutumikira Mulungu, kapena kutumikira ndalama – Mateyu 6:19,20,24,33.

C. Kubvala Yesu, kapena kukondweretsa zilakolako zathu zathupi – Aroma 13:14.

D. Kupemphera ndi chikhulupiriro, kapena kutaya mtima podera nkhawa – Luka 18:1; Afilipi 4:6.

E. Kufesa ndi cholinga chofuna kusangalatsa Mzimu Woyera, kapena kusangalatsa thupi – Agalatiya 6:8;

Aroma 8:13.

F. Kuyenda m'chipata chopapatiza, kapena moyera bwino – Mateyu 7:13,14.

G. Kugonjera zoipa, kapena kugonjetsa choipa ndi chabwino – Aroma 12:21.

6. Zinthu Zambiri Zidzatijenjemetsa ku Zolinga Zathu.

A. Zinthu zina zomwe zimatijenjemetsa ndi zinthu zabwinonso.

B. Zitsanzo zina zojenjemetsa za m’malembo:

1) Zochitika za m’banja – Luka 9:59-62

2) Madandaulo a m’moyo, chuma, zosangalalasangalala – Luka 8:7,14.

3) Ulimi, geni, ukwati, - Mateyu 22:5; Luka 14:16-20.

4) Ulemerero ndi chibvomerezo chochokera kwa anthu – Yohane 12:42-43.

5) Ntchito ya mpingo yomwe si iri udindo wathu. – Machitidwe 6:1-4.

C. Pofuna kuti tikwaniritse bwino zolinga zathu, tiyenera kukhala okonzekera kupereka zolinga zingapo

zosutsana ndinso kuvutika ngati nkofunika.

1) Abrahamu anasiya mudzi wake ndi kuyendayenda nagona m’mahema – Ahebri 11:17-19.

2) Abrahamu anali wokonzekera kupereka mwana wake ngati uku kunali kofunikira kutero

monga kumvera Mulungu – Ahebri 11:17-19.

Page 54: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

54

3) Mose anasiya mphamvu za ufumu ndi zokoma zonse ku Aigupto kuti atsogolere ana a

Mulungu – Ahebri 11:24-26.

4) Yesu anasiya ulemerero, moyo ofewa, kutchuka, ndi ulamuliro wa dziko lonse – Luka 4:1-

12; 9:58; Yohane 6:14,15.

5) Paulo anasiya mwayi wake wopezera thandizo la ndalama – 1 Akorinto 9:4,11,12.

6) Paulo anasiya zomkondweretsa ndiponso zizolowezi za mtundu wake – 1 Akorinto 9:19-22.

7) Paulo anasiya phindu lake labwino la mtsogolo ndi udindo wapamwamba – Afilipi 3:4-8.

8) Paulo analolera kulowa moyo wachiopsezo ndi udani kuchokera kwa anzake akale.

9) Paulo anazunza thupi naligonjetsa kuti mwina angalephere mu utumiki wake wa kwa Yesu –

1 Akorinto 9:27.

10) Paulo anadzimana ufulu wokwatira ndi kukhala pa banja (ichi sichovomerezeka kwa

aliyense) 1 Akorinto 7:7,8,32-35; werengani Mateyu 19:10-12

11) Tiyenera “kupirira zosautso monga asirikali abwino” – 2 Timoteo 2:3.

12) Tiyenera kuleka inde zinthu ngakhale zofunikira pa moyo wathu ngati zitsutsana ndi zolinga

zathu zofunikira – Mateyu 18:8-9.

7. Zimatithandiza Kwambiri Kukhala ndi Zolinga Zomveka ndi Kuoneka Bwino.

A. Zimathetsa kufooka kapena kumangoyendayenda ndiponso zimatithandiza kupita kutsogolo.

B. Zimatithandiza kupewa kutengeka ndi zina zapadera kapena kuyesedwa.

C. Zimatithandiza kupirira m'masautso – Ahebri 12:2.

D. Zimatithandiza kugwiritsa bwino ntchito nthawi ndi mwayi wathu – Aefeso 5:16; Akolose 4:5.

E. Zimatipangitsa kupeza bwino pa za umoyo wathu. (Gwero limodzi la nthenda ya kukhumudwa

(depression), ndi kusowa kwa zolinga zoti zipereke tanthauzo la moyo).

8. Munthu Amayenera Kukhala ndi Zolinga Zochitika mwa Msanga ndi Zina Zochita Patapita Nthawi.

A. Zolinga zotenga nthawi yaitali kuti zikwaniritsidwe zimapereka chithunzithunzi chonse ndi njira ya

moyo wathu.

B. Zolinga zotenga nthawi yaifupi kuti zikwaniritsidwe, ndi zina zotenga nthawi yapakatikati pa zonse,

imapereka utsogoleri pa chikhalidwe cha munthu cha tsiku ndi tsiku.

C. Zolinga zotenga nthawi yaifupi kuti zikwaniritsidwe ndi zotenga nthawi yapakatikati kuti

zikwanitsidwe ziyenera kulimbikitsa zolinga zanu zodzakwaniritsidwa patapita nthawi yaitali.

D. Sankhani zolinga zomwe ziri zomveka bwino ndi zooneka bwino komanso za phindu.

9. Ganizirani Bwino za Magawo Omwe Adzafunika kuti Mukafike ndi Kukwaniritsa Zolinga Zanuzo.

A. Ngati simuganizira zimenezi, ndiye kuti zolinga zanu zimangokhala nkhamba kamwa chabe

(zongonenedwa) ndipo mumangokwaniritsa pang’ono chabe.

Page 55: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

55

B. Ogwira ntchito a Mulungu a m’malembo anayamba kukonzekera ndipo kenako anayamba

kugwira ntchito gawo ndi gawo.

1) Yesu anayamba wawatengera ophunzira ake kumbali kopanda khamulo ndi cholinga choti

akayambe wawaphunzitsa – Marko 9:30-32; Luka 9:10.

2) Paulo anakonza dongosolo la chopereka lomwe likadayanjanitsa Akhristu achiYuda ndi

amitundu aja – Agalatiya 2:9,10; Aroma 15:25-31; 1 Akorinto 16:1-4; 2 Akorinto 8:9.

3) Pofuna kutumikira molimbika, Paulo anakonza dongosolo lakayendedwe kake ndi cholinga

choti akapezeke ku Yerusalemu patsiku la Pentekosti – Machitidwe 20:16.

4) Paulo anakonza dongosolo lopita ku Roma mwapadera kuti akamthandizeko pa dongosolo la

ulendo wake wopita ku Spania – Aroma 1:10-15; 15:22-24,28.

C Ngakhale simungaona bwinobwino magawo onse a zolinga zanu, tengani ndi chikhulupiriro magawo

omwe ali pafupi nanuwo, ndipo Mulungu adzakutsegulirani magawo ena akutsogolowo – Yoswa

3:14-16.

D Ntchito iri yonse m’moyo wanu iyenera kuchitidwa mwadongosolo komanso ndi cholinga chofuna

kutumikira Mulungu ndi anthu.

10. Mosankha Bwino ndi Kuganizira Bwino Komanso ndi Mphamvu Zonse Tsatirani Zolinga Zomwe

Mwakonzazo.

A. “Munthu wa talente imodzi” anataya zonse chifukwa ankaopa kulakwitsa – Mateyu 25:24-29.

B. Mulungu sanatipatse ife mzimu wa mantha komatu wa mphamvu, ndi chikondi, ndi chidziletso –

2 Timoteo 1:7.

C. Mfumu Yoasi ya ku Israeli analephera pa nkhondo chifukwa cholephera kupanga dongosolo losankha

maganizo amodzi omveka bwino. – 2 Mafumu 13:14-19.

D. Wantchito wangwiro wa Mulungu ayenera kumayang’ana patsogolo, osati pambuyo – Afilipi 3:13-14;

Luka 9:62.

E. Otembenuka a ku Efeso anaotcha zonse zakale poyera atachita chisankho chabwino moganiza bwino –

Machitidwe 19:18-20.

F. Zakeyu anasinthika mwa mphamvu kuloza ku chiyero – Luka 19:8.

G. Yoswa ananena poyera kwa Aisrayeli za cholinga chake – Yoswa 24:15.

H. Ife Akhristu tiyenera kutumikira ndi mphamvu zathu zonse – Malaki 9:10; Aroma 12:11.

11. Zitsanzo Zina za Zolinga za Munthu za Makono.

A Kukhala okhoza kutsogolera maphunziro a Baibulo mwa gulu.

B Kuphunzira kupereka madandaulo athu kwa Mulungu ndi chikhulupiriro.

C Kuphunzira kukhala nacho chikondi cha pa ine mwini kuti ndithenso kuwakonda ena.

D Kuphunzira kukhala ndi mtima wodekha ndi wofatsa.

Page 56: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

56

E Kuphunzira kutumikira anthu onse obvutidwa ndiponso kuwawidwa m’mtima.

F Kumaliza maphunziro anga a Baibulo kusukulu.

G Kuphunzira bukhu limodzi-limodzi mwadongosolo labwino m’Baibulomo.

H Kuzolowera kukhala ndi nthawi yachete ndi Ambuye tsiku ndi tsiku

I Kuthana ndi tchimo londizinga.

J Kuthetsa zonse zondionongera nthawi yanga m’moyo wanga.

K Kukhala mlaliki wampingo kapena mkazi wa mlaliki.

L Kukhala mkulu wa mpingo kapena mkazi wamkulu wa mpingo.

M Kukhala mtundu wa mwamuna, mkazi, kholo, mnyamata kapena mtsikana wolongosoledwa mu

Aefeso 5 ndi 6.

N Kupanga umoyo ndi makhalidwe anga achikoka ndi osiririka monga mboni ya Khristu.

O Kutulukira zinthu zonse zoipa zomwe ndi makhumudwitsa nazo ena ndi kuchitapo kanthu.

P Kumaliza maphunziro anga kuti ndimtumikire Khristu pa ntchito yanga.

Q Kukhala monga woombola miyoyo tsiku ndi tsiku.

R Kuthana ndi zonse zondikopa kuti ndikhale wofooka pa Chikhristu changa.

S Kudziwana ndi Akhristu ena olimba omwe angandilimbikitse ndi kukhala ndi nthawi yokhala nawo.

T Kutumikira anthu mosiyanasiyana.

U Kuwamvetsa bwino anthu, kuti ndithe kuwapatsa uphungu wabwino ndi kuwathandizanso bwino.

V Ngati ndiri mbeta, kukhala munthu yemwe angathe kukopa mkazi kapena mwamuna woyenera.

W Ngati ndiri womasuka kukwatira, ndipeze mkazi kapena mwamuna yemwe angamandilimbikitse

pakutumikira Mulungu.

X Kupereka khomo langa kuti Mulungu achite nalo ndi kukhala chida champhamvu pakutumikira Iye.

Y Kuphunzira kapena kumvetsa bwino chomwe ndi kufuna kuchidziwa.

Z Kuphunzira kuti ndidziwe bwino pokonzekera mayeso.

Mawu otsiriza: Inu mukuwadziwa Akhristu ena paokhapaokha ngakhale mabanja omwe amakhala ndi chikoka

chodabwitsa kwambiri pa zabwino. Awa ndi anthu omwe amanga ganizo limodzi ataganiza mozama kwambiri pa

zoti, kodi iwo ndi ndani, ndinso chomwe afuna kuchita ndi miyoyo yawo. Iwowa anafika poti sasinthasinthanso

zolinga zawo.

Nkhani imeneyi sikutinso amayionaona pafupipafupi ayi; ndi ganizo loti lakhazikika malingana ndi chisankho

chawo chotsiriza. Kutanthauza kumeneku ndi kudzipereka kwa mtundu umenewu sikwachilendo ayi, koma ndi

momwe ziyenera kukhalira chifukwa cha ufumu wa Khristu. Izi ndi zotheka kwa wina aliyense wa ife.

Page 57: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

57

Phunziro 12 - Zofunikira Zoonadi Zoyenera Kuganiziridwa Poyambirira

Mawu oyamba: Anthu awiri amayamba pamodzi ndi mwayi wofanana. Mmodzi amakhala wokondwa, wopindula

ndi wopambana m'zochita zake. Pamene winayo amangoononga moyo wake, wosatha kukwaniritsa chirichonse

ndipo pa mathero pake moyo wake umangothera m'kunong’oneza bondo (kukhumudwa).

" Banja lina liri ndi ana osangalala ndi omvera.

Koma banja lina liri ndi ana aukali, ogalukira ndi owononga.

" Wina amakhala pa ukwati ndi mkazi/mwamuna mmodzi mosangalala kwa moyo wake wonse.

Pamene wina akwatira kwatira ndipo amangodziunjikira chiwawa mumtima.

" Munthu wina amapeza chuma nakhala chikwaya koma kenako amadzipha yekha.

Koma wina ali ndi phindu la muyezo wosachurukira koma asangalala popeza ali ndi moyo.

" Munthu wina amakwaniritsa zolinga zake chimodzi-chimodzi.

Pamene wina amangonena namalota koma osachitapo ngakhale ndi chimodzi chomwe.

" Munthu wina amalandiridwa ndi Yesu kulowa kumwamba.

Pamene wina akubwezedwa.

Masiyanidwe: Zofunika Zenizeni ndi Zoyenera Kuganiziridwa Poyamba.

Inu muli ndi mwayi wokhala ndi moyo umodzi wokha basi. Mwapatsidwa njira zambiri zousungira ndi

kupindula nawo. Sionse zomwe zimakukopani monga zosiririka ndi maonekedwe onga abwino. Palibe china

coopsya kwambiri ngati kutaya ndikuononga zaka za moyo wanu kapena moyo wanu wonse, kenako ndi kuturukira

kuti mumangotsatira zopanda pake.

Kupambana kumakhazikika pa zofunikira zenizeni ndi pa zoyambirira. Munthu wa zaka 20 zakubadwa

angathe kukhala ndi zikwi za ndalama poyika ndalama yokwanira K50.00 padera kuti imupindulirire pa mwezi

uliwonse. Koma angathe kuchita izi pokhapokha ngati ali ndi chidwi chofuna kuika “kusunga ndalama” ngati

chinthu choyenerera kuganiziridwa poyamba pa zina zonse, ndi kusiya zina zonsezo zomwe akanagula ndi K50.00

ija. M’menemo ndi momwe ziriri m'moyo wathu wonse kuphatikizapo zauzimu.

1. Si Zonse Zimene Zimaoneka Mosiririka ndi Mofunika Chomwechi.

A. Adamu ndi Hava adachimwa chifukwa adakhulupirira bodza la Satana napanga chisankho

cholakwika. Genesis 3:1-7.

B. Satana ndiye “tate wamabodza onse” ndipo amatseka anthu kumaso kuti asaone zofunikira

zenizeni. Yohane 8:44; Chibvumbulutso 12:9; 2 Akorinto 4:4.

C. Thupi lathu lolepherali, la nyama si odalilika kuti lingatithandize kupanga chisankho cha

zofunikira zoyenere. Thupi limalakalaka zinthu zolakwika, ndipo zilakolako zathu zimatinyenga

pamene tifuna kupanga chisankho cha zofunikira zenizeni – Aefeso 4:22; Yeremiya 17:9.

D. Malembo amagwiritsa ntchito zithunzithunzi zosiyanasiyana pofuna kufotokoza bwino za anthu

omwe adapanga chisankho cha zinthu zofunikira mopusa:

1) Kugula chakudya chomwe sichiri chakudya – Yeremiya 55:2

Page 58: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

58

2) Kukumba zitsime zong’aluka zomwe sizingasunge madzi – Yeremiya 2:13.

3) Kuika ndalama m’thumba looboka - Hagai 1:6.

4) Kugona mutafunda bulangeke losakwanira msinkhu wanu – Yesaya 28:20.

5) Kumanga nyumba pa mtchenga - Mateyu 7:24-27.

2. Pamakhala Choopsya, Kutaya Phindu, Pamodzi ndi Kusweka Mtima Pamene Tinyengeka ndi Zinthu

Zowoneka Ngati Zoyenerera Monyenga.

A. Titha kumaganiza kuti tiri bwino pamene siziri choncho, mpakana nthawi nkutithera –

Chibvumbulutso 3:17; Miyambo 14:12.

B. Titha kutaya zinthu zamtengo wapatali zoti sitingathe kudzazipezanso. (Nthawi zija izi

zimangochitika pa kanthawi pang’ono ka uchitsiru) – Genesis 25:29-34; Ahebri 12:16,17.

Zofotokozera za lero:

1) Moyo ndi maganizo osokonezedwa ndi mankhwala ozunguza bongo.

2) Umoyo wathanzi wotayika chifukwa chochita zinthu zosagwirizana ndi umunthu ndi

kulowerera mu zinthu zina.

3) Kusinthika m’chikhalidwe chachibadwidwe chifukwa cha uchiledzelere ndinso kugwiritsa

ntchito chamba ndi mankhwala ena ozunguza bongo.

4) Ana kulowerera ndi kusokera kuchoka m’manja mwa Mulungu chifukwa cha moyo

wokonda zathupi ndi kutailira.

5) Kubvuta kwa maubale a mabanja ndi kusweka.

6) Kuyamba kugonana asanalowe m’banja.

7.) Kuonongeka maganizo chifukwa chozolowera kuona, kuwerenga ndi kumvera zolaula ndi

za maliseke.

8.) Miyoyo yathu kuonongeka kwa muyaya chifukwa chonyalanyaza Mulungu ndi zofunikira

zoyenera za mpaka kale kale.

C. Zinthu zomwe tinazidalira monga zotipatsa chitetezo pa moyo wathu, zingathe mwadzidzidzi

kutipangitsa kulephera ndi kutithawa, kutisiya m’mantha opandanso chiyembekezo china chiri

chonse - Luka 12:15-21; 16:19-31; Mateyu 25:10-13; 7:21-23; Yesaya 28:15-19.

1) Imafika nthawi imene sipamapezekanso mwayiwo woyambira kugwiritsa ntchito bwino

moyo wathu.

2) Ngati tagulitsa miyoyo yathu ndi zinthu zina, tidzachita chiyani pamene Satana adzabwera

kudzaitenga?

D. Zinthu zomwe timaona ngati zidzakhalabe kwamuyaya sidzitero ayi – 1 Yohane 2:16-17; Mateyu

6:19-20.

1) Zinthu zomwe matupi athu amalakalaka.

Page 59: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

59

2) Zinthu zomwe maso athu amalakalaka.

3) Zinthu zomwe timadzikuza nazo padziko pano.

E. Titha kukhala munthu wina wake yemwe ife sitifuna kukhala, ndi pangitsa enanso kukhala monga

momwe sitifunira kuti akhale. Zofunikira ndi zoyenera kuganiziridwa moyambirira zathu

zimatisintha ndi kutipatsa moyo ndi khalidwe lina.

F. Kuyamba ndi zolakwika kwathu kumatisokoneza kuona zenizeni zoyenera kuganiziridwa

poyambirira zomwe zikanatidalitsa.

3. Zabwino Zimabwera Kwa Ife Kupyolera mu Zoyenera Kuganiziridwa Poyambirira.

A. Timakwaniritsa zinthu zofunika mwambiri pa chitetezo ndi chipulumutso chathu. Zinthu

Zofunikira kwambiri zimatheka – Miyambo 24:27.

B. Timapewa kuononga miyoyo yathu ndi mphamvu zathu.

C. Timakhala ndi chuma koma chuma chake ndi chimene Mulungu agwirizana nacho – Mateyu 6:19-

20; 1 Akorinto 3:21-23.

D. Sankhani bwino zofunika zoyenerera ndipo zina ziri zonse zofunikira koposa zonse zidzakhala

zanu – Mateyu 6:33.

4. Malembo Amaphunzitsa za Zimene Ziri Zofunikiradi Ndinso Momwe Tingakonzere Dongosolo la

Zofunikira Zolondola M’moyo ndi Kupambana.

A. Malembo amatiunikira zabodza ndi kutichenjeza kuti tithawe. Zitsanzo:

1) Kusangalalira khalidwe lotsutsana ndi umunthu (nkhuli ya chiwerewere) Miyambo 5:15;

9:13-18; 1 Atesalonika 4:3-8; 1 Akorinto 6:15-20.

2) Uchidakwa, kuledzera (ndinso kutsuta chamba) - Miyambo 23:29-35.

3) Zokondweretsa (monga choganizira choyambirira m’moyo) – 2 Timoteo 3:4; 1 Timoteo

5:6.

4) Kutamandidwa ndi kulandira ulemu, kukhulupiridwa – Yohane 5:44; 12:42-43.

5) Nzeru za dziko lapansi 1 Akorinto :18-25; 2:1-5.

6) "Maufulu - Afilipi 2:5-11.

B. Malembo amatipatsa mndandanda wa mfundo zotithandiza kuchita chisankho chabwino cha

zofunikira zoyenera:

1) Khalidwe la mkati mwa mtima lokoma koposa lowonekera kunja kwa mtima - 1 Samueli

16:7; 1 Petro 3:1-5.

2) Kutumikira Mulungu modzipereka koposa kungoganizira ndalama ndi zinthu zina -

Mateyu 6:19-21,24-33; Luka 12:15.

3) Kuona zosaoneka ndi maso monga zofunikira koposa zooneka – 2 Akorinto 4:18; 5:7.

Page 60: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

60

4) Za muyaya kuposa zongokhala kanthawi kochepa – 2 Akorinto 4:16-18; 1Yohane

2:16,17; 2 Petro 3:8-13.

5) Za kumwamba kuposa za padziko - Akolose 3:1,2.

6) Umulungu poyamba tisanaphunzire zinazo – 1 Timoteo 4:8.

7) Chibvomerezo cha Mulungu poyamba pa chibvomerezo cha munthu – Yohane 5:44;

12:43; Aroma 2:28-29.

8) Zauzimu poyamba pa zathupi ndi zapansi pano – Yohane 6:63; 4:21-24; Luka 10:38-42.

9) Mtima wapa lamulo pamwamba pa kalata chabe kapena chilembo - 2 Akorinto 3:6;

Mateyu 23:23,24; 5:20-48.

10) Chikondi cha pa Mulungu choposa cha padziko lapansi – Yakobo 4:4,5; Yohane

15:14,15.

5. Lamulo la Yesu pa Zoyenera Kuganiziridwa Moyambirira: "Yambani kufuna ufumu wa Mulungu ndi

chilungamo chake poyambirira, ndipo zina zonse zidzapatsidwa kwa inunso”– Mateyu 6:33.

A. Tayang’anani bwino zina za zomwe timaziganizira moyambirira m’moyo wa masiku ano. Koma

zimayenerezedwa bwanji ndi moyo wa Khristu?

1) Kukhala ndi nthawi zabwino kopitirira.

2) Ndikhale ndi ufulu wanga, ndikhale omasuka.

3) Ndipange ndalama zochuruka.

4) Kusangalatsa umoyo wanga (ngati zindikondweretsa, ndichite basi)

5) Ndikhale wopambana mu ntchito yanga.

6) Kukhala munthu wodziwika, wamdidi ndi wa ulemu wake.

7) Kuchotsa mabvuto, umphawi, matenda ndi kuponderezedwa.

8) Kukhala ndi mphamvu mu ndale.

9) Kukwatira/kukwatiwa ndi munthu woti asangalatse moyo wanga.

10) Kulandira ufulu wodzilamula ndekha popanda wina wondiuza chochita.

11) Kupeza njira zina zodzithandiza nazo.

12) Kupeza galimoto ya makono yonga yampikisano.

B. Yesu anamaphunzitsa kuti palibe chinthu chabwino kapena chimatipatsa moyo ngati sichitumikira

ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake – Mateyu 6:33.

C. Mulungu anawaphunzitsa anthu ake a m’Chipangano Chakale momwe angaperekere ulemu kwa

Mulungu woyambirira mu zonse zomwe anachita.

Page 61: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

61

1) Zokolola zawo zoyamba - Eksodo 23:19.

2) Ana a ziweto oyambirira kubadwa ndi ana awonso - Eksodo 34:19,20; Deuteronomo

15:19.

3) Chachikhumi cha zopindula zawo zonse - Levitiko 27:30,32.

4) Nyama zokhazo zopanda chirema ziperekedwe nsembe - Deuteronomo 15:21.

5) Tsiku limodzi sabata iriyonse likhale lopatulidwira Mulungu - Eksodo 20:8-11.

6) Pasakhalenso kupembedza milungu ina - Eksodo 20:3-6.

7) Osakwatira akunja (osapembedza) - Deuteronomo 7:3,4.

D. Zizindikiro zina za zofunikira za ufumu wakumwamba zoyenera kuziganizira moyambirira

m’miyoyo yathu:

1) Kusonkhana kawirikawiri ndi kupembedza pamene mpingo ukumana, ndinso kulambira

kawirikawiri kwa banja lonse - Ahebri 10:25.

2) Ulemu kwa makolo ndi aulamuliro ena - Aefeso 6:2; Aroma 13:1,2.

3) Kuphunzira mawu a Mulungu mosalekeza – Masalmo 1:2.

4) Kupemphera mosalekeza – Danieli 6:10b; 1 Atesalonika 5:17.

5) Kupereka kawiri-kawiri, maufulu ndi monga momwe tapindulira 1 Akorinto 16:1,2; 2

Akorinto 9:6,7.

6) Kukhala mwa chiyero ndi mosamala; kupewa chosalungama chirichonse woona mtima – 2

Akorinto 6:14; 7:1; 1 Atesalonika 5:22.

7) Kumanga banja ndi munthu wokhala ndi maganizo ofunikira oyambirira ndi ufumu wa

kumwamba, (kwa omwe sanapeze banja) – 2 Akorinto 6:14; 1 Akorinto 7:39.

E. Sitingathe kufuna ndi kusunga ufumu wakumwamba popanda kusiya ndi kuiwala zinthu zina ndi

zina komanso kubvutika kumene nthawi zina – Machitidwe 14:22; Mateyu 10:37; Luka 14:26-27;

Mateyu 18:8-9.

1) Danieli1:1-16

2) Danieli 6:1-10

3) Danieli 3:1-18

4) Afilipi 3:7,8

5) Mateyu 13:44-46.

F. Pofuna kuika ufumu wakumwamba poyambirira, tiyenera kukhala okonzekera kukhala

osiyanitsidwa ndi ena – Yohane 17:14.

G. Kusankha zofunikira zosayenera ndi zonyenga kumatheka chifukwa chosakhala ndi chidwi

chosankha zofunikira zoona.

Page 62: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

62

H. Sitingataye chirichonse chofunikira kwambiri pamoyo wathu pa kuika ufumu wa Mulungu

poyambirira.

1) Mulungu anampatsa Solomo chirichonse chofunika chifukwa Solomoyo anaganizira

bwino chofunika choyambirira mwanzeru. – 1 Mafumu 3:4-14.

2) Mulungu nthawi zonse amatibwezera ife zochuruka zoposa zomwe ife timapereka.

a. Ndalama ndi zofunikira zina kwa woperekayo – Miyambo 3:9,10; Luka 6:38;

Malaki 3:7-12.

b. Ulemu kwa odzichepetsa – Mateyu 18:4; Luka 14:11.

c. Kulandira chifukwa chodzipereka – Mateyu 16:21.16:25.

d. Abwenzi ndi okondedwa kwa iwo amene asiyana ndi enawo chifukwa cha Khristu

– Marko 10:29-30.

e. Nthawi ya muyaya kwa iwo omwe amataya nthawi yawo chifukwa cha ufumu wa

kumwamba m'moyo uno – 1 Atesalonika 4:17.

Mawu otsiriza: Ngakhalenso m’moyo wa dziko lapansi, kupambana ndi kupeza bwino kumadalira pa zofunikira

ndi zoyenera kuganiziridwa moyambirira. Kodi muganiza kuti ngati ziri chonchi pansi pano bwanji momwe

zidzakhalire kumwambako!

Jim Elliott, mishonale yemwe anafa mophedwa analemba kuti, "Siwopusa iye amene apereka chomwe

sangathe kuchisunga kuti apeze chomwe sangathe kutaya”

PHUNZIRO 13 - KUSUNGA MAUBALE ABWINO

Mawu oyamba: Satana amafuna kugawanitsa ndi kudanitsa anthu. Amafetsa kuwawirana mtima ndi udani. Khristu

amafuna kuyanjanitsa ndi kugwirizanitsa anthu. Iye amafetsa mtendere ndi chikondi. Anthu nthawi zonse adzakhala

ndi maganizo olekana ndi makangano. Ngati zimenezi tingozilekerera osaziperera njira yokonza, zimakwaniritsa

zolinga za Satana. Maganizo a Yesu angathe kuthetsa kulekana kwa maganizo pakati pa anthu ndi kugwetsa

malinga olekanitsa mabanja, mipingo, achinansi, kuntchito kapena maubale ena osiyanasiyana. Yesu watipatsa

mfundo zomwe zingathe kuchiza ndi kubwezeretsa ubale woonongeka. Tiyeni tione komwe makangano

amachokera ndi chomwe tingachite pa nkhani imeneyi.

1. Muzu weniweni wa kulimbana ndi kulakwirana pakati pa anthu ndi kunyada ndi kudzikonda – Mateyu

18:1-5.

A. Bvuto: Tonse timafuna kudziwa kuti “Kodi wamkulu ndani?” (wopambana, mpondamatiki, wokhoza,

wodzisamala, wosiririka, wokondedwa, wa ulamuliro woposa ndi zina zotero). Ngati nthawi zonse ndi

mangoganizira za ine ndekha, ndiye kuti kulimbana ndi enawo kuyenera kuyambika nthawi ina iriyonse.

B. Kuthetsa kwake: Kukhala wakufa kuthupi” – Agalatiya 2:20.

1) Mateyu 18:3,4 – Mudzione ngati kamwana kakang’ono podzifanizira ndi ena.

2) Afilipi 2:5-8 – Kutaya ulemu ndi ufulu wanu mwakufuna kwanu.

Page 63: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

63

3) Aefeso 5:21 – Kumverana chifukwa choopa ndi kulemekeza Khristu.

4) Afilipi 2:3,4 – Muwatenge ena onse monga ofunikira koposa inu.

5) Yohane 13:3-17 – Sambitsanani mapazi anu.

2. Sitingathe kubwezeretsa ubale womwe taononga – Mateyu 18:6.

A. Malipiro kwa olakwayo:

1) “Kuli bwino amizidwe m’nyanja yakuya.”

2) Mulungu sadzamva pemphero lake – Mateyu 5:23,24; Ahebri 12:14.

B. Mtengo kwa ena onse okhudzidwa.

1) Abale apabanja – kuwawidwa

2) Mpingo – kupatukana

3) Osakhulupirira - kukanidwa – Yohane 17:20,21; Afilipi 2:14-16.

C. Musalole kukhala woyambitsa udani kapena kukana kuthetsa zolimbana – Aroma 12:18.

1) Konzani msanga tolakwika ting’ono-ting’ono pa ubale wanu madzi asanafike mkhosi.

2) Pezani njira zothandiza kuti mukonze ubale molumikizana.

3) Limbikirani kuonetsa chikondi. Bwezerani chabwino ku choipa – Aroma 12:17,21.

4) Musaumirire pa ufulu wanu – mungadzaupezenso.

5) Mudzadalitsidwa – Mateyu 5:9.

3. Muyenera kuganizira ndi kuthana ndi zonse zoyambitsa maudani ndi kukhumudwitsa – Mateyu 18:7-

14.

A. Kuganizira gwero la zolakwirana: Kodi inu muli ndi gawo lanji pa kulimbanako? Mateyu 7:1-5.

1) Ndi milandu yochepa yomwe wolakwa amakhala mmodzi.

2) Yang’anani bwino mopanda kukondera chomwe chakhumudwitsa mnzanu, mwana, kholo,

mbale, ndi mlongo wanu.

3) Kodi zochita zanga pankhaniyi zimaonjeza bwanji moto wa nkhani?

a. Mwina zolakwa zamnzangayo sizachilendo kwenikweni, koma momwe ndazitengera ndi

momwe muli moonjezera mafuta pa moto.

b. Mwina ndimaganizira kwambiri za ufulu wanga.

c. Ena sadzasiya kuchimwa. Kuthetsa kwake kuyenera kukhala malingana ndi momwe

ndiitengera nkhaniyo.

d. Ichi ndicho chinsinsi cha ufulu ndi mtendere.

Page 64: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

64

B. Kuchotsa zoyambitsa kulakwirana:

1) Kuyankhula (dula dzanja lako, kolowola diso) kumasonyeza changu chochotsera zoyambitsa

uchimo ndi kulakwirana. Mizimu ikutayika.

2) Kudzitamandira ndi kudzikonda kwanga sikuli koyenera.

3) Chikondi ndicho chidzalipira mtengo wa mtendere ndi kuyanjananso.

a. Yesu analipira msonkho womwe sanayenera – Mateyu 17:24-27.

b. “Bwanji osangololera kuti inu mukhale onyengedwayo” – 1 Akorinto 6:1-8.

c. Abrahamu anangompatsa Loti mwayi woti iye asankhe malo okhalako poyambirira popewa

kulimbana – Genesis 13:8-11.

4) Muthane nazo zolakwiranazo tsopano – musalorele kuti kudzitamandira kwanu ndi kudzikonda

kwanu kuononge mwana wa Mulungu – Aroma 14:13,15,19,21.

4. Tsatirani ndondomeko ya Mulungu yothetsera zolakwirana – Mateyu 18:15-20; 5:23-26.

A. Pitani kwa yemwe wakulakwiraniyo ndi kumuuza iyeyo osati ena ayi.

1) Timangofuna kuuza wina aliyense chifukwa cha mkwiyo wathu.

2) Anthu ambiri amathamangira kuuza akulu a mpingo asanaonane ndi wowalakwirayo.

B. Pitani modzichepetsa ndi modekha – Agalatiya 6:1. Mkwiyo umapangitsa kuti munthu winayo ayambe

kudziteteza ndipo amayamba kudzikonzera njira zodzitchinjiriza nazo.

C. Chitani zimenezi mwachangu, mkanganowo usanakule, usanakhudze ena, ndipo mitima isanafike

polimba.

1) Timalandira chilango chowawa pokana nzeru ya malemba.

2) Kulimbana kumakhala zaka zambiri mwinanso mpaka moyo wawo wonse chifukwa cha kunyada.

3) Koma ngati pali chikondi chokwanira ndi kukhudzidwa pa moyo wabwino wa pa banja pake,

mpingo, kuntchito, anthu atha kupeza njira.

5. Khululukani monganso Mulungu anakukhululukirani. – Mateyu 18:21-35.

A. Kukhululuka kulibenso china chofaniziridwa nacho, ngati tifuna kupulumutsidwa – Mateyu 6:12,14,15.

1) Kusakhululuka ndilo “tchimo losakhululukidwa” lomwe tingalichite.

2) Nchifukwa chiyani tidzayembekezera kuti Mulungu atichitire ife zomwe sitingachitire enawo?

3) Kubwezera kuli kwa Mulungu – Aroma 12:19.

B. Kukhululuka ndi “mchitidwe wokhala ndi cholinga” osati wongomverera m’thupi ayi.

1) Monganso chikondi, ndi lamulo lachikhalire.

Page 65: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

65

2) Titha kuganizira zosankha kuchita mchitidwe wokhululuka. Kenako tidzayamba kumva m’thupi.

C. Kusakhululuka kumangolekerera ubale ukumangosweka.

1) Kuwawirana mtima pakati pa mwamuna ndi mkazi komwe kumangokhala osapezeredwa njira

yothetsedwa kumasakaza banja. (Ngakhale kuwawirana mtima kwa kholo, mbale, mlongo ngakhale

wina aliyense).

2) Mkwiyo ndi kuwawirana mtima kwathu kumapatsa Satana mwayi m’miyoyo yathu – Yakobo 1:20;

Aefeso 4:26,27.

D. Kukhululukirana kumabwezeretsa ndi kuchiza maubale owonongeka.

1) Ngati wina apempha chikhululukiro, tiyenera kutero nthawi yomweyo kuchokera pansi pa mtima,

popeza nafenso ndi ochimwa.

2) Mzimu wokhululukira umakhala wofunikira munthu winayo asanalape.

a. Khristu anapempherera iwo omupachika – Luka 23:34.

b. Mzimu wokhululukira sufulumiza kuchita choipa – 1 Petro 4:8; 1 Akorinto 13:6,7.

c. Pamene munthu mmodzi ali nawo mzimu wokhululukira ndipo abwera poyera, zimapangitsa

kuti winayonso abwere poyera.

Mawu otsiriza: Pamene tikuchita ndi zolakwirana, tikupemphedwa kuti “tithetse zoipa ndi zabwino.” – Aroma

12:20,21. Chabwino chomwe muchita chidzasungunula mtima wa yemwe munali kulimbana nayeyo – 1 Samueli

24:26.

PHUNZIRO 14 - Kusankha Mnzanu Woyenera. Mawu oyamba: Palibe chisankho china chomwe mungachite, chopusa kutembenukira kwa Khristu, chomwe chidzakupatsani chisangalalo ndi tsogolo lanu labwino. Miyoyo yambiri yokhala nazo zoyeneretsa zabwino yalephera ndi kungoziziritsidwa chifukwa chosankha mnzawo mosayenera. Ambiri ena athandizidwa ndi kupindula kwambiri chifukwa chopanga chisankho chabwino ndi choyenera. Zoonadi Mulungu ndi wokhuzidwa kwambiri pakufunikira kwa chisankho. Iye amafuna kuti ife tidzisankha mwanzeru, ndipo watipatsa ife malamulo ndi mfundo zoti zititsogolere popanga chisankho chabwinocho. Iye adzathanso kupereka nzeru zapadera ndi utsogoleri wabwino wosamalirika pa nkhani imeneyi. Komatu Mulungu amangotsogolera iwo okhawo omwe ali okonzeka kuganizira, ndi kupeza ndi kuchita chomwe chiri choyenera. Mkhristu sayenera “kutsogolera Mulungu,” koma funani chifuniro cha Mulungu pa za banja monga momwe achitira ndi zina zonse. Munthu yemwe amafuna thandizo la Mulungu ndi kuchita mwanzeru angathe kupeza mnzake wa moyo wake wonse yemwe adzakhale wothandiza, wosalepheretsa, ku utumiki wake wa kwa Mulungu; yemwe adzagawana za kufunika kwa utumiki wake. Pemphero ndi kuweruza mwanzeru ziri zinthu ziwiri zazikulu za momwe anthu odzalowa m’banja angadzasangalalire ndi kulandira zipatso m’banjamo. 1. Chisankho china chiri chonse chomwe timachita m’moyo wathu, kaya kuti tikwatire, kapena ayi,

kaya kuti tikwatire yani, zonsezi zichitike molemekeza Mulungu, kuti timsangalatse ndinso kuti titumikire zolinga za ufumu wake – 1 Akorinto 10:31; Mateyu 22:37,38; 6:33.

2. Pempherani kuti mulandire nzeru za banja. Mulungu afuna kukutsogolerani.

A. Ganizirani ndi kupeza ngati ndi Mulungu wafuna kuti inu mukwatire pa nthawi imeneyi.

Page 66: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

66

1) Kodi nkofunikira kuti mukhale pa umbeta, kwa kanthawi kameneka, kuti muthe

kusamalira za utumiki wanu kwa Mulungu mosasowa nthawi? 1 Akorinto 7:32-35.

2) Kodi nkofunikira kuyembekezera kaya musanakwatire kuti muyambe mwatsiriza zina zofunikira pamoyo wanu wakutsogolo, monga maphunziro?

3) Kodi mwa kula kokwanira kukwatira, Kodi muli nazo ndalama zokwanira

kuyambira bwanji?

B. Mulungu adzakupatsani nzeru ndi utsogoleri posankha mnzanu woyenera - Yakobo 1:5; Miyambo 3:5,6. Mulungu anatsogolera njira yabwino yothandiza Isaki kupeza mkazi woyenera - Genesis 24.

3. Yembekezerani kokwanira musanakwatire kuti mukhale okwanitsidwa kuti mudzapange chisankho

chabwino. Munthu wosakhwima maganizo, wadyera ndi wodzikonda yekha sangathe kudikira. Koma wokhwima maganizo angathe.

4. Kwatirani Mkhristu wodzipereka yemwe angathe kuthandizana nanu pakutumikira kwanu kwa

Mulungu ndi pa zolinga zanu zokhalira ndi moyo.

A. Moyo waphumphu wa malembo umaonetsa kuti sichofuna cha Mulungu kuti Mkhristu akwatire osakhulupirira:

1) Abrahamu anakanitsitsa kuti Isaki asakwatire Akanani osapembedza – Genesis 24:1-4.

2) Isaki ndi Rabeka nawonso analimbikira zomwezo pamene Yakobo anakula, ndipo

anamtumiza kutali komwe akanapeza mkazi wokhulupirira Mulungu – Genesis 27:46; 28:1-3.

3) Aisraeli analetsedwa kukwatira Akanani osapembedza Mulungu - Deuteronomo 7:1-4;

Ezara 9, 10.

4) Akhristu sayenera “kumangidwa m’goli limodzi ndi osakhulupirirawo" - 2 Akorinto 6:14. Izinso ziphatikizirapo ukwati.

5) Wa masiye wa Chikhristu, ngati afuna kukwatiwanso, ayenera kukwatiwa ndi amene “ali

mwa Ambuye” - 1 Akorinto 7:39.

6) Ngati mtumwi Paulo ndi atumwi enawo akadakwatira azikazi awo akanakhala okhulupirira - 1 Akorinto 9:5.

B. Mkhristu asamakonde kuyenda ndi osakhulupirira, chifukwa ndi anthu ochepa omwe angathe

kubwerera atalowa kale m'matope. Ambiri alibe mphamvu zimene. Kukhuzidwa kwa mumtima kumachitika poyambirira munthu asanazindikire bwino.

C. Musakonze ubwenzi ndi munthu ndi cholinga chofuna kumtembenuza. Ndi Akhristu ochepa

omwe ali olimba kotero kuti sangagwe pamene akodwa m’maganizo.

D. Inde ndi zoona kuti kumene Akhristu akwatira osakhulupirira, nthawi zina wosakhulupirirayo amatembenuzidwa. Pali zitsanzo zotere mumpingomo. Komabe chitsanzo ichi nthawi zambiri sichikhala ndi umboni wabwino, chifukwa Akhristu ambiri omwe anakwatira osakhulupirira ndipo sanathe kuwatembuza, pamene tinena pano sali mumpingo ndipo tinawaiwala.

E. Kulimbana kwambiri kumabwera m’banja pamene wina ndi wosakhulupirira.

F. Pamene Mkhristu akwatira wakunja ndi cholinga chofuna kumpulumutsa, ndiye kuti Mkhristuyo

azachepetsako tsogolo la ntchito yake yopulumutsa miyoyo ina yomwe ikanafikiridwa 5. Sankhani Mnzanu Posayang’anira Kukongola kwa Maonekedwe Kokha - 1 Atesalonika 4:3-8 (RSV).

Page 67: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

67

6. Sankhani Munthu Yemwe Molingana ndi Malamulo a Mulungu ali Woyenera ndi Womasuka Kukwatiwa - Mateyu 5:31,32; 19:9; Marko 10:11,12; 1 Akorinto 7:10,11.

7. Musakwatire Munthu ndi Cholinga Choti Mumusinthe.

A. Ngati munthu sakopeka kokwanira kuti asinthe zikhulupiriro zolakwika ndi makhalidwe olakwika pamene “chikondi chiri pa mponda-chimera” munthawi ya ubwezi wawo, nkosatheka kuti angasinthe mtsogolo.

B. Ngakhale patakhala kusinthika panthawi ya ubwenzi wanu, muyenera kukhala ndi nthawi

yokwanira yoti muone ngati kusinthako kwa chitika chifukwa cha Mulungu komanso ndi kwenikweni, osangoti kwa kanthawi kochepa chabe, kungofuna kunyengeza mnzakeyo mu nthawi zimene nonse simunakhwime maganizo.

C. Cholinga cha chitomero ndi ukwati sikuti mukalalikire kapena kukamsintha. Ngati simutha kulandira munthu momwe aliri, ndipo ngati simufuna kuti munthuyo akhale mayi wa ana anu monga momwe aliri, chonde, musamkwatire munthuyo! Pamene mulowa phangano la banja, Mulungu sakupatsani ufulu woti musinthe maganizo anu ndi kusiya ukwati.

8. Pali Zizindikiro Zina Zomwe Zingakuthandizeni Kuti Musankhe Munthu Woyenerera ndi Kupewa

Olakwikawo.

A. Khalidwe la kwa makolo ndi ubale kwa iwo.

1) Momwe munthu adziperekera ndi kumvera (kaya kulephera kumvera) ulamuliro wa makolo, zimaonetsa momwenso iye angadzachitire pakumvera ndikudzipereka kofunikira m’banja. Momwe munthu adziperekera ndi kumvera makolo ake zimaonetseratu momwe munthu adzalemekezere mnzake wa banja.

2) Mwamuna adzayesetsa kuchita ndi mkazi wake monga momwe ankachitira ndi amayi

ake; nayenso mkazi adzayesetsa kuchita ndi mwamuna wake monga momwe ankachitira ndi atate wake.

B. Momwe makolo achitira ndi moyo wa mwana:

1) Kusamala pakhomo – mosalongosoka kapena molongosoka

2) Kusamalira kwa bambo pa banja

3) Kasamalidwe ka chuma kolongosoka kapena kosalongosoka

4) Ulemu kapena mwano

5) Njira zabwino kapena zoipa zothetsera makangano

6) Mabvuto chifukwa cha kumwa kapena mankhwala ozunguza bongo

7) Kukhoza kapena kulephera kuonetsa chikondi

8) Udindo ndi kukhwima maganizo

9) Kutsudzulana

C. Khalidwe la munthu pa za ulamuliro.

D. Ubale wa munthu ndi anthu:

1) Kutha kapena kulephera kukhulupirira anthu

2) Kukhoza kapena kulephela kugwirizana, kumasuka

Page 68: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

68

3) Kukhoza kapena kulephera kufikira ena

4) Manyazi kapena kudzikhulupirira

E. Kudzidalira kwa munthu kapena kusadzidalira. Zizindikiro za kusowa kudzidalira munthu pa wekha. 1) Kufuna kukondedwa koma osakhutitsidwa, komanso kulephera kupereka

chikondi.

2) Kudzionetsera

3) Kufuna anthu onse azitama ndi kunena za inu.

4) Kukhala ndi mabvuto auchiledzelere ndi mankhwala ozunguza bongo.

5) Kumangokhala ndi zibwenzi nthawi ina iriyonse kosalekeza.

F. Kusakhazikika m’maganizo a pansi pa mtima kapena kukhazikika m’maganizo a pansi pa mtima, kutetezeka kapena ayi. “kuupeza mtima kapena kusaupeza mtima)

1) Nsanje ya a bwenzi a anzanu ndi ya zina zokondweretsa zawo .

2) Kumangofuna kukhala limodzi nthawi zonse.

3) Mabvuto a kuledzera kaya kudya mankhwala ozunguza bongo.

4) Kulephera kusankha ganizo lenileni ndi kuliteteza kapena kutetezedwa

nalo

5) Kulimbana ndi kukangana kawirikawiri ndi anthu.

6) Kukhala wobvutikavutika ndi maganizo ndi makhalidwe osiyanasiyana nthawi ndi nthawi (kukhala wolunda nthawi zina, wokondwa nthawi zina)

7) Kukwiyakwiya popanda chifukwa chenicheni.

8) Uhule.

G. Kukhwima m’maganizo kapena kusakhwima m’maganizo ndi zizindikiro zake.

1) Kukhala ndi chikhumbo khumbo.

2) Kusafuna kuonetsa nkhope yokondwa.

3) Kufuna kukhala ndi zonse zomwe muzikhumba.

4) Kulephera kusamala ndi Kulongosola chuma.

5) Kulephera kulongosola bwino za ntchito yanu ndi maudindo ena onse.

6) Kulephera kuweruza bwino.

7) Kusasonkhana kumpingo kawirikawiri.

8) Kusaganizira ndi kukhudzidwa ndi momwe ena amvera mumtima.

9) Kumangoyamba zinthu koma osatha kutsiriza.

H. Zolinga ndi zitsanzo zowoneka bwino.

Page 69: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

69

I. Moyo wotha kudziletsa ndi wa umunthu musanakwatire.

1) Banja lomwe silinathe kukhala ndi moyo wodziletsa asanalowe m’banja, amalephera kuti akhale okhulupirirana ndipo chimakhala chobvuta kuti akhulupirirane pamene alowa m’banja.

2) Kutsutsika chifukwa cha moyo wa m’mbuyomo wakhalidwe la nkhuli yachiwerewere ku

mapherezera pa moyo wina wokonda kutsutsana ndi kudzudzulana mtsogolo pamene mabvuto ena apezeka m’banja, ndipo zimayambitsa mabvuto m’maganizo.

3) Manyazi amadetsa chikondi cha pa wina ndi mnzakeyo ndinso chimwemwe cha ubale

wawowo. 9. Sankhani Munthu Yemwe Mukuona kuti Mutha Kuthandizana Naye M'zambiri Popanda Bvuto

Ndiponso Wofanirako M’zambiri. Banja Lidzakhala Losangalala Ngati ndi la Mphamvu Ngati Pali Zambiri Zofanana Pakati pa Awiriwa. Taonani Zina za Zoyenera Kuziona kuti Zikhale Zofanana Nanu:

A. Mtundu ndi chikhalidwe (Dziwani kuti malembo satikakamiza kuti tikwatire anthu amitundu

umodzi ndi ife okha ayi, koma kuti ichi chimabvutitsa ana obadwawo m’maganizo).

B. Nkhani ya chuma. C. Malingaliro pa za mwamuna kapena mkazi (pokomana m’thupi).

1) Maganizo pa zakulera ndi kuchotsa pakati.

2) Wokonda kulandira kapena kupereka.

3) Ndi zochita ziti zomwe ziri zongosangalatsa umoyo kapena

zobvomerezeka.

D. Maganizo pa zachuma.

1) Ndani adzayendetsa chuma?

2) Kodi mkazi akhale wa pa ntchito? Kwa nthawi yotalika bwanji?

3) Kodi tilandire thandizo kwa makolo? Lochuruka bwanji?

4) Zosunga.

5) Zopereka zathu kumpingo.

6) Zogula pa ngongole.

7) Kusagwirizana ndi kusintha pakagwiritsidwe ntchito ka ndalama mwadzidzidzi.

E. Maganizo pa ana.

1) Kukhala kapena kusakhala ndi ana?

2) Nanga akhale angati?

3) Tidzayambe liti; nanga atalikane bwanji?

4) Kodi tidzidzamwa mankhwala olera? Nanga njira yobvomerezeka idzakhale iti?

5) Kodi amayi ndiwo adzasamale anawo, kapena kupeza wolera?

Page 70: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

70

6) Kodi anawo aleredwe motani? Munjira zotani?

7) Kuwaphunzitsa uphungu wabwino.

8) Mapemphero apabanja? Maphunziro a chipembedzo?

9) Njira ndi kuonetsetsa kuti anawo akusunga mwambo, kolangidwe.

F. Zikhulupiriro za chipembedzo.

1) Kukasonkhana kuti; kodi tikasonkhane?

2) Zopereka.

3) Nthawi yotenga gawo m'zochitikachitika za mpingo.

4) Ana aphunzitsidwe chiyani? Kodi tiana tibatizidwe?

G. Maonekedwe ndi khalidwe la munthu (ulipo mulingo wake wothandiza kuzindikira ngati ziripo zina zoti mutha kumvana naye mnzanuyo m’zambiri).

H. Maudindo a akazi ndi amuna.

I. Zodzikonda ndi zosadzikonda.

J. Kulumikizana ndi kuyankhulana.

K. Dongosolo la ntchito yodzagwira mtsogolo.

L. Maubale a pa ukwati.

1) Kodi kumvera kwakukulu kudzakhala kwa mkazi, mwamuna wako kapena makolo?

2) Kodi mudzamvana bwino ndi abale amkazi wanu / mwamuna wanu?

3) Kodi mudzakhala bwanji ndi makolo anu, pafupi kapena kutali?

4) Kodi mungadzathe kukhala motalikana nawo ngati nkofunikira?

5) Kodi makolo mudzakhala nawo kwa nthawi yotalika bwanji?

M. Njira zothetsera makangano.

N. Za ndale / zadziko / za boma

O. Anzanu.

P. Kukhuzidwa ndi zofunika za dziko kapena zosowa za anthu.

Q. Luntha ndi nzeru, machitidwe awo pa maphunziro.

R. Zosangalatsa zenizeni. 10. Nzeru Zina Zothandiza pa Chitomero ndi Chibwenzi:

A. Musasiye kulumikizana ndi kuchezerana ndi Akhristu anzanu chifukwa cha kukondana kwanu ndi mkazi / mwamuna wanu.

B. Osaletsa mnzanuyo kuchita zomkondweretsa. Mpatseni mwayi ndi ufulu woti akhale monga

munthu payekha wotha kumachita zina zomukondweretsa ndi kumusangalatsa pa moyo wake.

Page 71: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

71

Pa banja lowe liri langwiro ndi lotetezeka, mwayi umenewu ndithu ulipo.

C. Tumikirani Mulungu pamodzi. Ngati ubale wanu ndi munthu wina aliyense siulimbikitsa zomwe munali kuchita pa utumiki wa Mulungu koma ungolepheretsa, umenewu si ubale woyenera ayi.

D. Sibwino kupitiriza ubale ndi munthu yemwe simungathe kupemphera naye pamodzi ndi

kuphunzira pamodzinso.

E. Chenjerani musazolowere kukhudzana ndi mnzanuyo. Kumakhala kobvuta kuti mubwerere. Anthu osakwatira saloledwa kukhala omasuka pamaso pa Mulungu ndi kuchita mwa ufulu zinthu zoloza kukugonana ngakhale kugonana kumene. Sankhani malo omwe simukayeseka, komanso pitani m’magulu; samalani ndi nthawi pamodzi ngati nkotheka; ndipo kambiranani za bvutolo momasuka pamodzi. Lolani kulandira uphungu ngati nkoyenera. Nthawi zina “kupitirira” kaya kupita kutali kumaononga ubale wanu wabwino; pamakhala kusinthika pa momwe mumamvera poyamba chifukwa cha kutsutsika ndi manyazi.

F. Ngati muturukira kuti mnzanuyo alibe zoyeneretsa ndipo sali woyenera malingana ndi malembo,

ndi bwino kuthetsa ubale wanu nthawi yomweyo koposa kumangopitirira. Ichi ndicho chifukwa chake muyenera kukhala pa chitomero poyamba , kuti muthe kudziwa ngati inu muli woyenera kwa iye kapena iye kwa inu.

Mawu otsiriza: Palibe chomwe mumataya koma mumapeza zonse zofuna zanu ngati mutsatira nzeru zopambana za Mulungu wathu ndikupempha thandizo lake pamene nthawi yanu yofunafuna mnzanu wa banja yafika. Iye amafuna mutapeza mbambande. Iye adzakulemekezani ngati muika cholinga chake poyambirira mu nkhani imeneyi.

PHUNZIRO 15 - Kutsatira utsogoleri wa Mulungu

Mawu oyamba: Mkhristu weniweni amadzipereka ku kutumikira chifuniro cha Mulungu. Ichi ndi chomwe iye

amakhalira padziko. Ngati timamutchula Yesu kuti Ambuye, ndiye kuti tikubvomera kuti ali ndi udindo wolamulira

miyoyo yathu. Mu ganizo liri lonse, funso loyambirira limakhala loti “Kodi chokhoza ndi chiti? Kodi Mulungu

afuna ine ndichite chiti? Kodi ndi chiti chomwe chidzamusangalatse?" Kutulukira ndi kutsata chifuniro cha Mulungu kumatithandiza. Pamene tinali mumdima, otekedwa kumaso ndi onyengedwa ndi mdierekeze, timaganiza kuti zinthu za uchimo ndizo zinali zabwino kwa ife. Koma pamene tiri kuyandikira ku kuwala ndipo choonadi cha Khristu chitimasula ife timauka tidziwiradziwirabe kuti moyo ndi madalitso zimabwera pamene timvera Mulungu mwa chikhulupiriro. Tiri ndi udindo woona ndi kusiyanitsa chabwino ndi choipa ndi kusankhapo chabwinocho – Ahebri 5:14. Koma pamene tifika pa nthawi yoti tipange chisankho chofunikira kwambiri, pamakhala zotikoka zambiri ndinso zotikopa zambiri zomwe zimatikokera kumbali zosiyanasiyana – kudzikondweretsa tokha, zopindula zadziko, abwenzi athu, chikhalidwe chathu, kugonjera abale apabanja, chikumbumtima, chiphunzitso cha Mulungu ndi zina zotere. Pamakhala utsogoleri wina wachinyengo wooneka monga wochokera kwa Mulungu koma zisali chomwecho. Maganizo athu omwe auchimo atha kutinyenga ife eni – Yeremiya 17:9. Ndi kobvuta kukhala ndi cholinga pa chifuniro cha Mulungu ngati palinso zinthu zina zomwe tikuzifunitsitsa. Sitingathe kudzitsogolera tokha; timasowa thandizo la Mulungu - Yeremiya 10:23. Mulungu amadziwa kuti timabvutika kwambiri kuti tisiyanitse mawu ake ndi zokhumba zathu chabe kapena za chinyengo zomwe dziko lapansi limafuna. Iye walonjeza kuthandiza ndi kutsogolera munthu aliyense wokondadi chiyero ndipo ndi wokonzeka kuchita chifuniro chake. Nkotheka kudziwa chifuniro cha Mulungu ngati titsimikiza kutero. 1. Mulungu Walonjedza Kutsogolera iwo Qmwe Afuna Kumvera Iye Mokhulupirika – Miyambo 3:5,6;

Yesaya 42:16; Yakobo 1:5; Afilipi 3:15; Mateyu 5:6; Yohane 7:17; Yesaya 30:21.

2. Zinthu Zothandizira pa Utsogoleri wa Mulungu M’mitima Yathu:

A. Kudziwa malembo; kukhala ndi nthawi yophunzira malembo mwa mapemphero ndi kulingirira - Masalmo 1:2; 119:11.

Page 72: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

72

B. Kudzichepetsa ndi mtima womvera aulamuliro - Yakobo 4:6; Masalmo 25:9.

C. Kumvera kuunika komwe muli nako kale, kuyenda munjira yomwe muidziwa kale kuti muyenera kuyendamo - Yoswa 3:8, 13-17

D. Chikondi cha pachoonadi ndi chiyero - Mateyu 5:6; Yohane 7:17

E. Kutsimikizika pakufuna kumvera choonadi angakhale chikatimvetse zowawa ndi zosautsa -

Masalmo 15:4b; Danieli 1:8-20; 3:1-18; 6:1-10; Machitidwe 4:3,18-20; 5:28,29

F. Kudziwa mbusa - Yohane 10:1-5

G. Kukhala wofanana kwambiri ndi Khristu kuti tithe mwa chilengedwe chathu, kusankha njira yabwino - 2 Akorinto 3:17,18; Agalatiya 5:22,23

H. Kumvetsa zolinga zenizeni za Mulungu kuti tithe kuchita moyenera – Aefeso 1:11; 5:17. Zolinga

za Mulungu, malingana ndi mndandanda wolembedwa ndi Yvonne Simms ku bukhu lotchedwa “Discovering God’s will” kutulukira cholinga ndi chofuna cha Mulungu.

1) Kutipatsa ife Chiyanjano ndi iye – 2 Akorinto 5:19,20; 1 Yohane 1:3.

2) Kuti tiphunzire zambiri za iye ndi zaife – Yohane 17:3; Akolose 1:10; Afilipi 3:15b.

3) Kuti tikhale ofanana naye – 2 Akorinto 3:18; 2 Petro 1:4.

4) Kuitana ena kuti amdziwe Iye - Yohane 17:3

I. Kumvetsa mfundo zenizeni za cholinga cha Mulungu choululidwacho kuti tithe kugwiritsa ntchito

mfundo zimene:

1) Tiyenera kuchita zina zonse mwa kulemekeza Mulungu – 1 Akorinto 10:31.

2) Tiyenera kukonda Mulungu ndi mtima wathu wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. - Mateyu 22:37,38.

3) Funafunani ufumu wa Mulungu poyamba ndi chilungamo chake ndi kumkhulupirira Iye

pa zofuna zathu zonse pano padziko - Mateyu 6:33.

4) Kondani mnzanu monga mudzikondera inu eni (chitirani ena zomwe mukadakonda iwo atakuchitiraninso) - Mateyu 22:39,40; 7:12.

5) Musazunze anzanu m’maganizo kapena m’chirichonse - Aroma 13:8-10.

6) Pewani zonse zomwe zingapunthwitse inu eni kapena anzanu kapena kukufooketsani -

Mateyu 18:6-9

7) Konzani mwachangu ubale womwe waonongeka - Mateyu 5:23-24; 18:15-17; Aefeso 4:26

J. Pemphani nzeru ndi utsogoleri - Yakobo 1:5

K. Khulupirirani - Yakobo 1:6-8; Miyambo 3:5,6 3. Zinthu zomwe zimalepheretsa utsogoleri wa Mulungu:

A. Kudzipereka moperewera pakumvera kwathu – (mtima wogawanika pakati) - Yakobo 4:4,8; Numeri 22 mpaka 24: 31:7,8

B. Kukonda zonyansa; kusayera mtima - Masalmo 66:18; 2 Atesalonika 2:10-12; Aroma 1:21-28

C. Kupanda chikhulupiriro - Yakobo 1:5-8

Page 73: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

73

D. Kusadikira Mulungu; kulephera kuyembekezera uphungu wa Mulungu ndi cholinga chake -

Genesis 15:2-5; 16:1-4 4. Zomwe Malembo Anena pa Utsogoleri:

A. Onani njira zina zomwe Mulungu anatsogolera nazo atumiki ake mu Baibulo:

1) Kudzera m’malembo - Danieli 9:2; 2 1 Timoteo 3:16,17

2) Kudzera m’maloto - Genesis 41:1-7, 15-32; Mateyu 1:20; 2:13,22

3) Kudzera m’masomphenya - Machitidwe 16:9,10

4) Kudzera mu urim ndi tumimu - Eksodo 28:30; 1 Samueli 28:6

5) Kudzera mwa aneneri - Machitidwe 11:27-30

6) Kudzera mwa mawu ochokera kwa Mzimu Woyera - Machitidwe 8:29

7) Kudzera mwa Angelo - Machitidwe 8:26

8) Kudzera mwa zizindikiro - Oweruza 6:15-22, 36-40

9) Kudzera mwa zochitikachika – Oweruza 7:9-15

10) Kudzera mwa kuchita mayere - Machitidwe 1:23-26; Yona 1:7

11) Kudzera mwa mapemphero – Machitidwe 15:6-20

B. Tingasiyanitse bwanji ulosi woona ndi wabodza? (1 Yohane 4:1-3; 1 Atesalonika 5:21): Ulosi umakhala wonama ngati: 1) Mneneri akulimbikitsani inu kuti muchite zolakwika - Deuteronomo 13:1-3.

2) Zolosera zake za mneneriyo sizitsimikizika ndi kuoneka bwino - Deuteronomo 18:21,22.

3) Chipatso cha moyo wa mneneriyo pamodzi ndi miyoyo ya omtsatira ake iri yachabe -

Mateyu 7:15-20.

4) Mneneri anena kuti “Yesu atembereredwe” – 1 Akorinto 12:3.

5) Mneneriyo alalika uthenga wosiyana ndi womwe Khristu analalika pamodzi ndi atumwi ake. - Agalatiya 1:8,9.

6) Mneneriyo akana zina za choonadi chenicheni cha chikhulupiriro – 1 Yohane 4:2,3; 2

Yohane 7,9.

7) Ulosiwo utsutsana ndi chiphunzitso chenicheni cha malemba - Machitidwe 17:11.

8) Ngati ulosiwo utchinjiriza anthuwo kuchoonadi ndi kuwaphunzitsa za chinyengo – 2 Akorinto 3:17.

5. Njira Zina Zomwe Zingatithandize kuti Lilandire Bwino Utsogoleri wa Mulungu:

A. Malembo opatulika – 2 Timoteo 3:15-17; 2 Petro 1:20; Mateyu 4:4,7,10.

1) Malembo amauziridwa ndi Mzimu wa Mulungu; amenewa ndi mawu a Mulungu, choncho ndi wosiyana ndi mabuku ena onse. Mu malembo muli zonse za choonadi

Page 74: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

74

chomwe chimakhala chofunikira kutitsogolera ife popanga maganizo a zisankho zathu zoyenera.

2) Malembo ndi bvumbulutso lenileni la Mulungu, ndi choonadi chenicheni cha Mulungu

choperekedwa “kwa anthu onse.” Malangizo onse a munthu, ziphunzitso zonse za chipembedzo, maulosi onse owona, mautsogoleri onse owoneka owona ayenera kuyesedwa ndi muyezo wa malembo – Machitidwe 17:11; 2 Timoteo 3:16,17; Agalatiya 1:8,9; Yuda 3.

B. Maulamulo omwe Mulungu watiyikira – Aefeso 6:1-3; 5:22-24; Ahebri 13:17; Aroma 13:1-6; 1

Petro 2:13-17.

C. Chikumbumtima chathu – Aroma 14:23; 2:15; Yakobo 4:17; (chenjezo: chikumbumtima chanu chiyenera chikhale chounikiridwa ndi mawu a Mulungu kuti chikutsogolereni bwino – Miyambo 14:12).

D. Malangizo ochokera ku chiyanjano cha okhulupirira m’thupi la Khristu, makamaka anthu ake

omwe amadziwa ndi kukonda Mulungu pamodzi mawu ake – Miyambo 15:22.

1) Nthawi zambiri zimatithandiza kwambiri kukambirana ndi kupempherera pamodzi.

2) Ngati moyo wanu wazingidwa ndi nkhawa kaya maganizo okubvutani pansi pa mtima kufikira kusokoneza maganizo anu, ndi bwino nthawi zina kudalira ganizo lomveka bwino la mnzathu wina amene maganizo ake akuyenda bwino.

E. Chipatso cha Mzimu Woyera (chilengedwe, makhalidwe ndi mtima wa Yesu mwa ife) – Agalatiya

5:22,23; Afilipi 2:5-8.

F. Utsogoleri wachilengedwe kudzera mu zochitikachitika ndi zowonekawoneka monga:

1) Maitanidwe ndi miyayi

2) Kutsekuliridwa ndi kukanizidwa.

3) Mapezedwe a ndalama zofunikira ndinso kusowa

4) Zochitika panthawi imodzi kuonetsa kuti Mulungu ndiye akutsogolera.

G. Kukhutitsidwa, kumvetsetsa kukhulupiriradi mumtima.

1) Samalani: Zimatheka kusokonezeka pa maganizo anu anu ngakhale Satana pomaganiza kuti ndi ochitika motsogoleredwa ndi Mulungu. Onetsetsani kuti maganizo ali onse mwawayesa ndi malemba.

2) Maganizo a Satana angathe kusiyanitsidwa monga aSimusi alemba::

a. Malamulo a Mulungu ndi a poyera; a Satana ndi ozemba, obvuta kumvetsa..

b. Satana amakonda kutiyesa ndi zilakolako zathu za uchimo; Mulungu

amatidandaulira kuti tilakalake chiyero.

c. Satana ndi wopupuluma; Mulungu amadikira nthawi popeza ali nayo.

H. Zofunikira kukumbukiridwa; zoyenera kuganiziridwa kapena nzeru zogwiritsa ntchito zolowa m’maganizo pomwe tikumana ndi nyengo ndi anthu osiyanasiyana.. 1) Chenjezo: Koma zimenezinso muone kuti zigwirizane ndi malembo..

2) Kumvetsa kwanu kwa mumtima kutha kukhala kofunikira kwa inu nokha koma

musakakamize ena ayi..

Page 75: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

75

3) Pali anthu ena omwe sakhulupirira kuti Mulungu amatha kutsogolera mwa njira imeneyi, koma ife tibvomereza kuti izi ndi zoona, chifukwa cha mfundo yoti timathandiza mlaliki pa ulaliki wake mwa kumupempherera, kapena kupempha Mulungu kuti athandize pa zokambirana zathu zobvuta kapena pa mayeso ku sukulu kapena pa ntchito. Sitikutanthauza kuti munthunso ndi wouzirida kapena “kudzodzedwa” ngati atumwi koma kungoti Mulungu amathandiza anthu.

I. Kutsimikizira: - Machitidwe 9;11,12; Oweruza 6:36-40.

1) Mulungu sapereka zizindikiro kwa osakhulupirika - Marko 8:11,12.

2) Koma ali wachifundo kwa iwo odzipereka ndi omvera kuti alimbikitse chikhulupiriro

chawo powapatsa utsogoleri wake mwa kukwaniritsa ndi kutsimikizira.

3) Ngakhale mneneri Yeremiya wodzozedwayo nthawi zina nayenso ankafuna kutsimikiziridwa asanakhulupirire kuti chinthucho cha chokeradi kwa Mulungu - Yeremiya 32:6-8.

J. Kuponya maere pambuyo pa pemphero – Machitidwe 1:23-26; Yona 1:7; Miyambo 16:33.

1) Izi zichitide ngati mwina, chirichonse chayeseredwa ndipo yankho lofunika

silikupezedwa. Chitani chimenechi monga chinthu chotsiriza chenicheni.

2) Taonani kuti atumwi aja anayesera njira zina zambiri yoyesera zinthu asanaponye mayere.

3) Musagwiritse ntchito njira imeneyi monga njira yachidule pofuna kuthawa maphunzro a

Baibulo, pemphero, kukambirana, kulingirira ndi kukula mu uzimu.

4) Ngati mwa pemphero munthu agwiritsa ntchito njira imeneyi ayenera akhale okonzeka kutsatira ndi chikhulupiriro chonse kuti Mulungu ndiye watsogolera.

5) Sitikusonyezedwa m'njira iriyonse kuti Mulungu adzalemekeza njira yomwe siinagwiritse

ntchito njira zina zokhulupirika. Mufuniranji utsogoleri wa Mulungu ngati simufunsa mphamvu ndi nzeru zake? (Simms).

6. Nanga Mumatani Ngati Mukulepherabe Kupeza Yankho?

A. Nthawi zina Mulungu amatileka kuti tilowe m’nthawi za “mdima” ndi mayesero ndi cholinga chofuna kuti tikhwime mu chikhulupiriro chathu ndi khalidwe ndikuti chilakolako chathu cha pa iye chichulukire ndi kukulira – Yakobo 1:2,3,12; Aroma 5:3-5; Yobu.

B. Nthawi zimenezi zikafika tengeranipo mwayi wophunzira kutonthoza mtima wanu ndi

kuyembekezera mwa chikhulupiriro pa Mulungu.

C. Yambani kutsatira njira zakumvera zomwe munayenera kutsata koma simunayambe kuzitsata.

D. Yesetsani kufufuza ndi kutulukira komanso kuthana ndi njira zonse za kusamvera zomwe zimakulepheretsani kuti Mulungu akutsogolereni (koma nthawi zina kukhala mumdima kopitirira sikungadalire zimenezi).

E. Mulungu mwina atha kumakuonetsani kuti amayembekezera kuti inu mugwiritse ntchito nzeru za

inu nokha.

F. Ngati mwafika pa ndime yomwe mwafunitsitsa kupanga ganizo ndipo ndi koyeneradi kutero, komanso mwayesera njira zina zonse kuti muone cholinga cha Mulungu, mutha:

1) Kuganizira pa zochepa zomwe mukudziwa, angakhale zioneka zazing’ono, ndipo

mupereke zotsatira zake kwa Mulungu (Iye walonjeza kutsogolera ndi kusunga ana ake) kapena

Page 76: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

76

2) Ngati mwayesera njira zina zonse, pempherani ndipo muponye maere kapena china

chiri chonse chofanana ndi chimenechi. Mukhale okonzeka kubvomera zotsatira zake ndi kumazitsatira zedi.

3) Dalirani maganizo a wina yemwe mumamudalira ndi kumkhulupirira chifukwa cha

chiweruzo chake ndi chikhulupiriro chake. (Koma khalani osamala kuti pamene iye akuthandizani, ndipo patapita nthawi mugwa m'mabvuto, musadzamuwawire mtima ndi kumusungira mkwiyo.)

7. Mfundo Zosiyanasiyana Zokhudza Kutsogoleredwa.

A. Uphungu uli wonse, nzeru ziri zonse kapena utsogoleri ndi kuunikira kwa mtundu uliwonsewo kuyenera kudziyesedwa ndi malembo – 1 Atesalonika 5:21; 2 Timoteo 3:16-17. Palibe kuunikira koona kochokera kwa Mulungu komwenso kungatsutsane ndi mawu ake am’Baibulo.

B. Mulungu anatipatsa ife nzeru zathu, kudziwa, kuphunzira powonera ndi mphamvu yosankha kuti

tithe kusankha njira yathu. Iye watipatsanso mfundo zonse zofunika kudzera mu Baibulo. Ife ndife akazembe a Mulungu omasuka, opangidwa m’chifanizo cha Mulungu, otha kupanga tokha chisankho chathu. Ngati Mulungu akadakhala kuti angotilamula monga makina m’malo motilola kuti tichite zina mwanzeru zathu, ndiye kuti akanalakwira umunthu wathu ndi kutitenga monga makina. Komanso akanatilanda mphamvu za kukula zomwe zimabwera pamene munthu afufuza, aphunzira ndi kupanga zisankho zake yekha. Pounikiridwa ndi mawu a Mulungu, kukhala ndi khalidwe lofanana ndi la Yesu lopezeka mwa ife kudzera mwa Mzimu Woyera, timayenera kupanga chisankho tokha. Kufufuza chizindikiro kutha kukhala monga njira yotsimikizira poopa ndi kupewa kuchita kapena kutenga udindo monga momwe Mulungu anafunira pamene anatilenga ife.

C. Kufunafuna kutsogoleredwa “pogwetsa Baibulo kuti ligwe litatseguka” kapena kuika chala pa

vesi iriyonse mosayang’anira zimangokhala ngati zikhulupiriro za chikunja ndipo zimachepetsa mphamvu ya Baibulo monga chinthu chongopangidwa ndi munthu m’malo mwa chinthu chopangidwa monga uthenga weniweni wochokera kwa Mulungu. Iyinso ndi njira yogwiritsidwa ntchito ndi anthu aulesi amene salola kupemphera, kuphunzira, ndi kukambirana.

D. Tikuletsedwa molimbika kutemebenukira kwa owombeza kuti atiunikire - Yesaya 8:19,20;

Deuteronomo 18:10,11.

E. Zinthu zomwe sizinatchulidwe mwachindunji m’Baibulo zafotokozeredwa ndi mfundo za umunthu ndi zauzimu zophunzitsidwa m’malembo.

F. Kutsatira utsogoleri wa Mulungu ndi chinthu chomwe chimanka chikulirakulira.. G. Pamene mwadala musankha kuchita chinthu china chomwe sichiri cholingana ndi chifuniro cha

Mulungu, mtendere wanu umatayika pomwepo.

H. Anthu ena amaopa kuti mwina anganyengedwe moopsa ndi utsogoleri wachinyengo wochokera kwa Satana. 2 Akorinto 11:14,15. Komabe Mulungu watilonjeza kuti Satana sangathe kunyenga munthu wokonda choonadi mokhulupirika ndi zolimbitsa zake kwa nthawi yaitali – 1 Akorinto 10:13; Yohane 7:17; Mateyu 7:15; tawerengani Eksodo 7:1-8:19 ndipo mufanizire.

Mawu otsiriza: Mulungu amakonda ana ake koposa kholo lina liri lonse la padziko lapansi. Iye ali ndi chidwi chopusa kholo lina liri lonse la kuthupi kuti tiyende m’njira yoyenera. Iye watimasula ife (kuti tikhale wofanana naye), koma amatithandiza kuti tichite bwino. Pemphero la Mkhristu aliyense likhale:

"Ndi phunzitseni kuchita chifuniro chanu, chifukwa ndinu Mulungu wanga; ndi pempha Mzimu wanu wabwino unditsogolere kukhala pomwe ndiyenerapo." (Masalmo 143:10).

Awa ndiwo mathero a njira yomwe ife Akhristu timayendamo pakukula kwathu. Ndi pemphero la mlembi wa phunziroli kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito zinthu zimenezi

Page 77: Kukula m’Moyo mwa Chikhristu - Namikango Bible Schoolnamikangobibleschool.org/uploads/PDFS/KUKULA MCHIKHRISTU.pdfChristian Growth – 11/28/12 1 Kukula m’Moyo mwa Chikhristu Phunziro

Christian Growth –

11/28/12

77

kuti alemekezeke ndikuti athandize anthu. Monga momwe zinthu izi zakhalira monga mwa choonadi cha Mulungu, tipempha kuti Mulungu azisunge ndi kuzigwiritsa ntchito mwa iwo omwe aziphunzira; Ngati pali zina zomwe sizinachokere kwa Mulunguyo, tipempha Ambuye “azisefe monga mankhusu kapena madeya.”

By G.B. Shelburne, III (except for any graphics and scripture quotations). May be reproduced for non-profit, non-publishing instructional purposes provided

this entire copyright notice is included and lesson content is not altered. South Houston Bible Institute, PO Box 891246, Houston, TX 77289-1246, tel. 281-990-8899, Email [email protected], web site <www.shbi.org>. Malemba ena achokera ku Bukhu Lopatulika lopangidwa ndi Bible Society of Malawi, P.O. Box

740, Blantyre, Malawi, copyright 1998. Phunziroli linamasulidwa m’Chichewa ku Namikango Mission, June 2003.